Ekisodo 8:1-32
8 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+
2 Ngati upitiriza kukana kuti apite, ndigwetsera dziko lako lonse mliri wa achule.+
3 Achulewo adzachuluka kwambiri mumtsinje wa Nailo, ndipo adzatuluka mumtsinjemo ndi kulowa m’nyumba yako, m’chipinda chako chogona, pabedi pako, ndiponso m’nyumba za atumiki ako, za anthu ako, m’mauvuni ako, ndi m’ziwiya zako zokandiramo ufa.+
4 Ndipo achulewo adzabwera kwa iwe, anthu ako ndi atumiki ako onse.”’”+
5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tambasula dzanja lako ndi kulozetsa ndodo+ yako kumitsinje, kungalande zochokera kumtsinje wa Nailo ndi kuzithaphwi, kuti achule atuluke mmenemo ndi kubwera pamtunda m’dziko lonse la Iguputo.’”
6 Pamenepo Aroni anatambasula dzanja lake ndi kuloza madzi onse a mu Iguputo, ndipo achule anayamba kutuluka ndi kudzaza dziko lonse la Iguputo.
7 Komabe, ansembe ochita zamatsenga anachitanso zomwezo mwa matsenga awo, ndipo anachititsa achule kubwera pamtunda m’dziko la Iguputo.+
8 Patapita nthawi, Farao anaitana Mose ndi Aroni ndi kuwauza kuti: “Chondererani Yehova+ kuti achotse achule pa ine ndi anthu anga, pakuti ndikufuna kulola anthu anu kuti apite kukapereka nsembe kwa Yehova.”+
9 Ndiyeno Mose anauza Farao kuti: “Munene ndinu kuti ndikachonderere liti kwa Mulungu m’malo mwa inu, m’malo mwa atumiki anu, ndi anthu anu, kuti iye achotse achule pa inu ndi m’nyumba zanu. Koma achulewo adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.”
10 Pamenepo Farao anayankha kuti: “Mawa.” Ndiyeno Mose anati: “Zidzachitika monga mwa mawu anu, kuti mudziwe kuti palibenso wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,+
11 popeza achule adzachoka pa inu, panyumba zanu, pa atumiki anu ndi pa anthu anu. Adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.”+
12 Chotero Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa Farao, ndipo Mose anafuulira Yehova+ kuti achotse achule amene Iye anagwetsera Farao.
13 Pamenepo Yehova anachita monga mmene Mose anapemphera,+ ndipo achule amene anali m’nyumba, m’mabwalo ndi m’minda anayamba kufa.
14 Aiguputo anayamba kuunjika achulewo milumilu, ndipo dziko lonselo linayamba kununkha.+
15 Farao ataona kuti mliri wa achulewo watha, anaumitsa mtima wake,+ ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, monga momwe Yehova ananenera.+
16 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo+ yako ndi kumenya fumbi lapansi, kuti likhale ntchentche zoluma m’dziko lonse la Iguputo.’”
17 Iwo anachitadi zomwezo. Choncho Aroni anatambasula dzanja lake ndi kumenya fumbi lapansi ndi ndodo yake, ndipo ntchentchezo zinayamba kuluma anthu ndi nyama zomwe. Fumbi lonse la m’dziko la Iguputo linasanduka ntchentche zoluma.+
18 Ndipo ansembe ochita zamatsenga, anafunanso kuti apange ntchentche zoluma mwa matsenga awo,+ koma analephera.+ Ndipo ntchentchezo zinali kuluma anthu ndi nyama zomwe.
19 Ataona zimenezi ansembe ochita zamatsenga anauza Farao kuti: “Chimenechi ndi chala cha Mulungu!”+ Koma Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake,+ ndipo sanamvere, monga momwe Yehova ananenera.
20 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ulawirire m’mawa kwambiri kukakumana ndi Farao.+ Iyetu adzapita kumtsinje, ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+
21 Koma ngati sulola anthu anga kupita, taona nditumiza tizilombo touluka toyamwa magazi+ kwa iweyo, atumiki ako, anthu ako ndi m’nyumba zanu. Ndipo nyumba za mu Iguputo zidzangodzaziratu ndi tizilombo timeneti, komanso pena paliponse pamene pali anthu.
22 Pa tsiku limenelo ndidzapatula dera la Goseni kumene kuli anthu anga, kuti kusakhale tizilombo toyamwa magazi.+ Ndidzatero kuti udziwe kuti ine ndine Yehova, ndipo ndili ndi mphamvu padziko lonse lapansi.+
23 Ndipo ndidzaika malire pakati pa anthu anga ndi anthu ako.+ Mawa chizindikiro chimenechi chidzachitika.”’”
24 Yehova anachitadi zimenezo, moti tizilombo touluka toyamwa magazi tinali ponseponse m’nyumba ya Farao, m’nyumba za atumiki ake ndi m’dziko lonse la Iguputo.+ Dziko linaipa chifukwa cha tizilombo timeneto.+
25 Zitatero, Farao anaitana Mose ndi Aroni ndi kuwauza kuti: “Pitani, kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu m’dziko lomwe lino.”+
26 Koma Mose anati: “Sikoyenera kuchita zimenezo, chifukwa mwina chinthu chomwe tingapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu chingakhale chonyansa kwa Aiguputo.+ Kodi Aiguputo sadzatiponya miyala ngati tingapereke nsembe chinthu chonyansa pamaso pawo?
27 Ife tidzapita ulendo wamasiku atatu m’chipululu, ndipo kumeneko tikapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, monga momwe watiuzira.”+
28 Ndiyeno Farao anati: “Ineyo ndikulolani kupita,+ ndipo mukaperekadi nsembe kwa Yehova Mulungu wanu m’chipululu,+ koma musapite kutali kwambiri. Ndichonderereni kwa Mulungu wanu.”+
29 Pamenepo Mose anati: “Mmene ndikuchoka pano, ndikukachonderera Yehova ndipo mawa tizilomboti tichoka pa Farao, atumiki ake ndi anthu ake. Koma Farao asatipusitsenso mwa kusalola anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Yehova.”+
30 Zitatero Mose anachoka pamaso pa Farao ndipo anapita kukachonderera Yehova.+
31 Choncho Yehova anachita monga momwe Mose anapemphera,+ ndipo tizilomboto tinachoka pa Farao, atumiki ake ndi anthu ake.+ Sipanatsale kachilombo ngakhale n’kamodzi komwe.
32 Koma pamenepanso, Farao anaumitsa mtima wake, ndipo sanalole anthuwo kuchoka.+