Deuteronomo 27:1-26
27 Mose pamodzi ndi akulu a Isiraeli anapitiriza kuuza anthuwo kuti: “Muzisunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero.+
2 Mukawoloka Yorodano+ ndi kulowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muimike miyala ikuluikulu ndi kuipaka utoto woyera.
3 Ndiyeno mukawoloka,+ mulembe pamiyalapo mawu onse a chilamulochi+ kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, malinga ndi zimene Yehova Mulungu wa makolo anu wakuuzani.+
4 Choncho mukawoloka Yorodano, muimike miyala imeneyi paphiri la Ebala,+ monga mmene ndakulamulirani lero, ndipo muipake utoto woyera.+
5 Mumangirenso Yehova Mulungu wanu guwa lansembe kumeneko, guwa lansembe lamiyala. Musaseme miyalayo ndi chipangizo chilichonse chachitsulo.+
6 Muzigwiritsa ntchito miyala yathunthu pomangira Yehova Mulungu wanu guwa lansembe, ndipo muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu paguwalo.+
7 Muzipereka nsembe zachiyanjano+ ndi kuzidyera pamenepo,+ ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+
8 Mulembe mawu onse a chilamulochi pamiyalayo,+ muwalembe moonekera bwino.”+
9 Kenako Mose ndi ansembe achilevi analankhula ndi Aisiraeli onse kuti: “Aisiraeli inu, khalani chete ndi kumvetsera. Lero mwakhala anthu a Yehova Mulungu wanu.+
10 Choncho muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo+ ndi malangizo ake,+ amene ndikukupatsani lero.”
11 Tsiku limenelo Mose anapitiriza kulankhula ndi anthuwo kuti:
12 “Amene adzaimirira ndi kudalitsa anthu paphiri la Gerizimu+ mukawoloka Yorodano ndi awa: Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini.
13 Amene adzaimirira kuti avomere pamene matemberero+ akutchulidwa paphiri la Ebala+ ndi awa: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafitali.
14 Pamenepo Alevi azinena mawu awa mokweza kuuza mwamuna aliyense wa Isiraeli+ kuti:
15 “‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndi kuchibisa. Chifanizirocho ndi chinthu chonyansa kwa Yehova,+ Mulungu wopanga manja a mmisiri wa matabwa ndi zitsulo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)*+
16 “‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
17 “‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
18 “‘Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa wakhungu.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
19 “‘Wotembereredwa ndi munthu wopotoza+ chiweruzo+ cha mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
20 “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mkazi wa bambo ake, chifukwa wavula bambo akewo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
21 “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona nyama iliyonse.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
22 “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
23 “‘Wotembereredwa ndi mwamuna wogona ndi apongozi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
24 “‘Wotembereredwa ndi munthu wobisalira mnzake ndi kumupha.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
25 “‘Wotembereredwa ndi munthu wolandira chiphuphu kuti akanthe ndi kupheratu munthu, kuti akhetse magazi a munthu wosachimwa.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
26 “‘Wotembereredwa ndi munthu amene sadzatsatira mawu a m’chilamulo ichi ndipo sadzawagwiritsa ntchito.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”