Ekisodo 14:1-31
14 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose kuti:
2 “Lankhula ndi ana a Isiraeli kuti abwerere ndi kumanga msasa pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, koma moyang’anizana ndi Baala-zefoni.+ Mumange msasa wanu pafupi ndi nyanja, patsogolo pa Baala-zefoni.
3 Ndiyeno ponena za ana a Isiraeli, Farao adzati, ‘Asokonezeka ndipo akungoyendayenda m’dziko lathu. Chipululu chawatsekera.’+
4 Pamenepo ndidzalola Farao kuumitsa mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzapezerapo ulemerero mwa kugonjetsa Farao ndi magulu ake onse ankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi momwemo.
5 Kenako mfumu ya Iguputo inauzidwa kuti Aisiraeli athawa. Pomwepo mtima wa Farao ndi atumiki ake unasinthanso ataganizira za Aisiraeli,+ moti anati: “Tachitanji pamenepa polola akapolo athu Aisiraeli kuchoka?”+
6 Choncho anakonzekeretsa magaleta* ake ankhondo, n’kutenganso asilikali ake.+
7 Anatenga magaleta osankhidwa mwapadera 600+ ndi magaleta ena onse a Iguputo, ndipo lililonse la magaletawo munakwera asilikali.
8 Choncho Yehova analola Farao mfumu ya Iguputo kuumitsa mtima wake,+ ndipo anathamangira ana a Isiraeli pamene iwo anali kutuluka ndi dzanja lokwezeka.*+
9 Motero Aiguputo anali kuwathamangira, ndipo magaleta onse a Farao, asilikali apamahatchi+ ndi magulu ake ankhondo anawayandikira. Aisiraeliwo anali atamanga msasa m’mphepete mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti moyang’anizana ndi Baala-zefoni.+
10 Farao atafika pafupi, ana a Isiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Pamenepo ana a Isiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.+
11 Choncho iwo anafunsa Mose kuti: “Kodi watibweretsa kuno kuti tidzafere m’chipululu muno chifukwa chakuti mu Iguputo mulibe manda?+ N’chifukwa chiyani watichitira zimenezi, kutitulutsa mu Iguputo?
12 Kodi si zimene tinakuuza tili ku Iguputo, kuti, ‘Tisiye tizitumikira Aiguputo’? Chifukwa n’kwabwino kutumikira Aiguputo kusiyana n’kuti tifere m’chipululu.”+
13 Pamenepo Mose anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Chilimikani ndi kuona chipulumutso cha Yehova chimene akuchitireni lero.+ Pakuti Aiguputo amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso, ndithu, simudzawaonanso.+
14 Yehova adzakumenyerani nkhondo,+ ndipo inu mudzakhala chete, osachitapo kalikonse.”
15 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “N’chifukwa chiyani ukudandaula?+ Uza ana a Isiraeli kuti anyamuke.
16 Ndipo iwe, tenga ndodo yako+ ndi kutambasula dzanja lako kuloza panyanja kuti nyanjayo igawanike.+ Ukatero ana a Isiraeli adutsa pakati pa nyanja, panthaka youma.+
17 Koma ine ndilola Aiguputo kuumitsa mitima yawo,+ kuti atsatire Aisiraeli panyanjapo, kutinso ndipezerepo ulemerero mwa kugonjetsa Farao, magulu ake onse ankhondo, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.+
18 Ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndikadzipezera ulemerero mwa kugonjetsa Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.”+
19 Ndiyeno mngelo+ wa Mulungu woona amene anali kuyenda patsogolo pa Aisiraeli anachoka n’kupita kumbuyo kwawo. Motero, mtambo woima njo ngati chipilala uja unachoka kutsogolo n’kukaima kumbuyo kwawo.+
20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unali kuchititsa mdima, ndipo mbali ina unali kuwaunikira usiku.+ Ndipo gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse.
21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+
22 Patapita nthawi ana a Isiraeli anadutsa pakati pa nyanja, panthaka youma,+ madziwo ataima ngati khoma* kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+
23 Pamenepo Aiguputo anawalondola, ndipo mahatchi onse a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi, anayamba kuwathamangira,+ kulowa pakati pa nyanja.
24 Ndiyeno pa nthawi ya ulonda wam’mawa,* Yehova ali mumtambo ndi moto woima njo ngati chipilala,+ anayang’ana gulu la Aiguputo, ndipo anachititsa Aiguputowo kusokonezeka.+
25 Iye anali kugulula mawilo a magaleta awo moti anali kuwayendetsa movutikira.+ Pamenepo Aiguputo anayamba kunena kuti: “Tiyeni tithawe pamaso pa Isiraeli, chifukwa Yehova akuwamenyera nkhondo yolimbana ndi Aiguputo.”+
26 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza panyanja,+ kuti madzi abwerere ndi kumiza Aiguputo, magaleta awo ankhondo ndi asilikali awo apamahatchi.”
27 Nthawi yomweyo Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza panyanja, ndipo nyanjayo inayamba kubwerera m’malo mwake, kuli pafupi kucha. Pamenepo Aiguputo anayamba kuthawa kuti madziwo asawapeze, koma Yehova anakutumulira Aiguputowo pakatikati pa nyanja.+
28 Choncho madziwo anabwereradi,+ ndipo anamiza magaleta ankhondo ndi asilikali apamahatchi a magulu onse ankhondo a Farao, amene analondola Aisiraeli m’nyanjamo.+ Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+
29 Koma ana Aisiraeli anayenda panthaka youma pakati pa nyanja,+ ndipo madzi anaima ngati khoma kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+
30 Choncho pa tsiku limenelo Yehova anapulumutsa Isiraeli m’manja mwa Aiguputo,+ ndipo Isiraeli anaona Aiguputo atafa m’mphepete mwa nyanja.+
31 Isiraeli anaonanso dzanja lamphamvu limene Yehova anagonjetsa nalo Aiguputo. Pamenepo Aisiraeli anayamba kuopa Yehova ndi kukhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mawu akuti “dzanja lokwezeka” akutanthauza kuti ana a Isiraeli anatuluka mosonyeza mphamvu, kulimba mtima ndi kupambana.
^ Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
^ Aheberi ankagawa usiku m’magawo atatu, ndipo uwu unali ulonda wachitatu komanso womaliza. Unali kuyamba cha m’ma 2 koloko usiku mpaka 6 koloko m’mawa.