Ezekieli 27:1-36
27 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira+ yokhudza Turo.
3 Uimbire Turo kuti,“‘Iwe amene ukukhala polowera m’nyanja,+ mkazi wochita malonda ndi anthu okhala m’zilumba zambiri,+ tamvera zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena. Iye wanena kuti: “Iwe Turo wanena kuti, ‘Ine ndine chiphadzuwa.’+
4 Madera ako ali mkatikati mwa nyanja.+ Omwe anakupanga anakukongoletsa kwambiri.+
5 Anakupanga ndi matabwa a mtengo wa mlombwa okhaokha ochokera ku Seniri.+ Anatenga mkungudza wa ku Lebanoni+ kuti ukhale mtengo wako womangirirapo chinsalu choyendetsera ngalawa.
6 Zopalasira ngalawa zako anazipanga ndi mitengo ikuluikulu ya ku Basana. Mbali ya kutsogolo kwako anaipanga ndi matabwa a paini, n’kuikongoletsa ndi minyanga yochokera kuzilumba za Kitimu.+
7 Chinsalu chako choyendetsera ngalawa anachipanga ndi nsalu za mitundu yosiyanasiyana zochokera ku Iguputo.+ Pamwamba pako anaphimbapo ndi chinsalu chopangidwa ndi ulusi wabuluu+ komanso ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ wochokera kuzilumba za Elisa.+
8 “‘“Anthu a ku Sidoni+ ndi ku Arivadi+ ndi amene anali kukupalasa. Iwe Turo, anthu ako aluso+ anali mkati mwako monga ogwira ntchito m’chombo.+
9 Amuna achikulire a ku Gebala+ ndi anthu ake aluso anali mkati mwako monga anthu omata molumikizira matabwa ako.+ Zombo zonse zapanyanja ndi oziyendetsa anali mwa iwe kuti muchite malonda ndi kusinthana zinthu.
10 Amuna a ku Perisiya,+ ku Ludi+ ndi ku Puti+ anali m’gulu lako lankhondo, anali m’gulu la asilikali ako. Amuna amenewa anali kupachika zishango ndi zisoti mwa iwe.+ Iwo ndi amene anakuchititsa kukhala waulemerero.
11 Ana aamuna a ku Arivadi+ pamodzi ndi gulu lako lankhondo anali kukhala pamwamba pa mpanda wako kuzungulira mzinda wonse. Pansanja zako panali amuna olimbikira nkhondo. Iwo anapachika zishango zawo zozungulira m’makoma ako kuzungulira mpandawo.+ Amuna amenewa anakuchititsa kuti ukhale chiphadzuwa.
12 “‘“Tarisi+ unali kuchita naye malonda a zinthu zambiri zosiyanasiyana zamtengo wapatali.+ Unamupatsa zinthu zako zimene unasunga posinthanitsa ndi siliva, chitsulo, tini ndi mtovu.+
13 Iwe unali kuchita malonda ndi Yavani,+ Tubala+ ndi Meseke.+ Unali kuwapatsa katundu wako wogulitsa pomusinthanitsa ndi anthu+ komanso zinthu zamkuwa.
14 Unapereka zinthu zako zimene unasunga pozisinthanitsa ndi mahatchi ndi nyulu zochokera kwa ana a Togarima.+
15 Ana a Dedani+ unali kuchita nawo malonda, ndipo unalemba ntchito zilumba zambiri kuti zizikuchitira malonda. Anthu a m’zilumbazo anali kukulipira minyanga+ komanso mitengo ya phingo.
16 Unali kuchita malonda ndi Edomu chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako. Unapereka zinthu zimene unasunga posinthanitsa ndi miyala ya nofeki,+ ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, nsalu zamitundu yosiyanasiyana, nsalu zabwino kwambiri, miyala yamtengo wapatali ya korali ndi ya rube.
17 “‘“Unali kuchita malonda ndi Yuda komanso dziko la Isiraeli. Unapereka zinthu zimene unasunga posinthanitsa+ ndi tirigu+ wa ku Miniti,+ zakudya zapamwamba, uchi,+ mafuta ndi basamu.+
18 “‘“Unali kuchita malonda ndi Damasiko+ pogulitsa katundu wambiri amene unali naye, pakuti unali ndi katundu wambiri wosiyanasiyana. Posinthana katundu, iye anakupatsa vinyo+ wa ku Heliboni ndi ubweya wa nkhosa wotuwa mofiirira.
19 Vedani ndi Yavani akudera la Uzali anakupatsa katundu wawo kuti iwe uwapatse katundu amene unasunga. Iwo anakupatsa ziwiya zachitsulo, mitengo ya kasiya ndi mabango onunkhira+ posinthanitsa ndi katundu wako.
20 Dedani+ unali kuchita naye malonda a nsalu zoika pazishalo za mahatchi.
21 Unalemba ntchito Aluya+ ndi atsogoleri onse a ku Kedara+ kuti azikugulitsira malonda. Iwo anali kukugulitsira ana a nkhosa amphongo, nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo.+
22 Unali kuchita malonda ndi amalonda a ku Sheba+ ndi ku Raama.+ Unali kuwapatsa zinthu zako zimene unasunga, posinthanitsa ndi mtundu ulionse wa mafuta onunkhira abwino kwambiri, mtundu uliwonse wa miyala yamtengo wapatali ndi golide.+
23 Unali kuchita malonda ndi Harana,+ Kane, Edeni,+ amalonda a ku Sheba,+ Ashuri+ ndi Kilimadi.
24 Unali kuchita nawo malonda a zovala zokongola kwambiri, malaya akunja opangidwa ndi nsalu yabuluu komanso nsalu yamitundu yosiyanasiyana. Unalinso kuchita nawo malonda a makapeti okhala ndi mitundu iwiri ndiponso zingwe zopota zolimba kwambiri. Unali kuchita nawo malondawo pamalo ako ochitira malonda.
25 “‘“Zombo za ku Tarisi+ zoyenda m’gulu limodzi zinali kunyamula katundu wako wamalonda. Choncho unalemera ndi kukhala waulemerero kwambiri pakati pa nyanja.+
26 “‘“Anthu okupalasa akupititsa pamadzi ozama.+ Mphepo ya kum’mawa yakuwononga pakatikati pa nyanja.+
27 Zinthu zako zamtengo wapatali, zinthu zimene unasunga,+ katundu wako wamalonda,+ anthu okuyendetsa, anthu ogwira ntchito mwa iwe,+ anthu omata molumikizira matabwa ako,+ anthu ako okugulitsira malonda, amuna ako onse ankhondo+ amene ali mwa iwe ndiponso amene ali pakati pa anthu ako onse, adzamira pakati pa nyanja pa tsiku la kuwonongedwa kwako.+
28 “‘“Chifukwa cha kufuula kwa anthu ogwira ntchito mwa iwe, dziko lonse lidzagwedezeka.+
29 Anthu onse ogwiritsa ntchito zopalasira ngalawa, anthu oyendetsa zombo ndi anthu onse ogwira ntchito m’zombo panyanja, adzatuluka m’zombo zawo n’kukaima pamtunda.+
30 Iwo adzakulirira mofuula ndi mowawidwa mtima.+ Adzadzithira dothi kumutu+ ndi kugubuduzika paphulusa.+
31 Adzadzimeta mpala chifukwa cha iwe+ ndi kuvala ziguduli+ ndipo adzakulirira mowawidwa mtima.+
32 Pokulira adzaimba nyimbo yoimba polira+ yakuti,“‘“‘Ndani angafanane ndi Turo+ amene wawonongedwa pakati pa nyanja?+
33 Zinthu zimene unasunga+ zikafika kumtunda+ zinali kukwanira mitundu yambiri ya anthu.+ Mafumu a padziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zako zochuluka zamtengo wapatali ndi katundu wako wogulitsa.+
34 Tsopano nyanja yakuwononga, ndipo wamira m’madzi ozama.+ Katundu wako wamalonda ndi khamu la anthu+ limene linali mwa iwe zatheratu.
35 Anthu onse okhala m’zilumba+ adzakuyang’anitsitsa modabwa ndipo mafumu awo adzanjenjemera chifukwa cha mantha.+ Nkhope zawo zonse zidzaoneka zankhawa.+
36 Amalonda ochokera pakati pa mitundu ina ya anthu adzakuimbira miluzu.+ Zoopsa zodzidzimutsa zidzakugwera ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.’”’”+