Ekisodo 33:1-23

33  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Nyamukani, muchoke pano, iweyo ndi anthu amene unawatsogolera potuluka m’dziko la Iguputo.+ Mupite kudziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzapereka dziko ili kwa mbewu yako.’+  Ndipo ndidzatumiza mngelo patsogolo panu+ kuti akathamangitse Akanani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+  Mupite kudziko loyenda mkaka ndi uchi,+ pakuti sindidzayenda pakati panu, pakuti ndingakufafanizeni panjira,+ chifukwa ndinu anthu ouma khosi.”+  Anthu atamva mawu odetsa nkhawa amenewa, anayamba kulira,+ ndipo palibe aliyense wa iwo anavala zodzikongoletsera.  Ndiyeno Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Inu ndinu anthu ouma khosi.+ Ndingathe kulowa pakati panu ndi kukufafanizani m’kamphindi.+ Chotero, vulani zodzikongoletsera, pakuti ndikufuna kuona choti ndikuchiteni.’”+  Pamenepo ana a Isiraeli anavula zodzikongoletsera ali kuphiri la Horebe+ ndipo sanazivalenso.  Zitatero, Mose anatenga hema wake ndi kukam’manga kunja kwa msasa, kutali kwambiri ndi msasawo, ndipo anatcha hemayo dzina lakuti chihema chokumanako. Aliyense wofuna kufunsira+ kwa Yehova anali kupita kuchihema chokumanako, chimene chinali kunja kwa msasa.  Ndiyeno Mose akatuluka mumsasawo kupita kuchihema, anthu onse anali kuimirira.+ Aliyense anali kuimirira pakhomo la hema wake, n’kumayang’anitsitsa Mose kufikira atalowa m’chihema.  Ndipo Mose akangolowa m’chihema, mtambo woima njo ngati chipilala+ unali kutsika ndi kuima pakhomo la chihemacho. Zikatero Mulungu anali kulankhula+ ndi Mose. 10  Anthu onse anali kuona mtambowo+ utaima pakhomo la chihema, ndipo onse anali kuimirira ndi kugwada, aliyense pakhomo la hema wake.+ 11  Pamenepo Yehova anali kulankhula ndi Mose pamasom’pamaso,+ mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake. Mose akabwerera kumsasa, mtumiki wake+ Yoswa, mwana wa Nuni,+ sanali kuchoka m’chihemacho, popeza anali kalinde. 12  Tsopano Mose anauza Yehova kuti: “Inu mukundiuza kuti, ‘Tsogolera anthuwa,’ koma simunandidziwitse amene mudzam’tuma kuti ndiyende naye limodzi. Komanso mwanena kuti ‘Ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe,+ ndipo ndakukomera mtima.’ 13  Tsopano ngati mwandikomera mtima,+ chonde ndidziwitseni njira zanu,+ kuti ndikudziweni, kutinso mundikomere mtima. Ndipo kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”+ 14  Pamenepo Mulungu anati: “Ineyo ndidzayenda nawe+ ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”+ 15  Zitatero iye anati: “Ngati inuyo simuyenda nafe, musatichotse pano. 16  Ndipo ndidziwa bwanji kuti mwandikomera mtima, ineyo ndi anthu anu? Si mwa kuyenda nafe kodi?+ Pajatu ine ndi anthu anu mwatisiyanitsa ndi anthu ena onse amene ali padziko lapansi.”+ 17  Chotero Yehova anatinso kwa Mose: “Ndidzachita izinso zimene wanena,+ chifukwa ndakukomera mtima ndipo ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe.” 18  Pamenepo Mose anati: “Ndionetseni ulemerero wanu.”+ 19  Koma Mulungu anati: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse,+ ndipo ndidzalengeza dzina langa lakuti Yehova kwa iwe.+ Amene ndikufuna kum’komera mtima ndidzam’komera mtima, ndipo amene ndikufuna kum’sonyeza chifundo, ndidzam’sonyeza chifundo.”+ 20  Ndipo anawonjezera kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu angandione n’kukhalabe ndi moyo.”+ 21  Ndiyeno Yehova ananenanso kuti: “Nawa malo pafupi ndi ine, ndipo ukakhale pathanthwepo. 22  Choncho pamene ulemerero wanga ukudutsa pafupi ndi iwe, ndidzakuika kuphanga la thanthwelo, ndipo ndidzakuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23  Kenako ndidzachotsa dzanja langa, ndipo udzaona kumsana kwanga, koma nkhope yanga sudzaiona.”+

Mawu a M'munsi