Deuteronomo 8:1-20

8  “Muonetsetse kuti mukusunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero,+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ ndi kuti muchulukanedi, n’kupita kukatenga dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.+  Muzikumbukira njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani m’chipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa,+ kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mukanasunga malamulo ake kapena ayi.  Anakuphunzitsani kudzichepetsa pokukhalitsani ndi njala+ ndi kukudyetsani mana,+ amene inu kapena makolo anu sanawadziwe. Anachita zimenezi kuti mudziwe kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse ochokera m’kamwa mwa Yehova.+  Zovala zanu sizinathe ndipo mapazi anu sanatupe m’zaka 40 zimenezi.+  Inu mukudziwa bwino mumtima mwanu kuti Yehova Mulungu wanu anali kukuwongolerani, ngati mmene bambo amawongolerera mwana wake.+  “Muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu mwa kuyenda m’njira zake+ ndi kumuopa.+  Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani m’dziko labwino,+ dziko la zigwa* za madzi,+ akasupe ndi madzi ochuluka otuluka m’zigwa ndi m’madera a mapiri,  dziko la tirigu, balere, mphesa, nkhuyu ndi makangaza,*+ dziko la maolivi opangira mafuta ndiponso la uchi,+  dziko limene mudzadya mkate wosaperewera, limenenso simudzasowa kalikonse, dziko limene miyala yake amapangira zitsulo, limenenso m’mapiri ake mudzakumbamo mkuwa. 10  “Mukadzadya ndi kukhuta+ mudzatamandenso+ Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.+ 11  Samalani kuti musaiwale+ Yehova Mulungu wanu ndi kusasunga malamulo, zigamulo ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero.+ 12  Samalani, kuopera kuti mungadye ndi kukhuta, kumanga nyumba zabwino ndi kukhalamo,+ 13  ng’ombe zanu ndi nkhosa zanu n’kuchuluka, siliva ndi golide wanu n’kuwonjezeka ndiponso zinthu zanu zonse n’kukuchulukirani, 14  mtima wanu n’kuyamba kudzikweza+ ndi kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 15  Mungaiwale amene anakuyendetsani m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni,+ zinkhanira ndiponso dziko louma lopanda madzi. Amenenso anakutulutsirani madzi pamwala wolimba ngati nsangalabwi.+ 16  Mungaiwale amene anakudyetsani mana+ m’chipululu, chakudya chimene makolo anu sanachidziwe, pofuna kukuphunzitsani kudzichepetsa+ ndi kuti akuyeseni kuti potsirizira pake akuchitireni zabwino.+ 17  Samalani kuti munganene mumtima mwanu kuti, ‘Chuma ichi ndachipeza ndi mphamvu zanga ndi nyonga za dzanja langa.’+ 18  Muzikumbukira Yehova Mulungu wanu, chifukwa ndiye amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbirira makolo anu, monga mmene wachitira lero.+ 19  “Koma mukadzaiwala Yehova Mulungu wanu, n’kutsatira milungu ina, kuitumikira ndiponso kuigwadira, ndikukuchitirani umboni lero kuti anthu inu mudzatha.+ 20  Mudzatheratu ngati mitundu imene Yehova akuiwononga pamaso panu, chifukwa simudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.