Ezekieli 4:1-17

4  “Iwe mwana wa munthu, tenga njerwa ndipo uiike pamaso pako. Panjerwapo ujambulepo mzinda wa Yerusalemu.+  Uchite nkhondo ndi mzindawo+ ndipo umange mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo.+ Umangenso chiunda chomenyerapo nkhondo*+ ndi misasa yokhalamo asilikali ankhondo. Uikenso zida zankhondo zowonongera mzindawo kuzungulira mzinda wonsewo.+  Utenge chiwaya kuti chikhale ngati khoma lachitsulo pakati pa iweyo ndi mzindawo. Uziyang’anitsitsa mzindawo ndipo usonyeze zimene adani adzachite poukira mzindawo. Chimenechi chikhale chizindikiro kwa nyumba ya Isiraeli.+  “Iweyo ugonere kumanzere kwako ndipo ugonere zolakwa za nyumba ya Isiraeli.+ Kwa masiku amene udzagonere kumanzereko, udzanyamula zolakwa zawo.  Ine ndidzakupatsa zaka zimene iwo akhala akundilakwira+ zokwanira masiku 390,+ ndipo iweyo udzanyamula zolakwa za nyumba ya Isiraeli.  Udzakwanitse masiku onsewo. “Kenako udzagonere mbali ya kumanja kwako, ndipo udzanyamule zolakwa za nyumba ya Yuda kwa masiku 40.+ Tsiku limodzi limene ndakupatsa likuimira chaka chimodzi. Tsiku limodzi kuimira chaka chimodzi.+  Nkhope yako izidzayang’anitsitsa Yerusalemu atazunguliridwa ndi asilikali.+ Udzapinde malaya ako kuti dzanja lako lidzakhale pamtunda, ndipo udzalosere zinthu zoipira mzindawo.  “Ine ndidzakumanga ndi zingwe+ kuti usatembenukire kumbali ina, mpaka utamaliza masiku ako ozungulira mzindawo.  “Tenga tirigu,+ balere, nyemba zikuluzikulu,+ mphodza,+ mapira, ndi tirigu wamtundu wina.*+ Zonsezo uziike mumphika umodzi kuti zikhale chakudya chako cha masiku amene udzakhale ukugonera mbali imodzi. Udzadye chakudya chimenechi kwa masiku 390.+ 10  Uzidzadya chakudya chochita kuyeza. Tsiku lililonse uzidzadya chokwana masekeli* 20.+ Uzidzadya chakudyachi mwa apo ndi apo. 11  “Uzidzamwa madzi ochita kuyeza, okwanira gawo limodzi la magawo 6 a muyezo wa hini.* Tsiku lililonse, uzidzamwa madziwa nthawi ndi nthawi. 12  “Uzidzadya chakudyacho ngati mkate wozungulira wa balere+ ndipo uzidzachiphika pa tudzi+ touma ta anthu, iwo akuona.” 13  Yehova anapitiriza kunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ana a Isiraeli azidzadya chakudya chodetsedwa+ pakati pa mitundu yosiyanasiyana imene ndidzawathamangitsireko.”+ 14  Kenako ine ndinati: “Chonde Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindine woipitsidwa.+ Sindinadyepo nyama yopezeka itafa kapena nyama yochita kukhadzulidwa ndi chilombo kuyambira ndili mwana+ mpaka panopo, ndipo m’kamwa mwanga simunalowepo nyama yodetsedwa.”+ 15  Choncho iye anandiuza kuti: “Chabwino, ndikupatsa ndowe za ng’ombe m’malo mwa tudzi touma ta anthu kuti uphikirepo chakudya chako.” 16  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola ndodo mu Yerusalemu. Ndidzathyola ndodo zimene amakolowekapo mikate yozungulira yoboola pakati.+ Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo adzachidya ali ndi nkhawa.+ Iwo adzamwa madzi ochita kuyeza ali ndi mantha,+ 17  mwakuti chakudya ndi madzi zidzakhala zosowa. Azidzayang’anizana modabwa ndipo adzaonda chifukwa cha zolakwa zawo.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu amene tawamasulira kuti “tirigu wamtundu wina” akutanthauza mtundu wa tirigu wosakoma kwenikweni umene unali kulimidwa ku Iguputo kale.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.