Deuteronomo 10:1-22
10 “Pa nthawi imeneyo Yehova anandiuza kuti, ‘Dzisemere miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo udzipangire likasa lamatabwa.+ Ukatero ukwere m’phiri muno kwa ine.
2 Pamiyalayo ndidzalembapo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija, imene unaswa, ndipo udzaiike m’likasalo.’
3 Choncho ndinapanga likasa la mtengo wa mthethe ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija.+ Kenako ndinakwera m’phiri, miyala iwiriyo ili m’manja mwanga.
4 Pamenepo analemba pamiyalayo mawu ofanana ndi oyamba aja,+ Mawu Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani m’phiri kuchokera pakati pa moto,+ tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo.
5 Ndiyeno ndinatembenuka, n’kutsika m’phirimo,+ ndipo ndinaika miyala iwiriyo m’likasa limene ndinapanga kuti izikhala mmenemo, monga mmene Yehova anandilamulira.+
6 “Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka kuchoka ku Beeroti Bene-yaakana+ kupita ku Mosera. Aroni anafera kumalo amenewo, ndipo anamuikanso kumeneko.+ Mwana wake Eleazara anayamba kutumikira monga wansembe m’malo mwa Aroniyo.+
7 Ndiyeno ananyamuka pamalo amenewo kupita ku Gudigoda. Anachokanso ku Gudigoda kupita ku Yotibata,+ dziko la zigwa* zokhala ndi madzi ndithu.
8 “Pa nthawi imeneyo, Yehova anapatula fuko la Levi+ kuti lizinyamula likasa la pangano la Yehova,+ liziima pamaso pa Yehova pom’tumikira,+ ndi kuti lizidalitsa m’dzina lake kufikira lero.+
9 N’chifukwa chake Levi alibe gawo ndiponso cholowa+ monga abale ake. Yehova ndiye cholowa chake, monga mmene Yehova Mulungu wanu anamuuzira.+
10 Ndipo ine ndinakhala m’phirimo masiku ofanana ndi oyamba aja, masiku 40, usana ndi usiku,+ ndipo Yehova anandimveranso pa nthawi imeneyi.+ Yehova sanafune kukuwonongani.+
11 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsogolera anthu kuti ayambe ulendo, kuti akalowe ndi kutenga dziko limene ndinalumbirira makolo awo kuti ndidzawapatsa.’+
12 “Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani,+ koposa kuopa+ Yehova Mulungu wanu kuti muziyenda m’njira zake zonse,+ kukonda+ ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+
13 kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi mfundo zake+ zimene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino?+
14 Taonani, kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu wanu,+ kumwambamwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi+ ndi zonse zili mmenemo ndi zake zonsezo.
15 Koma Yehova anadziphatika kwa makolo anu ndi kuwakonda, moti anasankha ana awo obadwa m’mbuyo mwawo,+ inuyo, pakati pa anthu onse monga mmene zilili lero.
16 Mitima yanu muichite mdulidwe+ ndipo musakhalenso ouma khosi.+
17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye.+ Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa,+ amene sakondera+ munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.+
18 Iye amaperekera chiweruzo ana amasiye* ndi akazi amasiye,+ ndipo amakonda mlendo wokhala pakati panu+ moti amam’patsa mkate ndi chofunda.
19 Inunso muzikonda mlendo wokhala pakati panu,+ chifukwa munali alendo m’dziko la Iguputo.+
20 “Muziopa Yehova Mulungu wanu.+ Muzim’tumikira,+ kum’mamatira+ ndi kulumbira pa dzina lake.+
21 Iye ndi amene muyenera kum’tamanda,+ ndipo iye ndi Mulungu wanu amene wakuchitirani zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha, zimene mwaziona ndi maso anu.+
22 Makolo anu anapita ku Iguputo ndi anthu 70,+ ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakuthambo.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”