Ekisodo 38:1-31
38 Ndiyeno anapanga guwa lansembe zopsereza la matabwa a mthethe, m’litali mwake mikono isanu, ndipo m’lifupi mikono isanu. Guwalo linali lofanana muyezo wake mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake linali mikono itatu.+
2 Anapanganso nyanga+ m’makona ake anayi. Nyanga zakezo zinatuluka m’makona akewo, ndipo guwalo analikuta ndi mkuwa.+
3 Kenako anapanga ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo. Anapanga ndowa, mafosholo, mbale zolowa, mafoloko aakulu, ndi zopalira moto. Ziwiya zake zonse anazipanga ndi mkuwa.+
4 Guwalo analipangiranso sefa wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana. Analowetsa sefayo cha pakati pa guwa lansembe, m’munsi mwa mkombero.+
5 Analipangiranso mphete zinayi m’makona ake anayi kuti muzilowa mitengo yonyamulira. Mphetezo anazilumikiza pafupi ndi sefa wa zitsulo zamkuwa.
6 Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe, ndipo anaikuta ndi mkuwa.+
7 Mitengoyo anailowetsa m’mphetezo m’mbali mwa guwalo kuti ikhale yonyamulira guwalo.+ Guwa limenelo analipanga ngati bokosi lamatabwa losatseka pansi.+
8 Kenako anapanga beseni losambira lamkuwa+ ndi choikapo chake chamkuwa. Popanga zimenezi anagwiritsa ntchito akalirole* a akazi otumikira, amene anali kutumikira mwadongosolo pachipata cha chihema chokumanako.+
9 Ndiyeno anapanga bwalo la chihema chopatulika.+ Kumbali ya ku Negebu, chakum’mwera, bwalolo analitchinga ndi mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri. Mpandawo unali mikono 100 kutalika kwake kumbali imodziyo.+
10 Nsanamira zake 20 ndi zitsulo 20 zamphako zokhazikapo nsanamirazo zinali zamkuwa. Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.+
11 Kumbali yakumpoto, mpandawo unali mikono 100 kutalika kwake. Nsanamira zake 20 ndi zitsulo 20 zokhazikapo nsanamirazo zinali zamkuwa. Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.+
12 Koma kumbali yakumadzulo, mpanda wa nsaluwo unali mikono 50 kutalika kwake. Kunali nsanamira 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo nsanamirazo.+ Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.
13 Ndipo kumbali yakum’mawa, kotulukira dzuwa, mpandawo unali mikono 50 kutalika kwake.+
14 Kumbali imodzi ya chipata cha bwalo, mpanda wa nsaluwo unali mikono 15. Kunali nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+
15 Ndipo kumbali inanso ya chipata cha bwalolo, mpandawo unali mikono 15 kutalika kwake. Zinali choncho kumbali iyi ya chipata komanso kumbali inayo. Kunali nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+
16 Nsalu zonse za mpanda wotchingira bwalo lonselo zinali za ulusi wopota wabwino kwambiri.
17 Ndipo zitsulo zokhazikapo nsanamira zinali zamkuwa. Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu za mpanda ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. Mitu ya nsanamirazo inali yokutidwa ndi siliva, ndipo nsanamira zonse za bwalo zinali ndi tizitsulo tasiliva tolumikizira.+
18 Ndiyeno nsalu yotchinga pachipata cha bwalo inali yowombedwa mwaluso. Anaiwomba ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ Inali mikono 20 kutalika kwake, ndipo nsalu yonseyo msinkhu wake unali mikono isanu, mofanana ndi nsalu zotchingira mpanda wa bwalo.+
19 Mizati yake inayi ndi zitsulo zinayi zokhazikapo mizatiyo zinali zamkuwa. Tizitsulo ta mizatiyo tokolowekapo nsalu tinali tasiliva, ndipo mitu ya mizatiyo ndi tizitsulo tolumikizira anazikuta ndi siliva.
20 Zikhomo zonse za chihema chopatulika ndi za bwalo lonse zinali zamkuwa.+
21 Tsopano izi ndiye zinthu zonse zimene anawerengera za chihema chopatulika, chihema cha Umboni,+ monga mwa ntchito ya Alevi,+ motsogoleredwa ndi Itamara+ mwana wa Aroni wansembe. Iwo anawerengera zimenezi Mose atalamula.
22 Bezaleli+ mwana wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda, anachita zonse zimene Yehova analamula Mose.
23 Iye anali ndi Oholiabu,+ mwana wa Ahisama wa fuko la Dani, mmisiri wa ntchito zosiyanasiyana, katswiri wodziwa kupeta ndi wodziwa kuwomba nsalu ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.
24 Golide yense amene anagwiritsidwa ntchito pa ntchito yonse ya pamalo oyera, anali woperekedwa monga nsembe yoweyula.*+ Muyezo wake unali matalente 29 ndi masekeli 730 pamuyezo wolingana ndi sekeli+ la kumalo oyera.*+
25 Ndipo siliva wa anthu amene anawerengedwa m’khamu la Isiraeli, anali matalente 100 ndi masekeli 1,775 pamuyezo wolingana ndi sekeli la kumalo oyera.
26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli lolingana ndi hafu ya sekeli la kumalo oyera. Owerengedwa onse anakwana 603,550.+
27 Matalente 100 asiliva anawagwiritsa ntchito kupangira zitsulo zamphako za malo oyera zokhazikapo mafelemu ndi zitsulo zamphako za pafupi ndi nsalu yotchinga. Anagwiritsa ntchito matalente 100 kupangira zitsulo 100 zamphako, talente imodzi anapangira chitsulo chimodzi.+
28 Masekeli 1,775 asiliva anawagwiritsa ntchito kupangira tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu, ndi kukutira mitu ya nsanamirazo. Atatero analumikiza nsanamirazo.
29 Mkuwa wa nsembe yoweyula unali matalente 70 ndi masekeli 2,400.
30 Ndipo mkuwa umenewu anaugwiritsa ntchito kupangira zitsulo zamphako zokhazikapo mizati ya pakhomo la chihema chokumanako, guwa lansembe lamkuwa, sefa wa guwalo wa zitsulo zolukanalukana ndi ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo.
31 Anapangiranso zitsulo zokhazikapo nsanamira za mpanda wa bwalo lonse, zitsulo zokhazikapo mizati ya pachipata cha bwalolo, zikhomo+ zonse za chihema chopatulika ndi zikhomo zonse za bwalo.
Mawu a M'munsi
^ Amenewa anali akalirole achitsulo amene anali kuwasalalitsa kwambiri kuti azionetsa nkhope.