Ekisodo 23:1-33
23 “Usafalitse nkhani yabodza.+ Usagwirizane ndi munthu woipa mwa kukhala mboni yokonzera wina zoipa.+
2 Usatsatire khamu pochita zoipa.+ Pa mlandu usapereke umboni wopotoza chilungamo potsatira khamu la anthu.+
3 Usakondere munthu wosauka pa mlandu wake.+
4 “Ukapeza ng’ombe kapena bulu wa mdani wako atasochera, um’bweze ndithu kwa mwiniwake.+
5 Ukaona bulu wa munthu wodana nawe atagona pansi polemedwa ndi katundu, pamenepo usam’siye yekha munthu wodana naweyo. Uthandizane naye kumasula katunduyo.+
6 “Usapotoze chigamulo cha munthu wosauka wokhala pakati panu, pa mlandu wake.+
7 “Utalikirane ndi mawu onama.+ Usaphe munthu wosalakwa ndi munthu wolungama, chifukwa woipa sindidzamuyesa wolungama.+
8 “Usalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+
9 “Usapondereze mlendo wokhala pakati panu,+ popeza mukudziwa mmene zimakhalira ukakhala mlendo, chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+
10 “Kwa zaka 6 uzilima munda wako ndi kukolola.+
11 Koma chaka cha 7 usaulime, uusiye kuti ugonere.+ Osauka mwa anthu ako adye za m’mundamo ndipo zimene iwo asiya, zilombo zakutchire zidye.+ Uzichita zimenezi ndi munda wako wa mpesa ndi wa maolivi.
12 “Uzigwira ntchito masiku 6.+ Koma tsiku la 7 usamagwire ntchito, kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zizipuma, ndipo mwana wa kapolo wako wamkazi ndi mlendo azipumula.+
13 “Muzisamalira zonse zimene ndakuuzani,+ ndipo musatchule dzina la milungu ina. Lisamveke pakamwa panu.+
14 “Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+
15 Muzichita chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda chofufumitsa+ masiku 7 pa nthawi yake m’mwezi wa Abibu,*+ monga momwe ndakulamulirani, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi umenewu. Ndipo palibe ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+
16 Komanso muzichita chikondwerero cha zokolola, chokondwerera zipatso za ntchito ya manja anu zoyamba kucha+ zimene munabzala m’munda.+ Muzichitanso chikondwerero cha kututa kumapeto kwa chaka, pamene mututa zipatso za manja anu, zam’munda.+
17 Katatu pa chaka mwamuna aliyense pakati panu azionekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova.+
18 “Popereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. Ndipo mafuta a chikondwerero changa asamagone mpaka m’mawa.+
19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+
“Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+
20 “Tsopano ndikukutumizira mngelo+ wokutsogolera kuti akuteteze m’njira ndi kukakulowetsa m’dziko limene ndakukonzera.+
21 Samala ndipo umvere mawu ake. Usam’pandukire, chifukwa sadzalekerera zolakwa zanu,+ pakuti dzina langa lili mwa iye.
22 Koma ukalabadiradi mawu ake ndi kuchitadi zonse zimene ine ndidzanena,+ pamenepo ndidzalusira adani ako ndi kuvutitsa okuvutitsa.+
23 Pakuti mngelo wanga adzakutsogolera ndi kukulowetsa m’dziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawafafaniza ndithu.+
24 Usaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo usapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo,+ koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+
25 Muzitumikira Yehova Mulungu wanu,+ ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi.+ Ndipo ndidzachotsa matenda pakati panu.+
26 M’dziko lanu simudzapezeka mkazi wopititsa padera kapena wosabereka.+ Ndipo ndidzachulukitsa masiku anu.+
27 “Iwe usanafike, ndidzachititsa anthu kumva za ine+ ndipo adzanjenjemera. Ndidzasokoneza anthu onse amene udzawapeze. Adani ako onse adzachita mantha ndipo adzathawa.*+
28 Iwe usanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso pako.+
29 Sindidzawathamangitsa pamaso pako m’chaka chimodzi, kuti dzikolo lingakhale bwinja ndi kuti zilombo zakutchire zingachuluke ndi kukuvutitsa.+
30 Ndidzawathamangitsa pamaso pako pang’onopang’ono kufikira mutaberekana ndi kulanda dzikolo.+
31 “Dziko limene ndidzakupatsa lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita izi, chifukwa anthu okhala m’dzikomo ndidzawapereka m’manja mwako, ndipo iwe udzawathamangitsa pamaso pako.+
32 Usachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo.+
33 Asakhale m’dziko lako, kuti asakuchimwitse pamaso panga. Ukatumikira milungu yawo, umenewo udzakhala msampha kwa iwe.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 13.
^ Mawu ake enieni, “Ndidzakupatsa kumbuyo kwa makosi a adani ako onse.”
^ Mabaibulo a Septuagint ndi Vulgate amanena kuti, “ndidzatumizira anthuwo mavu.”
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.