Ezara 5:1-17

5  Mneneri Hagai+ ndi mneneri Zekariya+ mdzukulu wa Ido,+ analosera kwa Ayuda amene anali mu Yuda ndi mu Yerusalemu, m’dzina+ la Mulungu wa Isiraeli yemwe anali nawo.+  Panali pa nthawi imeneyi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu. Nyumbayi inali ku Yerusalemu ndipo panali aneneri a Mulungu+ omwe anali kuwathandiza.  Pa nthawi imeneyo Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,*+ Setara-bozenai, ndi anzawo anabwera kwa Ayudawo n’kudzawafunsa kuti: “Kodi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi ndi kumaliza khoma* lamatabwali?”+  Anawafunsanso kuti: “Amuna amene akumanga nyumba imeneyi mayina awo ndani?”  Koma maso+ a Mulungu wawo anali+ pa akulu a Ayuda, ndipo anthu aja sanawasiyitse ntchitoyo. Anadikira mpaka pamene analemba chikalata chokhudza nkhaniyo n’kuchitumiza kwa Dariyo, ndiponso mpaka pamene chikalata choyankha nkhani imeneyi chinabwera.  Izi n’zimene zinali m’kalata+ imene Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,+ Setara-bozenai+ ndi anzake,+ ndiponso abwanamkubwa aang’ono amene anali kutsidya lina la Mtsinje, anatumiza kwa mfumu Dariyo.  Anatumiza mawu kwa iye, ndipo kalatayo anailemba motere: “Kwa Mfumu Dariyo: “Mtendere ukhale nanu.+  Inu mfumu dziwani kuti ife tinapita kuchigawo+ cha Yuda kunyumba ya Mulungu wamkulu.+ Kumeneko takapeza kuti nyumbayo akuimanga ndi miyala yochita kuigubuduzira pamalo ake ndiponso akuika matabwa m’makoma ake. Iwo akugwira ntchitoyo mwakhama ndipo ikupita patsogolo.  Ndiyeno ife tinafunsa akuluakulu amenewo kuti: ‘Kodi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi ndi kumaliza khoma lamatabwali?’+ 10  Tinawafunsanso mayina awo kuti tilembe mayina a atsogoleri awo, n’cholinga choti tikuuzeni kuti muwadziwe.+ 11  “Akuluakuluwo anatiyankha kuti: ‘Ife ndife atumiki a Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi,+ ndipo tikumanganso nyumba imene inamangidwa zaka zambiri zapitazo, imene mfumu yaikulu ya Isiraeli inamanga ndi kuimaliza.+ 12  Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa+ Mulungu wakumwamba, iye anawapereka+ m’manja mwa Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo Mkasidi,+ yemwe anagwetsa nyumbayi+ n’kutengera anthuwo ku ukapolo ku Babulo.+ 13  Komabe m’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Babulo, mfumu Koresi inaika lamulo loti nyumba ya Mulunguyi imangidwenso.+ 14  Komanso, ziwiya zagolide ndi zasiliva+ zimene Nebukadinezara anazitenga m’kachisi wa Mulungu yemwe anali ku Yerusalemu, n’kupita nazo kukachisi wa ku Babulo,+ mfumu Koresi+ inazichotsa m’kachisi wa ku Babuloyo. Ndiyeno zinaperekedwa kwa Sezibazara,+ munthu amene Koresi anamuika kukhala bwanamkubwa.+ 15  Koresiyo anamuuza iye kuti: “Tenga ziwiya izi.+ Pita ukaziike m’kachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo ukaonetsetse kuti nyumba ya Mulungu yamangidwanso pamalo ake.”+ 16  Sezibazarayo atabwera anamanga maziko a nyumba ya Mulungu+ yomwe ili ku Yerusalemu. Kuyambira nthawi imeneyo mpaka pano nyumbayi ikumangidwanso ndipo sinamalizidwe.’+ 17  “Tsopano ngati inu mfumu mukuona kuti n’koyenera, uzani anthu afufuze+ m’nyumba ya chuma cha mfumu imene ili ku Babuloko, kuti aone ngati mfumu Koresi inaikadi lamulo+ loti nyumba ya Mulungu yomwe ili ku Yerusalemu imangidwenso. Inu mfumu mutitumizire chigamulo chanu pankhani imeneyi.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.