Ezekieli 43:1-27

43  Kenako munthu uja ananditengera kuchipata chimene chinayang’ana kum’mawa.+  Kumeneko ndinaona ulemerero+ wa Mulungu wa Isiraeli ukubwera kuchokera kumbali ya kum’mawa.+ Mawu ake anali kumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri,+ ndipo dziko lapansi linawala chifukwa cha ulemerero wake.+  Zimene ndinaonazo zinali zofanana ndi zimene ndinaona m’masomphenya ena.+ Zinali zofanana ndi masomphenya amene ndinaona pamene ndinapita kukawononga mzinda.*+ Ndinaona zinthu zofanana ndi zimene ndinaona m’mphepete mwa mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.  Ndiyeno ulemerero+ wa Yehova unalowa m’Nyumbayo kudzera pachipata choyang’ana kum’mawa.+  Kenako mzimu unandidzutsa+ m’kupita nane kubwalo lamkati. Kumeneko ndinangoona kuti ulemerero wa Yehova wadzaza m’Nyumba ija.+  Tsopano ndinayamba kumva wina akulankhula nane kuchokera m’Nyumbamo.+ Apa n’kuti munthu uja ataima pambali panga.+  Pamenepo Mulungu anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, malo awa ndi malo a mpando wanga wachifumu+ ndiponso poikapo mapazi anga.+ Ndidzakhala pamalo amenewa, pakati pa ana a Isiraeli mpaka kalekale.+ A nyumba ya Isiraeli ndi mafumu awo+ sadzaipitsanso dzina langa loyera+ ndi dama lawo komanso ndi mitembo+ ya mafumu awo.*  Sadzaipitsanso dzina langa poika khomo lawo pafupi ndi khomo langa. Sadzaikanso felemu la khomo lawo pafupi ndi felemu la khomo langa moti pakati pa iwowo ndi ine n’kungokhala khoma lokha lotisiyanitsa.+ Iwo anaipitsa dzina langa loyera ndi zinthu zawo zonyansa zimene anali kuchita+ moti ndinawafafaniza nditakwiya.+  Tsopano aleke dama+ lawo ndi kuchotsa mitembo ya mafumu awo n’kukaiika kutali ndi ine.+ Akatero ine ndidzakhala pakati pawo mpaka kalekale.+ 10  “Koma iwe mwana wa munthu, uza nyumba ya Isiraeli za Nyumba+ ino kuti achite manyazi chifukwa cha zolakwa zawo,+ ndipo adzayeze nyumbayi ndi kudziwa tsatanetsatane wa kamangidwe kake. 11  Iwo akachita manyazi chifukwa cha zonse zimene anachita, ujambule chithunzi cha kamangidwe ka Nyumbayi+ iwo akuona. Usonyeze maonekedwe ake, makomo ake olowera ndi otulukira, zithunzi za kamangidwe kake ndi miyezo yake yonse. Uwadziwitse malamulo ake onse kuti aone kamangidwe ka nyumbayi ndi miyezo yake yonse kuti azizitsatira.+ 12  Lamulo lokhudza Nyumbayi ndi ili: Malo onse a pamwamba pa phiri kuzungulira nyumbayi ndi oyera koposa.+ Limeneli ndi lamulo lokhudza Nyumbayi. 13  “Nayi miyezo ya guwa lansembe loyezedwa pogwiritsa ntchito muyezo wa mkono+ ndi chikhato.+ Miyezo ya chigawo chapansi cha guwa lansembe inali motere: Kuchokera pansi kufika pamwamba, chinali mkono umodzi. Chigawo chimenechi chinali chokulirapo m’mbali ndi mkono umodzi kuposa cha pamwamba pake. M’mphepete mwa chigawo chimenechi munali kakhoma kakatali chikhatho* chimodzi. 14  Chigawo chachiwiri chimene chinali pamwamba pa chigawo choyambacho chinali chachitali mikono iwiri. Chigawo chimenechi chinali chokulirapo m’mbali ndi mkono umodzi kuposa chimene chinali pamwamba pake. Chigawo chachitatu chinali chachitali mikono inayi. Chigawo chimenechi chinali chokulirapo m’mbali ndi mkono umodzi kuposa chimene chinali pamwamba pake. 15  Malo osonkhapo moto anali pachigawo cha pamwamba penipeni pa guwalo. Chigawo chimenechi chinali chachitali mikono inayi. M’mbali mwa malo osonkhapo motowo munali nyanga zinayi.+ 16  Chigawo cha malo osonkhapo motocho chinali chofanana mbali zonse zinayi.+ M’litali mwake chinali mikono 12 ndipo m’lifupi mwake chinalinso mikono 12.+ 17  Chigawo chachitatu chinali mikono 14 m’litali ndiponso mikono 14 m’lifupi mbali zonse zinayi. Kakhoma ka m’mphepete mwake kanali kakatali hafu ya mkono, ndipo pansi pake kanali mkono umodzi kuzungulira chigawo chonsecho. “Guwalo linali ndi masitepe oyang’ana mbali ya kum’mawa.” 18  Munthu uja anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti, ‘Amenewa ndi malamulo a guwa lansembe amene anaperekedwa pa nthawi imene analipanga. Guwali analipanga kuti aziperekerapo nsembe zopsereza zathunthu+ ndi kuwazapo magazi.’+ 19  “‘Ansembe achilevi+ omwe ndi ana a Zadoki,+ amene amayandikira kwa ine ndi kunditumikira,+ uwapatse ng’ombe yaing’ono yamphongo kuchokera pagulu la ziweto kuti ikhale nsembe yamachimo.’+ Watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 20  ‘Utengeko magazi akewo n’kuwapaka panyanga zinayi za guwa lansembe ndi m’makona anayi a chigawo chachitatu cha guwalo. Magaziwo uwapakenso pakakhoma konse kozungulira chigawo chachitatucho. Uchite zimenezi kuti uyeretse guwa lansembelo ku machimo+ ndipo uliperekere nsembe yophimba machimo.+ 21  Kenako utenge ng’ombe yaing’ono yamphongo ya nsembe yamachimo. Ndiyeno wina akapsereze ng’ombeyo pamalo opserezera a pa Nyumbayo, kunja kwa malo opatulika.+ 22  Pa tsiku lachiwiri, udzabweretse mbuzi yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yamachimo. Ansembewo adzayeretse guwa lansembelo ku machimo monga mmene analiyeretsera ku machimo popereka ng’ombe yaing’ono yamphongo.’ 23  “‘Pomaliza mwambo woyeretsa guwalo ku machimo, udzatenge ng’ombe yaing’ono yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema pagulu la ziweto n’kuzibweretsa kuno. 24  Udzazibweretse pamaso pa Yehova ndipo ansembe adzaziwaze mchere n’kuzipereka+ kwa Yehova monga nsembe yopsereza yathunthu. 25  Kwa masiku 7 uzipereka mbuzi yamphongo monga nsembe yamachimo tsiku lililonse.+ Ansembe azipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo ndi nkhosa yamphongo. Nyama zimenezi zizichokera pagulu la ziweto ndipo zizikhala zopanda chilema. 26  Kwa masiku 7, aphimbe machimo+ a guwalo ndipo aliyeretse ndi kuyamba kuligwiritsa ntchito. 27  Masiku 7 amenewo akatha, kuyambira pa tsiku la 8+ kupita m’tsogolo, ansembe azidzakuperekerani nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zachiyanjano paguwali, ndipo ine ndidzasangalala nanu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti anachita zimenezi mwa kulosera kuti mzindawo udzawonongedwa.
Mawu ake enieni, “mitembo ya mafumu awo pa imfa yawo.”
Umenewu ndi utali wofanana ndi utali wochokera pansonga ya chala chamanthu cha dzanja lanu kukafika pansonga ya chala chaching’ono, mutatambasula chikhatho. Utali umenewu ndi wokwana masentimita 22.2.