Ezekieli 36:1-38

36  “Koma iwe mwana wa munthu, losera zokhudza mapiri a ku Isiraeli. Unene kuti, ‘Inu mapiri a ku Isiraeli,+ tamverani mawu a Yehova.  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pajatu mdani wanu wakunenani kuti,+ ‘Eyaa! Tatenga ngakhale malo okwezeka akalekale+ kukhala athu!’”’+  “Choncho losera ndipo unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mwakhala bwinja+ ndipo adani anu akulumani kumbali zonse.+ Izi zachitika kuti anthu otsala a mitundu ina akutengeni kuti mukhale awo.+ Anthu akunena za inu ndi pakamwa pawo+ ndipo akukunenerani zoipa.+  Tsopano inu mapiri a ku Isiraeli,+ tamverani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walankhula ndi mapiri, zitunda, mitsinje, zigwa ndi malo owonongedwa amene ndi mabwinja.+ Walankhulanso ndi mizinda yopanda anthu imene anthu otsala a mitundu ina anaitenga kukhala yawo. Anthuwo anakhala moizungulira ndipo amainyoza.+  Mawu amene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena ndi akuti, ‘Ndithudi, ndidzadzudzula anthu otsala a mitundu ina ndiponso Edomu yense nditakwiya kwambiri.+ Ndidzadzudzula amene anatenga dziko langa kuti likhale lawo. Iwo analitenga akusangalala+ komanso kunyoza mumtima mwawo+ poona kuti atenga dzikolo ndi malo ake odyetserako ziweto.’”’+  “Pa chifukwa chimenechi, losera zokhudza dziko la Isiraeli. Lankhula kwa mapiri, zitunda, mitsinje ndi zigwa kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ineyo ndidzalankhula ndili waukali ndiponso nditakwiya chifukwa chakuti mitundu ina ya anthu yakhala ikukunyozani.”’+  “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndalumbira nditakweza dzanja langa+ kuti mitundu imene yakuzungulirani idzakhala yonyozeka.+  Koma inu mapiri a Isiraeli, mudzatulutsa nthambi ndi kubalira zipatso anthu anga Aisiraeli,+ chifukwa chakuti atsala pang’ono kulowa m’dziko lino.+  Ine ndidzatembenukira kwa inu ndi kukuthandizani.+ Inu mapiri a ku Isiraeli, ndithu anthu adzalima minda mwa inu ndi kubzala mbewu.+ 10  Ndidzachulukitsa anthu mwa inu. Ndidzachulukitsa nyumba yonse ya Isiraeli.+ M’mizinda mudzakhala anthu+ ndipo malo owonongeka adzamangidwanso.+ 11  Inde, ndidzachulukitsa anthu ndi nyama+ ndipo adzachulukana ndi kuberekana kwambiri. Ndidzachititsa kuti anthu akhale mwa inu monga momwe zinalili poyamba+ ndipo ndidzakuchitirani zabwino zambiri kuposa poyamba.+ Choncho inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 12  Ndidzachititsa kuti anthu anga Aisiraeli azidzayendayenda mwa inu, ndipo adzakutengani kukhala awo.+ Inu mudzakhala cholowa chawo+ ndipo simudzawapheranso ana.’”+ 13  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Anthu akukunenani kuti: “Inu ndinu odya anthu ndipo mwakhala dziko lopha ana a mitundu ya anthu okhala mwa inu.”’+ 14  ‘Pa chifukwa chimenechi inu simudzadyanso anthu+ ndipo simudzaphanso ana a mitundu ya anthu okhala mwa inu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 15  ‘Ndidzathetsa nkhani zonyoza zimene anthu a mitundu ina amakunenerani.+ Mitundu ya anthu sidzakunyozaninso+ ndipo simudzakhumudwitsanso mitundu ya anthu okhala mwa inu,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 16  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 17  “Iwe mwana wa munthu, pamene a nyumba ya Isiraeli anali kukhala m’dziko lawo, anali kudetsa dzikolo ndi njira zawo komanso zochita zawo.+ Pamaso panga, njira zawo zakhala ngati zonyansa za mkazi amene akusamba.+ 18  Pamenepo ndinawatsanulira mkwiyo wanga chifukwa cha magazi amene iwo anakhetsa m’dziko+ limenenso analidetsa ndi mafano awo onyansa.+ 19  Choncho ndinawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu, moti anamwazikira m’mayiko osiyanasiyana.+ Ndinawaweruza mogwirizana ndi njira zawo komanso zochita zawo.+ 20  Pamenepo iwo anapita kwa anthu a mitundu ina ndipo anthuwo anayamba kudetsa dzina langa loyera+ ponena za iwowo kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, ndipo anachoka m’dziko lake.’+ 21  Ndidzamva chisoni chifukwa cha dzina langa loyera limene nyumba ya Isiraeli yalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene iwo anapita.”+ 22  “Chotero uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo a nyumba ya Isiraeli, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mwalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapita.”’+ 23  ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu+ limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndikadzayeretsedwa pakati panu, pamaso pa anthu a mitundu inawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 24  ‘Ndidzakutengani pakati pa anthu a mitundu ina n’kukusonkhanitsani pamodzi kuchokera m’mayiko onse. Kenako ndidzakubweretsani m’dziko lanu.+ 25  Ine ndidzakuwazani madzi oyera ndipo mudzakhala oyera. Ndidzakuyeretsani+ pokuchotserani zonyansa zanu zonse+ ndi mafano anu onse onyansa.+ 26  Ndidzakupatsani mtima watsopano,+ ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa inu.+ Ndidzakuchotserani mtima wanu wamwala n’kukupatsani mtima wamnofu.+ 27  Ndidzaika mzimu wanga mwa inu,+ ndipo ndidzakuchititsani kuyenda motsatira malamulo anga.+ Mudzasunga zigamulo zanga ndi kuzitsatira.+ 28  Inu mudzakhala m’dziko limene ndinapatsa makolo anu.+ Mudzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.’+ 29  “‘Ndidzakupulumutsani ku zinthu zanu zonse zodetsa,+ ndipo ndidzauza mbewu kuti zibereke kwambiri moti sindidzabweretsanso njala pakati panu.+ 30  Ndidzachulukitsa zipatso za mtengo ndi zokolola zakumunda kuti musadzanyozekenso chifukwa cha njala pakati pa mitundu ina ya anthu.+ 31  Choncho mudzakumbukira njira zanu zoipa ndi zochita zanu zimene sizinali zabwino.+ Mudzanyansidwa ndi zochita zanu, zolakwa zanu ndi zinthu zonyansa zimene munachita.+ 32  Dziwani kuti ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Inu a nyumba ya Isiraeli, chitani manyazi ndi kuona kuti mwanyozeka chifukwa cha njira zanu.’+ 33  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limene ndidzakuyeretseni kuchotsa zolakwa zanu zonse, ndidzachititsanso kuti m’mizinda yanu mukhale anthu+ ndipo malo owonongeka adzamangidwanso.+ 34  Anthu adzalima m’dziko limene linali lowonongedwa. Adzalima m’dziko limene aliyense wodutsa ankaliona kuti ndi bwinja.+ 35  Anthu adzanena kuti: “Dziko ilo limene linali bwinja tsopano lakhala ngati munda wa Edeni.+ Mizinda imene inawonongedwa ija, imene inali mabwinja ndiponso imene nyumba zake zinagwetsedwa, tsopano ili ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo mukukhala anthu.”+ 36  Anthu a mitundu ina okuzungulirani amene adzatsale, adzadziwa kuti ine Yehova, ndamanga zinthu zimene zinagwetsedwa.+ Adzadziwa kuti ndabzala mitengo m’dziko limene linali bwinja. Ine Yehova ndanena zimenezi ndipo ndazichita.’+ 37  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidzalola kuti a nyumba ya Isiraeli andipemphe zoti ndiwachitire,+ ndipo ndidzachulukitsa anthu awo ngati gulu la nkhosa.+ 38  Mizinda imene inali mabwinja idzadzaza anthu ochuluka ngati khamu la oyera,+ ndiponso ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa nthawi za zikondwerero,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi