Deuteronomo 18:1-22
18 “Ansembe achilevi, kapena kuti fuko lonse la Levi,+ asakhale ndi gawo kapena cholowa pakati pa Isiraeli. Iwo azidya nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Azidya cholowa chake.+
2 Choncho asalandire cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo,+ monga mmene anawauzira.
3 “Ndipo izi ndi zinthu zimene ansembe ayenera kulandira kuchokera kwa anthu. Amene akupereka nsembe ya ng’ombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe mwendo wakutsogolo, nsagwada ndi chifu.
4 Uziperekanso gawo loyamba la mbewu zako, vinyo wako watsopano, mafuta ndi ubweya wa nkhosa wometedwa moyambirira.+
5 Pakuti iye ndi amene Yehova Mulungu wako wam’sankha pakati pa mafuko anu onse, kuti iye pamodzi ndi ana ake aimirire ndi kutumikira m’dzina la Yehova nthawi zonse.+
6 “Ngati Mlevi watuluka mu umodzi mwa mizinda yonse ya Isiraeli, umene iye anakhalamo kwa kanthawi,+ ndiyeno wabwera pamalo amene Yehova adzasankhe, chifukwa chakuti mtima wake walakalaka kukatumikira pamalopo,+
7 azitumikiranso m’dzina la Yehova Mulungu wake mofanana ndi abale ake onse Alevi, amene aimirira kumeneko pamaso pa Yehova.+
8 Ngakhale kuti wapeza chuma atagulitsa katundu wa makolo ake, gawo la chakudya chake lizikhala lofanana ndi ansembe onse.+
9 “Ukakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usakaphunzire kuchita zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu imeneyo akuchita.+
10 Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ wochita zamatsenga,+ woombeza,*+ wanyanga,+
11 kapena wolodza* ena,+ aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu,+ wolosera zam’tsogolo+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+
12 Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wako akuwapitikitsa pamaso pako.+
13 Ukhale wopanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wako.+
14 “Mitundu imene ukuilanda dziko inali kumvera anthu ochita zamatsenga+ ndi olosera.+ Koma iwe, Yehova Mulungu wako sanakulole kuchita zimenezi.+
15 Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati panu, kuchokera pakati pa abale anu, ndipo inu mudzamvere mneneri ameneyo.+
16 Adzakupatsani mneneri poyankha zonse zimene munapempha Yehova Mulungu wanu ku Horebe, tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Munapempha kuti, ‘Tiloleni tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuopera kuti tingafe.’+
17 Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Mawu onse amene iwo anena ali bwino.+
18 Ndidzawapatsa mneneri ngati iwe kuchokera pakati pa abale awo.+ Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwake,+ ndipo adzawauza zonse zimene ndidzamulamula.+
19 Pamenepo munthu amene sadzamvera mawu anga amene iye adzalankhule m’dzina langa, adzayankha mlandu kwa ine.+
20 “‘Koma mneneri amene adzadzikuza mwa kulankhula m’dzina langa mawu amene sindinamulamule kuti alankhule,+ kapena kulankhula m’dzina la milungu ina,+ mneneri ameneyo afe ndithu.+
21 Mumtima mwako ukanena kuti: “Tidzadziwa bwanji kuti si Yehova amene walankhula mawuwo?”+
22 Mneneri akalankhula m’dzina la Yehova, koma mawuwo sanachitike kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti si Yehova amene walankhula mawu amenewo.+ Mneneriyo walankhula mawu amenewo mwa iye yekha, modzikuza. Iwe usachite naye mantha.’+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “kudutsitsa pamoto.”
^ Mawu akuti ‘kulodza’ kapena ‘kuchisa’ amatanthauza kupweteka kapena kulepheretsa munthu kuchita chinachake mwa njira ya matsenga.