Ekisodo 27:1-21

27  “Upange guwa lansembe la matabwa a mthethe, m’litali mikono isanu, ndipo m’lifupi mikono isanu. Guwalo+ likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake likhale mikono itatu.  Upange nyanga m’makona ake anayi. Nyanga+ zakezo zituluke m’makona akewo, ndipo ulikute ndi mkuwa.+  Kenako upange ndowa zake zochotsera phulusa losakanizika ndi mafuta, mafosholo ake, mbale zake zolowa, mafoloko aakulu, ndi zopalira moto zake. Ziwiya zake zonse uzipange ndi mkuwa.+  Upangenso sefa wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana,+ ndipo pasefayo upange mphete zinayi zamkuwa m’makona ake anayi.  Ulowetse sefayo chapakati pa guwa lansembe, m’munsi mwa mkombero.+  Guwalo ulipangire mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe, ndipo uikute ndi mkuwa.+  Mitengo yonyamulirayo uziilowetsa mumphetezo kumbali ziwiri za guwalo polinyamula.+  Upange bokosi lamatabwa losatseka pansi. Alipange mmene iye wakusonyezera m’phiri.+  “Ndiyeno upange bwalo+ la chihema chopatulika. Kumbali ya ku Negebu, chakum’mwera, bwalolo ulitchinge ndi mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri.+ Mpandawo ukhale mikono 100 m’litali mwake kumbali imodziyo. 10  Upangenso nsanamira zake 20 ndi zitsulo zamkuwa 20 zamphako zokhazikapo nsanamirazo. Tizitsulo tokolowekapo nsalu ndi mfundo zake zikhale zasiliva.+ 11  Mpandawo kumbali yakumpoto, m’litali mwake ukhalenso momwemo. Nsalu yampandawo ikhale mikono 100 m’litali mwake, ndipo kukhale nsanamira 20 ndi zitsulo zamkuwa 20 zamphako zokhazikapo nsanamirazo. Tizitsulo tokolowekapo nsalu ndi mfundo zake zikhale zasiliva.+ 12  M’lifupi mwa bwalolo, kumbali ya kumadzulo, mpanda wa nsaluwo ukhale mikono 50 kutalika kwake, ndipo kukhale nsanamira 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo nsanamirazo.+ 13  Ndipo m’lifupi mwa bwalolo kumbali ya kum’mawa, kotulukira dzuwa, kukhale mikono 50.+ 14  Kudzanja lamanja la chipata cha bwalolo, mpanda wa nsaluwo ukhale mikono 15 kutalika kwake. Kukhale nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+ 15  Ndipo kudzanja lamanzere la chipata cha bwalolo kukhale nsalu za mpanda mikono 15. Kukhale nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+ 16  “Pachipata cha bwalo pakhale nsalu yowomba m’litali mwake ikhale mikono 20, ya ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.+ Pakhale nsanamira zinayi ndi zitsulo zinayi zokhazikapo nsanamirazo.+ 17  Nsanamira zonse kuzungulira bwalo lonselo zikhale ndi mfundo zasiliva, ndipo tizitsulo tokolowekapo nsalu tikhale tasiliva, koma zitsulo zokhazikapo nsanamirazo zikhale zamkuwa.+ 18  Bwaloli m’litali mwake likhale mikono 100,+ m’lifupi mwake mikono 50, ndipo msinkhu wake mikono isanu. Nsalu zake zikhale za ulusi wopota, wabwino kwambiri, ndipo zitsulo zake zokhazikapo nsanamira zikhale zamkuwa. 19  Ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wonse wa pachihema chopatulika, zikhomo zonse za chihema, ndi zikhomo za bwalo zikhale zamkuwa.+ 20  “Koma iwe, ulamule ana a Isiraeli kuti akupezere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 21  M’chihema chokumanako,* kunja kwa nsalu yotchinga+ pafupi ndi Umboni, Aroni ndi ana ake azikhazika nyale pamalo ake, kuunikira pamaso pa Yehova,+ kuyambira madzulo mpaka m’mawa. Limeneli ndi lamulo kwa ana a Isiraeli+ kuti mibadwo yawo izichita zimenezi mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “chihema chokumanako ndi Mulungu.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.