Ezara 8:1-36

8  Tsopano nawa mayina a atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ ndi mndandanda wa mayina wotsatira makolo+ a anthu amene anachoka nane ku Babulo, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita:+  Pa ana a Pinihasi+ panali Gerisomu, pa ana a Itamara+ panali Danieli,+ pa ana a Davide+ panali Hatusi.  Panalinso Zekariya kuchokera pa ana a Sekaniya, yemwe anali wochokera pa ana a Parosi.+ Iye anali ndi amuna amene analembetsa mayina awo okwanira 150.  Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Eliho-enai mwana wa Zerahiya. Iye anali ndi amuna 200.  Pa ana a Zatu+ panali Sekaniya mwana wa Yahazieli. Iye anali ndi amuna 300.  Pa ana a Adini+ panali Ebedi mwana wa Yonatani. Iye anali ndi amuna 50.  Pa ana a Elamu+ panali Yesaiya mwana wa Ataliya. Iye anali ndi amuna 70.  Pa ana a Sefatiya+ panali Zebadiya mwana wa Mikayeli. Iye anali ndi amuna 80.  Pa ana a Yowabu panali Obadiya mwana wa Yehiela. Iye anali ndi amuna 218. 10  Pa ana a Bani+ panali Selomiti mwana wa Yosifiya. Iye anali ndi amuna 160. 11  Pa ana a Bebai+ panali Zekariya mwana wa Bebai. Iye anali ndi amuna 28. 12  Pa ana a Azigadi+ panali Yohanani mwana wa Hakatani. Iye anali ndi amuna 110. 13  Anthu ochokera pa ana a Adonikamu+ omwe anali omaliza, mayina awo anali awa: Elifeleti, Yeyeli ndi Semaya. Iwo anali ndi amuna 60. 14  Pa ana a Bigivai+ panali Utai ndi Zabudi. Iwo anali ndi amuna 70. 15  Ndiyeno ndinawasonkhanitsa pamtsinje+ umene umafika ku Ahava+ ndipo tinamanga msasa pamenepo n’kukhalapo masiku atatu kuti ndiwaonetsetse anthuwo+ ndi ansembe,+ koma sindinapezepo ana a Levi.+ 16  Choncho ndinaitanitsa Eliezere, Ariyeli, Semaya, Elinatani, Yaribi, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu. Amenewa anali atsogoleri awo. Ndinaitanitsanso Yoyaribi ndi Elinatani, omwe anali alangizi.+ 17  Kenako ndinawalamula kuti apite kwa Ido yemwe anali mtsogoleri pamalo otchedwa Kasifiya. Ndinawauza mawu+ oti akauze Ido ndi abale ake Anetini+ ku Kasifiyako, kuti atibweretsere atumiki+ a panyumba ya Mulungu wathu. 18  Chotero, popeza dzanja labwino+ la Mulungu wathu linali pa ife, iwo anatibweretsera munthu wanzeru+ wochokera pakati pa ana a Mali+ mdzukulu wa Levi+ mwana wa Isiraeli, dzina lake Serebiya+ pamodzi ndi ana ake ndi abale ake. Onse pamodzi analipo 18. 19  Panalinso Hasabiya, yemwe anali pamodzi ndi Yesaiya wochokera pa ana a Merari,+ abale ake ndi ana awo. Onse pamodzi analipo 20. 20  Kuchokera pa Anetini amene Davide ndi akalonga anawaika kuti azitumikira Alevi, panali Anetini 220. Onsewa anawasankha pochita kuwatchula mayina awo. 21  Kenako ndinalamula kuti tisale kudya tili kumtsinje wa Ahava kuja, kuti tidzichepetse+ pamaso pa Mulungu wathu ndi kumupempha kuti atisonyeze njira yoyenera+ kwa ife, ana athu,+ ndi katundu wathu yense. 22  Ndinatero pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu lankhondo+ ndi okwera pamahatchi+ kuti atithandize kumenyana ndi adani m’njira, chifukwa tinali titauza mfumuyo kuti: “Dzanja+ la Mulungu wathu lili ndi onse om’funafuna kuti awachitire zabwino,+ koma mkwiyo wake+ wamphamvu umayakira onse omusiya.”+ 23  Chotero tinasala kudya+ n’kupempha+ Mulungu wathu zimenezi, moti iye anamva pempho+ lathu. 24  Tsopano ndinapatula anthu 12 kuchokera pa atsogoleri a ansembe. Mayina awo anali Serebiya+ ndi Hasabiya+ pamodzi ndi abale awo 10. 25  Ndiyeno ndinawayezera siliva, golide ndi ziwiya.+ Zimenezi zinali zopereka za kunyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu,+ aphungu ake,+ akalonga ake ndi Aisiraeli onse+ amene anali kumeneko anapereka. 26  Chotero ndinawayezera n’kuwapatsa siliva wokwana matalente* 650, ziwiya 100 zasiliva+ zokwana matalente awiri, golide wokwana matalente 100, 27  mbale 20 zing’onozing’ono zagolide zolowa zokwana madariki* 1,000 ndi ziwiya ziwiri zamkuwa wabwino wonyezimira mofiirira, zamtengo wapatali ngati golide. 28  Kenako ndinawauza kuti: “Inu ndinu oyera+ kwa Yehova. Ziwiyazi+ ndi zopatulika ndipo siliva ndi golideyu ndi nsembe yaufulu yopita kwa Yehova Mulungu wa makolo anu. 29  Khalani maso ndipo khalani atcheru mpaka mukaziyeze+ pamaso pa atsogoleri a ansembe, atsogoleri a Alevi ndi pamaso pa akalonga a makolo a Aisiraeli ku Yerusalemu, m’zipinda zodyera+ za panyumba ya Yehova.” 30  Ansembe ndi Aleviwo analandira siliva ndi golide amene anayezedwayo ndiponso ziwiya zimene zinayezedwazo, kuti apititse zinthuzi ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu.+ 31  Pomalizira pake tinachoka pamtsinje wa Ahava+ pa tsiku la 12 la mwezi woyamba+ kuti tipite ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu wathu linali nafe pa ulendowu moti anatipulumutsa+ m’manja mwa adani ndiponso kwa achifwamba a m’njira. 32  Kenako tinafika ku Yerusalemu+ n’kukhala kumeneko masiku atatu. 33  Pa tsiku lachinayi tinayeza siliva, golide+ ndi ziwiya+ zija m’nyumba ya Mulungu wathu. Titatero tinapereka zinthuzo m’manja mwa wansembe Meremoti+ mwana wa Uliya, yemwe anali limodzi ndi Eleazara mwana wa Pinihasi. Iwowa anali limodzi ndi Yozabadi+ mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binui,+ omwe anali Alevi. 34  Zinthu zonsezo tinaziwerenga n’kuziyeza kenako tinalemba kulemera kwa zinthu zonsezo pa nthawiyo. 35  Anthu amene anabwera kuchokera ku ukapolo,+ amene kale anali m’dziko la eni, anapereka nsembe zopsereza+ kwa Mulungu wa Isiraeli. Anapereka ng’ombe zamphongo 12+ za Aisiraeli onse, nkhosa zamphongo 96,+ ana a nkhosa amphongo 77, ndi mbuzi zamphongo 12+ monga nsembe yamachimo. Zonsezi anazipereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. 36  Kenako tinapereka malamulo+ a mfumu kwa masatarapi*+ a mfumu ndi abwanamkubwa+ a kutsidya lina la Mtsinje.*+ Iwo anathandiza anthuwo+ ndiponso anathandiza panyumba ya Mulungu woona.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
Umenewu ndi udindo wa olamulira akuluakulu a zigawo za dziko.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.