Deuteronomo 29:1-29

29  Awa ndi mawu a pangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi ana a Isiraeli m’dziko la Mowabu, kuwonjezera pa pangano limene anachita nawo ku Horebe.+  Choncho Mose anaitana Aisiraeli onse ndi kuwauza kuti: “Inuyo ndinu amene munaona ndi maso m’dziko la Iguputo zonse zimene Yehova anachitira Farao, atumiki ake onse ndi dziko lake lonse.+  Inuyo munaona mayesero,+ zizindikiro zazikulu+ zija ndi zozizwitsa.+  Koma Yehova sanakupatseni mtima woti muthe kuzindikira, maso oti muthe kuona ndi makutu oti muthe kumva, kufikira lero.+  ‘Pamene ndinali kukutsogolerani kwa zaka 40 m’chipululu,+ zovala zanu sizinathe ndiponso nsapato zanu sizinathe kumapazi anu.+  Simunadye mkate,+ simunamwe vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’  Ndiyeno munafika pamalo ano, ndipo Sihoni mfumu ya Hesiboni+ ndi Ogi+ mfumu ya Basana anatuluka kudzamenyana nafe nkhondo, koma tinawagonjetsa.+  Kenako tinatenga dziko lawo ndi kulipereka monga cholowa kwa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase.+  Choncho muzisunga mawu a pangano ili kuti zonse zimene muzichita zizikuyenderani bwino.+ 10  “Nonsenu mwaima pano lero pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu atsogoleri a mafuko, akulu anu, atsogoleri anu, mwamuna aliyense wa mu Isiraeli,+ 11  ana anu, akazi anu,+ alendo+ okhala mkati mwa msasa wanu, kuyambira wokutolerani nkhuni mpaka wokutungirani madzi,+ 12  kuti muchite pangano+ ndi Yehova Mulungu wanu mwa kulumbira, pangano limene Yehova Mulungu wanu akuchita nanu lero.+ 13  Cholinga chake n’chakuti akukhazikitseni lero monga anthu ake+ ndi kuti akuonetseni kuti ndi Mulungu wanu,+ monga mmene anakulonjezerani ndiponso monga mmene analumbirira makolo anu, Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+ 14  “Tsopano sindikuchita pangano ili mwa lumbiro ndi inu nokha ayi,+ 15  koma ndikuchita pangano ili ndi anthu amene aimirira ndi ife pano lero pamaso pa Yehova Mulungu wanu, komanso ndi awo amene sitili nawo pano lero.+ 16  (Pakuti inu mukudziwa bwino mmene tinali kukhalira m’dziko la Iguputo ndi mmene tinadutsira pakati pa anthu a mitundu ina. Podutsa pakati pa mitundu imeneyo,+ 17  munaona zinthu zawo zonyansa ndi mafano awo onyansa,*+ mafano amtengo ndi amwala, asiliva ndi agolide amene anali nawo.) 18  Cholinga cha pangano limeneli n’chakuti, pakati panu pasapezeke mwamuna, mkazi, banja kapena fuko limene mtima wake ukupatuka kusiyana ndi Yehova Mulungu wathu, ndi kupita kukatumikira milungu ya mitundu inayo,+ kuti pakati panu pasapezeke muzu wotulutsa chomera chakupha ndi chitsamba chowawa.+ 19  “Ndiyeno zikachitika kuti wina amene wamva mawu a lumbiro+ ili, walankhula modzitama mumtima mwake kuti, ‘Ndidzakhala ndi mtendere+ ngakhale kuti ndidzayenda motsatira zofuna za mtima wanga,’+ koma ali ndi cholinga chowononga wina aliyense, mofanana ndi kukokolola mtengo wothiriridwa bwino ndi wosathiriridwa womwe, 20  Yehova sadzafuna kukhululukira+ munthu woteroyo, m’malomwake mkwiyo+ ndi ukali+ wa Yehova udzamuyakira,+ ndipo matemberero onse olembedwa m’buku+ ili adzakhala pa iye, motero Yehova adzafafanizadi dzina la munthuyo pansi pa thambo. 21  Choncho Yehova adzam’patula+ pa mafuko onse a Isiraeli kuti amudzetsere tsoka, mogwirizana ndi matemberero onse a pangano lolembedwa m’buku ili la chilamulo. 22  “Pamenepo m’badwo wa m’tsogolo, ana anu amene adzabwera pambuyo panu, ndiponso mlendo amene adzachokera kudziko lakutali, akadzaona miliri ndi nthenda zimene Yehova wakantha nazo dzikolo,+ adzanena mawu. 23  Adzanena mawuwo akadzaonanso sulufule, mchere+ ndi kutentha,+ moti m’dzikomo simungabzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, mofanana ndi Sodomu ndi Gomora,+ Adima+ ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga mu ukali ndi mkwiyo wake.+ 24  Mitundu yonse idzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mkwiyo wake wayaka kwambiri chonchi?’ 25  Pamenepo anthu adzanena kuti, ‘N’chifukwa chakuti anataya pangano+ la Yehova Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene anali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo.+ 26  Ndipo anapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, milungu imene sanaidziwe, imenenso sanaloledwe kuti aziilambira.+ 27  Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira dziko limeneli mwa kulibweretsera matemberero onse olembedwa m’buku ili.+ 28  Choncho Yehova anawazula m’dziko lawo atapsa mtima,+ ali ndi ukali ndiponso mkwiyo waukulu n’kuwataya m’dziko lina monga mmene zilili lero.’+ 29  “Zinthu zobisika+ ndi za Yehova Mulungu wathu, koma zinthu zoululidwa+ ndi zathu ndi ana athu mpaka kalekale, kuti titsatire mawu onse a chilamulo ichi.+

Mawu a M'munsi

Mawu amene ali m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”