Ezekieli 11:1-25
11 Kenako mzimu+ unandinyamula+ n’kupita nane kuchipata cha kum’mawa cha nyumba ya Yehova chimene chinayang’ana mbali ya kum’mawa.+ Pakhomo la chipatacho ndinaonapo amuna okwanira 25.+ Pakati pawo ndinaonapo Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. Amuna onsewo anali akalonga.+
2 Ndiyeno Mulungu anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, amuna amenewa ndi amene akukonza chiwembu, ndiponso amene akukonza zoipa zokhudza mzindawu.+
3 Iwo akunena kuti: ‘Ino ndiyo nthawi yomanga nyumba.+ Mzindawu uli ngati mphika wakukamwa kwakukulu,+ ndipo ifeyo tili ngati nyama mumphikamo.’
4 “Tsopano iweyo, losera zinthu zowaipira. Losera, iwe mwana wa munthu.”+
5 Kenako mzimu wa Yehova unafika pa ine,+ ndipo iye anandiuza kuti: “Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Inu anthu a nyumba ya Isiraeli, mwanena bwino, ndipo ine ndadziwa maganizo anu.+
6 Inuyo mwapha anthu ambiri mumzindawu komanso mwadzaza misewu yake ndi anthu ophedwa.”’”+
7 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Anthu ophedwa amene mwawaika pakati pa mzindawu ndiwo nyama.+ Mzindawu ndiwo mphika wakukamwa kwakukulu.+ Koma inuyo mudzatulutsidwa mumzindawu.’”+
8 “‘Inu mukuopa lupanga,+ koma ine ndidzakubweretserani lupanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+
9 ‘Ndithu ine ndidzakutulutsani mumzindawu n’kukuperekani m’manja mwa alendo,+ ndipo ndidzakulangani.+
10 Inu mudzaphedwa ndi lupanga.+ Ndidzakuweruzirani m’malire a Isiraeli,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
11 Kwa inu, mzindawu sudzakhala mphika wakukamwa kwakukulu+ ndipo inuyo simudzakhala nyama mkati mwa mphikawo. Ndidzakuweruzirani m’malire a Isiraeli.
12 Inuyo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, chifukwa simunasunge malamulo anga ndiponso simunatsatire zigamulo zanga.+ Koma inu munatsatira zigamulo za anthu a mitundu yokuzungulirani.’”+
13 Nditangomaliza kulosera, Pelatiya mwana wa Benaya anamwalira.+ Choncho ine ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi, n’kufuula+ kuti: “Kalanga ine, inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa!+ Kodi mukufuna kufafaniziratu Aisiraeli otsalawa?”+
14 Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti:
15 “Iwe mwana wa munthu, anthu okhala ku Yerusalemu alankhula kwa abale ako+ enieni,* kwa nyumba yonse ya Isiraeli, ndiponso kwa anthu onse, kuti, ‘Chokani, pitani kutali ndi Yehova. Dzikoli ndi lathu. Laperekedwa kwa ife kuti likhale lathu.’+
16 Tsopano uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ngakhale kuti ndakawaika pakati pa mitundu yakutali yosiyanasiyana ya anthu, ndiponso ndawabalalitsira m’mayiko osiyanasiyana,+ ine ndidzakhala malo opatulika kwa iwo kwa kanthawi kochepa, m’mayiko amene iwo akukhalamo.”’+
17 “Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndidzakusonkhanitsani kuchokera kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso kuchokera m’mayiko amene ndinakubalalitsirani, ndipo ndidzakupatsani dziko la Isiraeli.”+
18 “‘Ndithu iwo adzabwera m’dzikomo, ndipo adzachotsamo mafano onse onyansa ndi zinthu zonse zonyansa.+
19 Ndidzawapatsa mtima umodzi+ ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa iwo.+ Ndidzachotsa mtima wamwala m’matupi awo+ n’kuwapatsa mtima wamnofu,+
20 kuti azidzatsatira malamulo anga, azidzasunga zigamulo zanga ndi kuzikwaniritsa.+ Iwo adzakhaladi anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”’+
21 “‘“Koma amene akuumirira mafano awo onyansa ndi zinthu zawo zonyansa,+ ndidzawabwezera monga mwa njira zawo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”+
22 Tsopano akerubi+ aja anatambasula mapiko awo ndipo mawilo anali pambali pawo.+ Ulemerero+ wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pa mitu yawo.+
23 Kenako, ulemerero wa Yehova+ unakwera m’mwamba kuchoka pakati pa mzindawo, n’kukaima pamwamba pa phiri+ limene lili kum’mawa kwa mzindawo.+
24 Tsopano mzimu+ unandinyamula+ n’kukandisiya kudziko la Kasidi kumene kunali anthu ogwidwa ukapolo.+ Zimenezi zinachitika m’masomphenya amene ndinaona mwa mzimu wa Mulungu. Kenako masomphenya amene ndinaonawa anachoka pa ine.
25 Pambuyo pake, ndinayamba kuuza anthu ogwidwa ukapolowo zinthu zonse za Yehova zimene iye anandionetsa.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “anthu okhudzidwa ndi ufulu wako wowombolanso cholowa chako.”