Deuteronomo 2:1-37
2 “Ndiyeno tinatembenuka ndi kulowera kuchipululu kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira, monga mmene Yehova anandiuzira.+ Ndipo tinayenda masiku ambiri m’dera lapafupi ndi phiri la Seiri.
2 Kenako Yehova anandiuza kuti,
3 ‘Mwayenda kwa nthawi yaitali m’dera lapafupi ndi phirili.+ Tembenukani ndi kulowera kumpoto.
4 Auze anthuwo kuti: “Mukudutsa m’malire a dziko la abale anu,+ ana a Esau,+ amene akukhala m’Seiri.+ Iwo adzachita nanu mantha,+ choncho muyenera kukhala osamala kwambiri.
5 Musalimbane nawo, chifukwa sindikupatsani dziko lawo, ngakhale kachigawo kokwana phazi limodzi lokha. Ndinapereka phiri la Seiri kwa Esau kuti likhale malo ake.+
6 Mudzadya chakudya chimene mudzagula kwa iwo ndi ndalama, ndipo mudzamwa madzi amene mudzagula kwa iwo ndi ndalama.+
7 Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse chimene dzanja lanu likuchita.+ Iye akudziwa za kuyenda kwanu kudutsa m’chipululu chachikulu ichi. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi,+ ndipo simunasowe kanthu.”’+
8 Chotero tinalambalala abale athu, ana a Esau,+ amene akukhala m’Seiri, ndipo sitinayende njira ya Araba,+ Elati ndi Ezioni-geberi.+
“Kenako tinatembenuka ndi kudutsa njira ya m’chipululu cha Mowabu.+
9 Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Usavutitse Amowabu kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko lawo kuti likhale lako. Ndinapereka Ari+ kwa ana a Loti kuti akhale malo awo.+
10 (Kale munali kukhala Aemi,+ anthu amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Iwo anali ataliatali ngati Aanaki.+
11 Arefai+ anali kuonedwanso ngati Aanaki,+ ndipo Amowabu anali kutcha Arefaiwo kuti Aemi.
12 Kale Ahori+ anali kukhala m’Seiri, ndipo ana a Esau+ anawalanda dzikolo ndi kuwapha. Atatero, ana a Esauwo anayamba kukhala m’dzikolo,+ monga mmene ana a Isiraeli ayenera kuchitira m’dziko lawo, limene Yehova adzawapatsa ndithu.)
13 Choncho nyamukani ndi kudutsa chigwa* cha Zeredi.’ Pamenepo tinadutsadi chigwa cha Zeredi.+
14 Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-barinea mpaka kuwoloka chigwa cha Zeredi anali zaka 38, kufikira m’badwo wa amuna otha kupita kunkhondo utatha pakati panu, monga mmene Yehova analumbirira kwa iwo.+
15 Dzanja+ la Yehova linali pa iwo kuwasautsa ndi kuwachotsa pakati panu, kufikira onse atatha.+
16 “Ndiyeno amuna onse otha kupita kunkhondo atatha kufa pakati pa anthu,+
17 Yehova analankhulanso ndi ine, kuti,
18 ‘Lero udutsa m’dera la Mowabu, pafupi ndi Ari,+
19 ndipo uyandikire pafupi ndi ana a Amoni. Usawavutitse kapena kumenyana nawo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko la ana a Amoni kuti likhale lako. Dziko limeneli ndinalipereka kwa ana a Loti kuti likhale lawo.+
20 Dzikoli linali kudziwika kuti ndi la Arefai.+ (Kale munali kukhala Arefai ndipo Aamoni anali kutcha Arefaiwo kuti Azamuzumi.
21 Anthu amenewa anali amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Analinso ataliatali ngati Aanaki.+ Yehova anawafafaniza+ kuwachotsa pamaso pa ana a Amoni kuti ana a Amoniwo atenge dzikolo ndi kukhalamo,
22 monga mmene anachitira ndi ana a Esau amene akukhala m’Seiri.+ Iye anafafaniza Ahori+ kuwachotsa pamaso pa ana a Esau, kuti ana a Esauwo atenge dzikolo ndi kukhalamo mpaka lero.
23 Aavi+ amene anali kukhala m’midzi mpaka kukafika ku Gaza,+ anawonongedwa ndi Akafitori+ ochokera ku Kafitori,+ kuwachotsa pamaso pawo kuti Akafitoriwo akhale m’dzikolo.)
24 “‘Nyamukani, muyende ndi kudutsa chigwa cha Arinoni.+ Taonani, ndapereka m’manja mwanu Sihoni,+ Mwamori, mfumu ya Hesiboni. Yambani kulanda dziko lake, ndipo menyanani naye nkhondo.
25 Lero ndichititsa anthu a mitundu ina okhala pansi pa thambo, amene adzamva za inu, kuchita nanu mantha kwambiri ndi kuyamba kukuopani. Chifukwa cha inu, iwo adzanthunthumira ndi kumva zopweteka zofanana ndi zowawa za pobereka.’+
26 “Kenako, ndinatumiza amithenga a mawu amtendere+ kuchokera m’chipululu cha Kademoti,+ kupita kwa Sihoni+ mfumu ya Hesiboni, kuti,
27 ‘Ndilole ndidutse m’dziko lako. Ndidzangodutsa mumsewu. Sindidzatembenukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+
28 Ndidzadya chakudya chimene udzandigulitsa ndi ndalama, ndipo ndidzamwa madzi amene udzandigulitsa ndi ndalama. Ndilole ndingodutsa m’dziko lako,+
29 monga mmene ana a Esau amene akukhala m’Seiri+ ndi Amowabu+ amene akukhala mu Ari anachitira kwa ine. Ndidzadutsa m’dziko lako mpaka kukawoloka Yorodano, kulowa m’dziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa.’+
30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+
31 “Zitatero, Yehova anandiuza kuti, ‘Taona, ndikupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Yamba kulanda dziko lake.’+
32 Sihoni atatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nafe nkhondo ku Yahazi,+
33 Yehova Mulungu wathu anam’pereka kwa ife,+ ndipo tinam’gonjetsa+ limodzi ndi ana ake ndi anthu ake onse.
34 Tinalandanso mizinda yake yonse pa nthawi imeneyo ndi kuwononga mzinda wina uliwonse.+ Tinapha amuna, akazi ndi ana, ndipo sitinasiye munthu aliyense wamoyo.
35 Ziweto zokha n’zimene tinatenga monga zofunkha pamodzi ndi zofunkha za m’mizinda imene tinalanda.+
36 Kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli m’mbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso kuchokera kumzinda wa m’chigwa mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda womwe unali wa malinga aatali kwambiri kwa ife.+ Yehova Mulungu wathu anawapereka onsewo kwa ife.
37 Koma simunayandikire dziko la ana a Amoni,+ dera lonse la m’mbali mwa chigwa cha Yaboki,+ kapena mizinda ya m’dera lamapiri, kapenanso malo alionse amene Yehova Mulungu wathu sanatilamule kuti tiwalande.