Ezekieli 41:1-26
41 Ndiyeno munthu uja ananditengera m’kachisi.* Mmenemo anayamba kuyeza zipilala zam’mbali. Chipilala china chinali mbali ya kumanzere ndipo china mbali ya kudzanja lamanja. Chipilala chilichonse chinali mikono 6 m’lifupi. Umenewu ndiwo unali muyezo wa chipilala chilichonse m’lifupi mwake.
2 Khomo lolowera m’chipinda chakunja linali lalikulu mikono 10, ndipo kuchokera pakhomolo kukafika pakona panali khoma la mikono isanu mbali iyi, ndi mikono isanu mbali inayo. Anayezanso m’litali mwa chipinda chakunja ndipo chinali mikono 40, m’lifupi mwake chinali mikono 20.
3 Kenako analowa m’chipinda chamkati n’kuyamba kuyeza chipilala cham’mbali cha pakhomo ndipo anapeza kuti kuchindikala kwake chinali mikono iwiri. Anayezanso kukula kwa khomo ndipo anapeza kuti linali mikono 6. Kuchokera pakhomo kukafika pakona panali mikono 7.
4 Ndiyeno anayeza makoma a chipinda chamkati kumbuyo kwa kachisi, ndipo anapeza kuti anali mikono 20 m’litali ndi mikono 20 m’lifupi.+ Kenako anandiuza kuti: “Amenewa ndi Malo Oyera Koposa.”+
5 Anayezanso kuchindikala kwa khoma la nyumbayo ndipo anapeza kuti linali mikono 6. M’lifupi mwa chipinda cham’mbali munali mikono inayi. Umu ndi mmene zinalili kuzungulira nyumba yonseyo.+
6 M’mbali mwa nyumbayo munali mizere itatu ya zipinda zosanjikizana. Mzere uliwonse unali ndi zipinda 30. Zipinda zam’mbali kuzungulira nyumbayo zinali kulowa ku khoma la nyumbayo kuti zikhale ndi chozichirikiza. Koma sizinachirikizike ndi khoma la nyumbayo.+
7 Zipinda za mzere wachiwiri zinali zokulirapo m’mbali kuposa za mzere woyamba, ndipo zipinda za mzere wachitatu zinali zokulirapo m’mbali kuposa za mzere wachiwiri. Panali masitepe oyenda chozungulira opitira m’zipinda zam’mwamba.+ Choncho zipinda za mzere wachitatu zinali zokulirapo kuposa zipinda za mzere wachiwiri, ndipo zipinda za mzere wachiwiri zinali zokulirapo kuposa za mzere woyamba. Munthu akafuna kupita kuzipinda zam’mwamba kuchokera kuzipinda zapansi+ anali kudutsa m’zipinda zapakati.
8 Ndinaona kuti nyumba yonseyo anaimanga pamaziko aatali omwe anachita khonde kuzungulira nyumbayo. Kutalika kwa maziko a zipinda zam’mbali kunali bango lathunthu, lalitali mikono 6 kuchokera pansi kukafika polumikizira.+
9 Khoma lakunja la chipinda cham’mbali linali lochindikala mikono isanu. Pomanga zipinda zam’mbali za nyumbayo, anasiya mpata m’mphepete mwa nyumbayo.
10 Kuchokera pazipinda zodyera+ kukafika pamaziko a nyumbayo panali mikono 20 kumbali zonse za nyumbayo.
11 Makomo a zipinda zam’mbali analoza kumpata wa m’mphepete mwa nyumbayo. Khomo limodzi linayang’ana kumpoto lina linayang’ana kum’mwera. Mpata wa m’mphepete mwa nyumbayo unali mikono isanu m’lifupi, kumbali zonse za nyumbayo.
12 Kumadzulo kwa nyumbayo kunalinso nyumba ina. Nyumba imeneyo inali mikono 70 m’lifupi mwake. Khoma lonse la nyumbayo linali lochindikala mikono isanu, ndipo m’litali mwake linali mikono 90. Pakati pa nyumba ziwirizi panali mpata waukulu.
13 Munthu uja anayeza kachisi n’kupeza kuti anali mikono 100 m’litali mwake. Anayezanso mpata waukulu umene unali mbali zonse za kachisiyo, nyumba imene inali kumadzulo kwake ndi makoma ake, ndipo zonse pamodzi zinali mikono 100 m’litali.
14 Kenako anayeza kumaso kwa kachisi m’lifupi mwake limodzi ndi mpata waukulu wa mbali ya kum’mawa kwa kachisiyo, ndipo anapeza kuti zinali mikono 100.
15 Munthu uja anayezanso m’litali mwa nyumba ya kumadzulo ija imene inayang’anizana ndi mpata waukulu. Anayeza timakonde take mbali iyi ndi mbali inayo n’kupeza kuti nyumbayo ndi timakondeto zinali mikono 100.
Anayezanso kachisi, malo ake amkati+ ndi makonde oyang’ana kubwalo.
16 Malo atatu onsewa anali ndi mawindo a mafelemu aakulu mkati koma aang’ono kunja.+ Analinso ndi timakonde ndiponso malo a pakhomo. M’makoma onse a kutsogolo kwa malo a pakhomo anakhomamo matabwa+ kuchokera pansi kufika m’mawindo, ndipo mawindowo anali otchinga.
17 Chilichonse panyumbayo chinali ndi muyezo wake. Izi zinali choncho kuyambira pamwamba pa khomo, mkati ndi kunja kwa nyumbayo, khoma lonse kuzungulira mkati mwa nyumbayo ndiponso kunja kwake.
18 Ngakhalenso zithunzi zojambula mochita kugoba za akerubi+ ndi za mitengo ya kanjedza,+ zinali ndi miyezo yake. Mitengoyo inali pakati pa kerubi ndi kerubi mnzake, ndipo akerubiwo anali ndi nkhope ziwiriziwiri.+
19 Nkhope ya munthu inayang’ana chithunzi cha mtengo wa kanjedza kumbali iyi ndipo nkhope ya mkango wamphamvu inayang’ana mtengo wa kanjedza kumbali inayo.+ Zithunzi zimenezi zinali zojambula pakhoma mochita kugoba ndipo zinajambulidwa kuzungulira m’nyumba monsemo.
20 Pakhoma la kachisiyo, kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo, anajambulapo mochita kugoba zithunzi za akerubi ndi za mitengo ya kanjedza.
21 Felemu la pakhomo la kachisi linali lofanana mbali zonse,+ ndipo kutsogolo kwa malo oyera kunali kuoneka motere:
22 Kunali guwa lansembe lamatabwa lalitali mikono itatu kuchokera pansi kufika pamwamba. M’litali mwake munali mikono iwiri ndipo m’makona ake munali mwa matabwa.+ M’litali mwa guwalo ndi m’mbali mwake munali mwa matabwa. Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Ili ndi tebulo limene lili pamaso pa Yehova.”+
23 Pakhomo la kachisi komanso la malo oyera panali zitseko ziwiri.+
24 Pakhomo lililonse panali zitseko ziwiri. Zitseko zonsezo zinali zotheka kuzitsegula. Khomo limodzi linali ndi zitseko ziwiri ndipo khomo linalo linalinso ndi zitseko ziwiri.
25 Pazitseko za kachisi anajambulapo zithunzi za akerubi ndi za mitengo ya kanjedza mochita kugoba.+ Zithunzi zimenezi zinali zofanana ndi zimene anajambula m’makoma. Kutsogolo kwa denga la khonde anakhomako mzere wa matabwa otulukira kunja.
26 M’mbali mwa khoma la pakhonde, m’zipinda zam’mbali za nyumbayo ndi pamzere wa matabwawo, munali mawindo a mafelemu aakulu mkati koma aang’ono kunja,+ ndipo anajambulamo zithunzi za mtengo wa kanjedza mbali zonse. Zithunzizi anazijambula mochita kugoba.
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti mawu akuti “kachisi” akutanthauza “Malo Oyera.”