Ezekieli 5:1-17
5 “Iwe mwana wa munthu, tenga lupanga lakuthwa. Likhale ngati lezala lako lometela ndipo umetele tsitsi lako ndi ndevu zako.+ Kenako utenge sikelo yoyezera ndipo ugawe tsitsilo m’magawo atatu.
2 Gawo limodzi la magawo atatu a tsitsilo ulitenthe pamoto pakati pa mzindawo masiku ozungulira mzindawo akatha.+ Kenako utenge gawo lina la magawo atatuwo. Gawo limeneli uzilimenya ndi lupanga ukuzungulira mzinda wonsewo.+ Gawo lomaliza la magawo atatuwo uliuluze ndi mphepo ndipo ine ndidzalitsatira nditasolola lupanga.+
3 “Pagawo lachitatuli utengepo tsitsi lochepa n’kulikulunga m’zovala zako.+
4 Utengeponso tsitsi lina n’kuliponya pamoto kuti linyeke. Kuchokera pamoto umenewu, padzabuka moto umene udzafalikire kunyumba yonse ya Isiraeli.+
5 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa mitundu ya anthu ndipo wazunguliridwa ndi mayiko ena.
6 Iye anapandukira zigamulo zanga pochita zoipa zoposa za mitundu ya anthuwo.+ Anapandukiranso malamulo anga kuposa mayiko amene amuzungulira, pakuti iye anakana zigamulo zanga ndipo sanayende m’malamulo anga.’+
7 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti anthu inu munali ovuta+ kuposa mitundu imene yakuzungulirani, ndipo simunayende m’malamulo anga, komanso simunatsatire zigamulo zanga,+ koma munatsatira zigamulo za mitundu imene yakuzungulirani,+
8 izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena: “Ine ndithana nawe mzinda iwe,+ ndipo ndidzapereka zigamulo pakati pako pamaso pa mitundu ya anthu.+
9 Chifukwa cha zonyansa zako zonse, ndidzakuchita zimene sindinachitepo ndiponso zimene sindidzachitanso.+
10 “‘“Choncho pakati pako, abambo adzadya ana awo+ ndipo ana adzadya abambo awo. Ine ndidzakulanga ndipo anthu ako onse otsala ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi.”’+
11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa+ ndi zinthu zako zonse zonyansa,+ ndithu ineyo ndidzakuchepetsa.+ Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo.+
12 Gawo limodzi la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzafa ndi mliri+ ndipo adzatha ndi njala pakati pako.+ Gawo lina la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzaphedwa ndi lupanga mokuzungulira. Gawo lomaliza la magawo atatu a anthu a mtundu wako ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi,+ ndipo ndidzawatsatira nditasolola lupanga.+
13 Ndiyeno mkwiyo wanga udzatha+ ndipo ukali wanga ndidzauthetsera pa iwo.+ Kenako mtima wanga udzakhala pansi.+ Ndikadzathetsera ukali wanga pa iwo, pamenepo iwo adzadziwa kuti ine Yehova ndalankhula chifukwa ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha basi.+
14 “‘Iweyo ndidzakusandutsa malo abwinja. Ndidzakusandutsanso chitonzo pakati pa mitundu yokuzungulira ndi pamaso pa munthu aliyense wodutsa.+
15 Udzakhala chitonzo+ ndi chinthu chochilankhulira mawu onyoza.+ Udzakhalanso chenjezo+ ndi choopsezera mitundu yokuzungulira ndikadzakuweruza mokwiya komanso mwaukali, ndiponso ndikadzakulanga mokwiya.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.
16 “‘Ndikadzakutumizirani mivi yakupha yobweretsa njala+ imene idzakuwonongeni,+ ndidzachititsa kuti njala ikule pakati panu, ndipo ndidzathyola ndodo zimene mumakolowekapo mikate yozungulira yoboola pakati.+
17 Ndidzakutumizirani njala ndi zilombo zakupha+ ndipo zidzakupherani ana anu. Mliri+ ndi magazi+ zidzadutsa pakati panu ndipo ine ndidzakubweretserani lupanga.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.’”