Ekisodo 5:1-23
5 Kenako Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndi kumuuza kuti:+ “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lolani anthu anga apite m’chipululu kuti akachite chikondwerero.’”+
2 Koma Farao anati: “Yehova ndani+ kuti ndimvere mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite?+ Ine sindikum’dziwa Yehova ngakhale pang’ono,+ komanso, sindilola kuti Aisiraeli apite.”+
3 Koma iwo anati: “Mulungu wa Aheberi walankhula nafe.+ Chotero mutilole chonde, tipite ulendo wamasiku atatu m’chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.+ Ngati sititero, adzatipha ndi mliri kapena lupanga.”+
4 Pamenepo mfumu ya Iguputo inawauza kuti: “N’chifukwa chiyani iwe Mose ndi Aroni mukufuna kuti anthu asiye ntchito zawo?+ Bwererani ku ukapolo wanu!”+
5 Farao anapitiriza kuti: “Anthu amenewa ndi ambiri m’dziko lino,+ ndipo inu mukufuna kuwasiyitsa ntchito yawo ya ukapolo.”+
6 Tsiku lomwelo Farao analamula amene anali kugwiritsa ntchito anthuwo mwankhanza, ndi akapitawo a anthuwo+ kuti:
7 “Anthu amenewa musawapezerenso udzu woumbira njerwa+ ngati kale. Muwasiye azikafuna okha udzu umenewo.
8 Komanso, muwauze kuti chiwerengero cha njerwa zofunika chikhale chakale chomwe chija. Musawachepetsere chiwerengerocho, chifukwa ayamba ulesi.+ N’chifukwa chake akulira kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu!’+
9 Agwiritseni ntchito yakalavulagaga anthu amenewa ndipo muonetsetse kuti sakuchita ulesi ndi kumvera zabodza.”+
10 Choncho amene anali kugwiritsa ntchito anthuwo,+ pamodzi ndi akapitawo anapita kwa Aisiraeli n’kukawauza kuti: “Mverani zimene Farao wanena, ‘Sindikupatsaninso udzu woumbira njerwa.
11 Inuyo muzikafuna nokha udzu kulikonse kumene mungaupeze, koma ntchito yanu sichepetsedwa ngakhale pang’ono.’”+
12 Chotero, anthu anali balalabalala m’dziko lonse la Iguputo kukafuna mapesi m’malo mwa udzu.
13 Motero amene anali kuwagwiritsa ntchito aja anali kuwakakamiza+ kugwira ntchito ponena kuti: “Muzimaliza ntchito yanu. Aliyense azimaliza ntchito yake tsiku lililonse, ngati mmene munali kuchitira pamene udzu unali kupezeka.”+
14 Kenako oyang’anira ntchito+ a Farao anamenya+ akapitawo a ana a Isiraeli amene iwo anawaika, n’kumati: “N’chifukwa chiyani dzulo ndi lero simunamalize kuumba njerwa+ zimene munauzidwa ngati mmene munali kuchitira kale?”+
15 Zitatero akapitawo+ a ana a Isiraeli anapita kwa Farao ndi kumudandaulira kuti: “N’chifukwa chiyani atumiki anu mukuwachitira zimenezi?
16 Ife atumiki anu sitikupatsidwa udzu, koma akutiuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ ndipo tikumenyedwa ngakhale kuti olakwa ndi anthu anu.”+
17 Koma iye anati: “Mukuchita ulesi, mukuchita ulesi!+ N’chifukwa chake mukunena kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’+
18 Choncho pitani, katumikireni! Ngakhale kuti sakupatsani udzu, komabe chiwerengero cha njerwa zimene muziumba sichisintha.”+
19 Pamenepo akapitawo a ana a Isiraeli anaona kuti zinthu zawaipira atamva mawu akuti:+ “Musachepetse ngakhale pang’ono chiwerengero cha njerwa zimene aliyense amaumba tsiku ndi tsiku.”+
20 Zitatero anakumana ndi Mose ndi Aroni,+ amene anali kudikira akapitawowa kuti aonane nawo pamene amachokera kwa Farao.
21 Nthawi yomweyo iwo anati: “Yehova aone zimene mwachitazi ndipo akuweruzeni,+ chifukwa mwatinunkhitsa+ pamaso pa Farao ndi atumiki ake, moti mwawapatsa lupanga m’manja mwawo kuti atiphe.”+
22 Pamenepo Mose anatembenukira kwa Yehova+ n’kunena kuti: “Yehova, n’chifukwa chiyani mwadzetsa zoipa pa anthu awa?+ Mwanditumiranji ine?+
23 Kuchokera pamene ndinapita kukalankhula ndi Farao m’dzina lanu,+ iye wachitira anthu awa zinthu zoipa,+ ndipo inu simunalanditse anthu anu.”+