Ekisodo 12:1-51

12  Tsopano Yehova anauza Mose ndi Aroni m’dziko la Iguputo kuti:  “Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba* wa miyezi ya pa chaka. Chaka chanu chiziyamba ndi mwezi uno.+  Uzani khamu lonse la Isiraeli kuti, ‘Pa tsiku la 10 la mwezi uno mabanja onse ochokera mwa kholo limodzi atenge nkhosa imodziimodzi,+ banja lililonse litenge nkhosa imodzi.  Koma ngati banja lili laling’ono moti silingamalize kudya nkhosa yonseyo, mutu wa banja limenelo agawane ndi munthu wokhala naye pafupi m’nyumba mwake, mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu. Aliyense mum’gawire nkhosayo malinga ndi mmene amadyera.  Nkhosa yanuyo ikhale yopanda chilema,+ yamphongo, yachaka chimodzi.+ Mungatenge mwana wa nkhosa kapena wa mbuzi.  Nkhosayo muisunge kufikira tsiku la 14 la mwezi uno.+ Kenako banja lililonse la Isiraeli lidzaphe nkhosa yawo madzulo kuli kachisisira.*+  Atatero adzatenge magazi ndi kuwaza pamafelemu awiri a m’mbali mwa khomo ndi pafelemu la pamwamba pa chitseko. Adzachite zimenezi panyumba zimene mudzadyeremo nkhosayo.+  “‘Adzadye nyamayo usiku umenewu.+ Idzakhale yowotcha ndipo adzaidye pamodzi ndi mikate yopanda chofufumitsa+ ndi masamba owawa.+  Musadzaidye yaiwisi kapena yowiritsa, yophika ndi madzi, koma mudzadye yowotcha pamoto. Mudzawotche mutu wake pamodzi ndi ziboda ndiponso zam’mimba. 10  Koma musadzasiye nyama iliyonse kuti ifike m’mawa. Iliyonse yotsala kufika m’mawa mudzaipsereze pamoto.+ 11  Kudya kwake mudzadye motere, mudzakhale mutamangirira m’chiuno mwanu,+ mutavala nsapato+ ndiponso mutatenga ndodo m’dzanja lanu. Muzidzadya mofulumira. Ameneyu ndi pasika* wa Yehova.+ 12  Ine ndidzadutsa m’dziko la Iguputo usiku umenewo+ ndi kupha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo, mwana wa munthu kapena wa chiweto.+ Ndipo ndidzapereka ziweruzo pa milungu yonse ya mu Iguputo.+ Ine ndine Yehova.+ 13  Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalamo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo ndi kukupitirirani,+ choncho mliri sudzakugwerani ndi kukuwonongani pamene ndikukantha dziko la Iguputo. 14  “‘Tsiku limeneli lidzakhala chikumbutso kwa inu, ndipo muzichitira Yehova chikondwerero m’mibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale, kuti muzichita chikondwerero chimenechi. 15  Muzidya mkate wopanda chofufumitsa masiku 7. Tsiku loyamba muzichotsa m’nyumba zanu mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa chifukwa aliyense wakudya mkate wokhala ndi chofufumitsa, kuchokera pa tsiku loyamba kukafika pa tsiku la 7,+ munthu wotero adzaphedwa kuti asakhalenso mu Isiraeli.+ 16  Pa tsiku loyamba muzidzachita msonkhano wopatulika, ndipo pa tsiku la 7 muzidzachitanso msonkhano wopatulika.+ Masiku amenewa musamadzagwire ntchito.+ Koma chakudya choti munthu aliyense adye, chimenecho chokha muzidzaphika.+ 17  “‘Muzidzasunga chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ chifukwa pa tsiku limeneli ndidzatulutsa makamu anu m’dziko la Iguputo. Muzidzasunga tsiku limeneli m’mibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 18  M’mwezi woyamba, tsiku la 14 la mwezi umenewo, madzulo muzidzadya mikate yopanda chofufumitsa, mpaka kukafika madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo.+ 19  Musamadzapezeke mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa m’nyumba zanu kwa masiku 7, chifukwa aliyense wakudya mtanda wokhala ndi chofufumitsa, kaya ndi mlendo kapena mbadwa ya Isiraeli,+ munthu ameneyo adzaphedwa kuti asakhalenso mu khamu la Isiraeli.+ 20  Musamadzadye chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. M’nyumba zanu zonse muzidzadya mikate yopanda chofufumitsa.’” 21  Mwamsanga, Mose anaitana akulu onse a Isiraeli+ ndi kuwauza kuti: “Sankhani nkhosa ndi mbuzi* malinga ndi mabanja anu, muiphere nsembe ya pasika.+ 22  Mukatero mutenge kamtengo ka hisope+ n’kukaviika m’beseni la magazi ndi kuwaza pafelemu la pamwamba pa chitseko, ndipo ena mwa magaziwo muwaze pamafelemu awiri a m’mbali mwa khomo. Aliyense asatuluke m’nyumba yake mpaka m’mawa. 23  Pamenepo Yehova akamapita kukapha Aiguputo ndi mliri, akaona magazi pamafelemu a pamwamba pa zitseko zanu ndi mafelemu awiri a m’mbali mwa khomo, Yehova adzapitirira khomo limenelo ndipo sadzalola chiwonongeko kulowa m’nyumba zanu ndi kukuphani.+ 24  “Choncho muzisunga zimenezi, limeneli ndi langizo+ kwa inu ndi kwa ana anu mpaka kalekale.+ 25  Ndipo mukadzalowa m’dziko limene Yehova adzakupatsani, monga mmene ananenera, pamenepo muzidzachita mwambo umenewu.+ 26  Ndiyeno ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’+ 27  pamenepo mudzawauze kuti, ‘Umenewu ndi mwambo wopereka nsembe ya pasika kwa Yehova,+ amene anapitirira nyumba za ana a Isiraeli mu Iguputo pamene anali kupha Aiguputo ndi mliri, koma anapulumutsa mabanja athu.’” Atatero, anthu anagwada ndi kuweramira pansi.+ 28  Pamenepo ana a Isiraeli anachoka ndi kukachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aroni.+ Anachitadi momwemo. 29  Chotero pakati pa usiku, Yehova anapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo.+ Kuyambira mwana woyamba wa Farao, amene wakhala pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa mkaidi amene ali m’ndende yapansi, ndiponso mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse.+ 30  Zitatero Farao, atumiki ake onse ndi Aiguputo onse anadzuka pakati pa usiku. Ndipo anthu anayamba kulira kwambiri m’dziko lonse la Iguputo,+ chifukwa panalibe banja ngakhale limodzi limene linalibe maliro. 31  Nthawi yomweyo Farao anaitanitsa+ Mose ndi Aroni usiku, ndipo anati: “Nyamukani, chokani pakati pa anthu anga, inuyo ndi ana onse a Isiraeli. Pitani, katumikireni Yehova, monga momwe mwanenera.+ 32  Tengani nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu monga mwanenera,+ ndipo pitani. Komanso mukandipemphere madalitso.” 33  Choncho Aiguputo anaumiriza anthuwo kuti achoke m’dzikolo mofulumira.+ Iwo anati, “chifukwa tonsefe tikungokhala ngati tafa kale!”+ 34  Pamenepo Aisiraeli ananyamula ufa wokanda wa mkate wopanda chofufumitsa. Anaunyamulira m’zokandiramo ufa pamapewa awo atazikulunga m’nsalu zawo. 35  Ndipo ana a Isiraeli anachita mogwirizana ndi mawu onse amene Mose anawauza, motero anapempha Aiguputo zinthu zasiliva, zagolide ndi zovala.+ 36  Choncho Yehova anachititsa Aiguputo kukomera mtima anthu ake,+ moti Aiguputo anawapatsa zinthu zonse zimene anapempha,+ ndipo iwo anatenga zinthu zambiri za Aiguputo.+ 37  Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Amuna amphamvu oyenda pansi analipo pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+ 38  Ndipo khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ anapita limodzi ndi ana a Isiraeli. Anapitanso ndi nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zambirimbiri. 39  Ndiyeno ufa wokanda umene anachoka nawo ku Iguputo uja anayamba kuuphika mikate yozungulira yopanda chofufumitsa, chifukwa ufa wokandawo unalibe zofufumitsa. Ufawo unalibe zofufumitsa chifukwa chakuti anawapitikitsa ku Iguputo ndipo anachoka mofulumira kwambiri. Komanso iwo anaphika mikateyo chifukwa chakuti sanathe kukonza chakudya chilichonse ponyamuka.+ 40  Ndiyeno ana a Isiraeli, amene anakhala+ ku Iguputo,+ anakhala m’dziko lachilendo* zaka 430.+ 41  Zaka 430 zimenezi zitatha, pa tsiku lomwe zinatha, makamu onse a Yehova anatuluka m’dziko la Iguputo.+ 42  Usiku umenewu ndi wofunika kuukumbukira polemekeza Yehova, chifukwa anawatulutsa m’dziko la Iguputo. Yehova anafuna kuti ana a Isiraeli onse, m’mibadwo yawo yonse, azikumbukira usiku umenewu.+ 43  Chotero Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Lamulo la pasika ndi ili:+ Mlendo* asadye nawo.+ 44  Koma mwamuna amene ndi kapolo wogulidwa ndi ndalama, muzim’dula.+ Akadulidwa nayenso angathe kudya. 45  Mlendo wobwera kudzakhala nanu ndiponso waganyu asadye nawo. 46  Muzidyera m’nyumba imodzi. Musatuluke panja ndi nyama iliyonse. Komanso musaphwanye fupa lililonse la nyamayo.+ 47  Khamu lonse la Isiraeli lizichita chikondwerero chimenechi.+ 48  Ngati mlendo wokhala nanu akufuna kuchita nanu chikondwerero cha pasika kwa Yehova, mwamuna aliyense wa m’nyumba yake adulidwe.+ Akatero atha kuchita nawo chikondwererocho, ndipo ayenera kuonedwa ngati mbadwa ya dzikolo. Koma munthu wosadulidwa asadye nawo. 49  Lamulo lililonse ligwire ntchito mofanana kwa mbadwa ndi kwa mlendo wokhala pakati panu.”+ 50  Choncho ana onse a Isiraeli anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aroni. Anachitadi momwemo.+ 51  Ndipo pa tsiku limeneli, Yehova anatulutsa ana a Isiraeli malinga ndi makamu awo+ m’dziko la Iguputo.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda, kuyambira pamene iwo anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.
Mawu ake enieni, “pakati pa madzulo awiri.” Malinga n’kunena kwa akatswiri ena, komanso Ayuda achikaraite ndi Asamariya, nthawi imeneyi ikuyambira pamene dzuwa lalowa kufikira pamene mdima weniweni wagwa. Koma Afarisi ndi Arabi ali ndi maganizo osiyana ndi amenewa. Iwo amati, madzulo oyamba ndi pamene dzuwa layamba kupendeka, ndipo madzulo achiwiri ndi kulowa kwa dzuwa kwenikweniko.
M’chinenero choyambirira, mawu omwe tawamasulira kuti “pasika” amatanthauza “kulumpha,” kapena “kupitirira.”
Kapena kuti “ng’ombe zazing’ono.”
Mawu ake enieni, “Ndiyeno kukhala kwa ana a Isiraeli, amene anakhala m’dziko la Iguputo.” Mabaibulo ena akale amasonyeza kuti chiwerengero cha zaka chimene chatchulidwachi sichikuimira zaka zimene Aisiraeli anakhala mu Iguputo mokha ayi, komanso chikuphatikizapo zaka zimene anakhala ku Kanani.
Mawu ake enieni, “Munthu amene si Mwisiraeli.”