Esitere 9:1-32

9  Tsiku la 13 la mwezi wa 12, umene ndi mwezi wa Adara,*+ linali tsiku limene mawu a mfumu ndi chilamulo chake zinayenera kuchitika.+ Limeneli linali tsiku limene adani a Ayuda anali kuyembekezera kugonjetsa Ayudawo. Koma pa tsikuli zinthu zinasintha, moti Ayudawo ndi amene anagonjetsa anthu amene anali kudana nawo.+  Ayuda anasonkhana pamodzi+ m’mizinda yawo m’zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero+ kuti agwire anthu amene anali kufuna kuwachitira zinthu zoipa.+ Ndipo palibe munthu amene analimba mtima pamaso pawo chifukwa anthu a mitundu yonse anali kuopa+ Ayudawo.  Akalonga onse+ a m’zigawozo, masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi onse ogwira ntchito+ za mfumu anali kuthandiza Ayudawo chifukwa anali kuopa+ Moredekai.  Izi zinali choncho chifukwa Moredekai anali ndi udindo waukulu+ m’nyumba ya mfumu ndipo anatchuka+ m’zigawo zonse chifukwa mphamvu zake zinali kukulirakulira.+  Ndiyeno Ayuda anakantha adani awo onse ndipo anawapha ndi kuwawononga ndi lupanga.+ Ayudawo anachita zonse zimene anali kufuna kwa anthu amene anali kudana nawo.+  Kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ Ayudawo anapha ndi kuwononga amuna 500.  Iwo anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata,  Porata, Adaliya, Aridata,  Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaizata, 10  ana aamuna 10+ a Hamani+ mwana wa Hamedata amene anali kudana ndi Ayuda.+ Ayuda anapha amuna amenewa koma sanafunkhe+ zinthu zawo. 11  Pa tsiku limenelo mfumu anaiuza chiwerengero cha anthu amene anaphedwa kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani. 12  Ndiyeno mfumu inauza Mfumukazi Esitere+ kuti: “Kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani+ Ayuda apha ndi kuwononga amuna 500 pamodzi ndi ana 10 a Hamani. Ndiye kuli bwanji nanga m’zigawo zina zonse+ za mfumu?+ Choncho, ukufuna kupempha chiyani? Chimene ukufunacho ndikupatsa.+ Ukufunanso chiyani china?+ Chimene ukufunacho chichitika.” 13  Pamenepo Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu,+ lolani kuti mawa Ayuda amene ali mu Susani achite mogwirizana ndi zimene lamulo laleroli likunena.+ Lolani kuti ana aamuna 10 a Hamani apachikidwe pamtengo.”+ 14  Choncho mfumu inalamula kuti achite zomwezo.+ Pamenepo lamulo linaperekedwa ku Susani, ndipo ana aamuna 10 a Hamani anapachikidwa. 15  Ndiyeno Ayuda amene anali ku Susani anasonkhananso pamodzi pa tsiku la 14+ la mwezi wa Adara, ndipo anapha amuna 300 ku Susani, koma sanafunkhe zinthu zawo.+ 16  Ayuda ena onse amene anali m’zigawo+ za mfumu anasonkhana pamodzi kuti ateteze miyoyo yawo.+ Ndipo anabwezera+ adani awo ndi kupha anthu 75,000 amene anali kudana nawo, koma sanafunkhe zinthu zawo 17  pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Ndiyeno pa tsiku la 14 la mweziwo anapuma ndi kulisandutsa tsiku laphwando+ ndi lachikondwerero.+ 18  Ayuda amene anali ku Susani anasonkhana pamodzi pa tsiku la 13+ ndi la 14 la mweziwo. Ndipo pa tsiku la 15 la mweziwo anapuma ndipo analisandutsa tsiku laphwando ndi lachikondwerero.+ 19  N’chifukwa chake Ayuda akumidzi amene anali kukhala m’madera akutali ndi mzinda, anasandutsa tsiku la 14 la mwezi wa Adara+ kukhala tsiku lachikondwerero,+ laphwando, losangalala ndiponso tsiku+ lotumizirana chakudya.+ 20  Ndiyeno Moredekai+ analemba zochitika zimenezi ndi kutumiza makalata kwa Ayuda onse amene anali m’zigawo zonse+ za Mfumu Ahasiwero, zakutali ndi zapafupi zomwe. 21  M’makalatawo anawalamula kuti pa tsiku la 14 ndi la 15 la mwezi wa Adara azichita+ chikondwerero chimenechi nthawi zonse chaka ndi chaka. 22  Anawalamula kuti masiku amenewa akhale ochita phwando, kusangalala, kutumizirana chakudya+ ndi kupereka mphatso kwa anthu osauka.+ Anatero pakuti amenewa ndi masiku amene Ayuda anasiya kuvutitsidwa ndi adani awo,+ komanso mwezi umene chisoni chawo chinasintha kukhala chikondwerero ndiponso pamene tsiku lolira+ linasintha kukhala tsiku losangalala. 23  Ndipo Ayuda anavomereza kuti masiku amenewa akhale achikondwerero chimene anali atayamba kale kuchita. Anavomereza zimenezo mogwirizananso ndi zimene Moredekai anawalembera. 24  Izi zinali choncho chifukwa Hamani+ mwana wa Hamedata+ Mwagagi,+ amene anali kudana+ ndi Ayuda onse, anakonzera Ayudawo chiwembu kuti awawononge.+ Choncho iye anachita Puri+ kapena kuti Maere,+ ndi cholinga chakuti awasautse ndi kuwawononga. 25  Koma Esitere ataonekera pamaso pa mfumu, mfumuyo inalemba lamulo lakuti:+ “Chiwembu+ chake choipa chimene anakonzera Ayuda chimugwere iyeyo.”+ Choncho Hamani komanso ana ake anawapachika pamtengo.+ 26  N’chifukwa chake masiku amenewa anawatcha kuti Purimu, kutengera dzina la Puri.+ Choncho mogwirizana ndi mawu onse a m’kalata imeneyi+ komanso chifukwa cha zimene anaona pa nkhani imeneyi ndi zimene zinawachitikira, 27  Ayudawo anaika lamulo ndi kuvomereza kuti iwo, ana awo ndi anthu onse odziphatika kwa iwo+ adzatsatira lamuloli. Lamuloli linali lakuti, nthawi zonse azisunga masiku awiri amenewa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa zokhudza masikuwa komanso kuti aziwasunga pa nthawi yoikidwiratu chaka ndi chaka. 28  Anayenera kukumbukira masiku amenewa mu m’badwo uliwonse, banja lililonse, chigawo chilichonse ndi mzinda uliwonse. Ayuda sanayenere kusiya kusunga masiku a Purimu ndipo ana awo sanayenere kusiya kukumbukira masiku amenewa.+ 29  Ndiyeno Mfumukazi Esitere, mwana wamkazi wa Abihaili,+ pamodzi ndi Moredekai Myuda, analemba kalata yachiwiri ndi ulamuliro wonse, kutsimikizira za Purimu. 30  Kenako anatumiza makalata a mawu amtendere ndi odalirika+ kwa Ayuda onse m’zigawo 127+ zimene Ahasiwero+ anali kulamulira. 31  Anatumiza makalatawo kuti atsimikizire kuti pa nthawi yoikidwiratu, Ayuda onse ndi ana awo azichita chikondwerero cha Purimu monga mmene Moredekai Myuda ndi Mfumukazi Esitere anawalamulira.+ Anawakumbutsanso lamulo limene iwo ndi ana awo+ anadziikira kuti adzasala kudya+ komanso kuti adzapemphera kwa Mulungu.+ 32  Choncho zimene Esitere ananena zinatsimikizira nkhani imeneyi ya Purimu+ ndipo zinalembedwa m’buku.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.