Ezekieli 26:1-21
26 M’chaka cha 11, pa tsiku loyamba la mwezi, Yehova analankhula nane kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, Turo+ wanena Yerusalemu+ kuti, ‘Eyaa! Zakhala bwino! Mzindawo wathyoledwa.+ Mzinda umene unali kukopa anthu a mitundu ina+ wathyoledwa. Tsopano ine zinthu zindiyendera bwino. Ndilemera chifukwa mzindawo wawonongedwa.’+
3 Pa chifukwa chimenechi, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikuukira iwe Turo ndipo ndikutumizira mitundu yambiri ya anthu+ kuti idzamenyane nawe. Anthuwo adzabwera ngati mafunde a m’nyanja.+
4 Mitunduyo idzagwetsa mpanda wa Turo+ ndi kugumula nsanja zake.+ Ine ndidzapala fumbi lake n’kumusandutsa malo osalala opanda kanthu kalikonse, apathanthwe.
5 Iye adzakhala malo oyanikapo makoka+ pakati pa nyanja.’+
“‘Ine ndanena, anthu a mitundu ina adzalanda zinthu zake,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
6 ‘Anthu a m’midzi yake yozungulira imene ili kunja kwa mzindawo adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+
7 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidzatumiza Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mfumu ya mafumu,+ kuchokera kumpoto+ kuti akaukire Turo. Iye adzapita ndi mahatchi,+ magaleta ankhondo,+ asilikali a pamahatchi, khamu la anthu+ kapena kuti gulu lalikulu la anthu.
8 Anthu okhala m’midzi yozungulira imene ili kunja kwa mzindawu adzawapha ndi lupanga. Iwo adzakumangira mpanda womenyerapo nkhondo ndi chiunda chomenyerapo nkhondo,+ ndipo adzadziteteza ndi chishango chachikulu.
9 Mfumuyo idzagumula mpanda wako ndi chida chogumulira, ndipo idzagwetsa nsanja zako ndi zida zake.
10 Fumbi limene chikhamu cha mahatchi ake chidzachite lidzakufotsera.+ Mpanda wako udzagwedezeka chifukwa cha phokoso la asilikali a pamahatchi ndi mawilo a magaleta ankhondo. Izi zidzachitika iye akamadzalowa m’zipata zako ngati mmene zimakhalira polowa mumzinda umene mpanda wake augumula.
11 Ziboda za mahatchi ake zidzapondaponda m’misewu yako yonse.+ Iye adzapha anthu ako ndi lupanga ndipo zipilala zako zolimba zidzagwa.
12 Iwo adzakulanda chuma chako+ ndi malonda ako.+ Adzagwetsa mpanda wako ndi nyumba zako zosiririka. Miyala yako, zinthu zako zamatabwa ndi fumbi lako, adzaziponya m’madzi.’
13 “‘Ndidzathetsa phokoso la kuimba kwako+ ndipo phokoso la azeze ako silidzamvekanso.+
14 Ndidzakusandutsa malo osalala apathanthwe lopanda kanthu.+ Udzakhala malo oyanikapo makoka.+ Iwe sudzamangidwanso, pakuti ine Yehova ndanena,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+
15 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mzinda wa Turo kuti, ‘Kodi zilumba sizidzagwedezeka chifukwa cha phokoso la kuwonongedwa kwako, kubuula kwa anthu ovulazidwa koopsa, ndi kuphedwa kwa anthu ako ambiri?+
16 Atsogoleri onse a kunyanja adzatsika+ m’mipando yawo yachifumu+ ndi kuvula malaya awo akunja odula manja. Adzavula zovala zawo za nsalu yopeta. Iwo adzavala zovala zonjenjemeretsa. Adzakhala padothi+ ndipo nthawi zonse azidzanjenjemera+ ndi kukuyang’anitsitsa modabwa.
17 Iwo adzakuimbira nyimbo yoimba polira.+ Azidzati:
“‘“Iwe mzinda wotamandika, zoona wawonongekadi! Mwa iwe munali kukhala anthu ochokera kunyanja.+ Unali wamphamvu panyanja.+ Iwe ndi anthu ako munali kuchititsa mantha anthu onse okhala padziko lapansi.
18 Pa tsiku la kuwonongedwa kwako, zilumba zidzanjenjemera. Zilumba za m’nyanja zidzasokonezeka chifukwa cha kuwonongedwa kwako.”’+
19 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndikadzakusandutsa mzinda wabwinja ngati mizinda imene simukukhala anthu, ndikadzakubweretsera madzi ambiri, ndipo madzi ochulukawo akadzakumiza,+
20 ndidzakutsitsira m’dzenje, ngati mmene ndinatsitsira ena onse m’manda momwe muli anthu amene anafa kalekale.+ Ine ndidzakuchititsa kukhala pansi, panthaka.+ Udzakhala kumeneko pamodzi ndi malo ena amene anawonongedwa kalekale ndiponso pamodzi ndi ena onse amene akutsikira kumanda.+ Ndidzachita zimenezi kuti anthu asadzakhalenso mwa iwe, koma m’dziko la anthu amoyo ndidzaikamo zokongoletsera.+
21 “‘Ndidzakugwetsera zoopsa modzidzimutsa+ ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna+ koma sudzapezeka mpaka kalekale,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”