Ezekieli 8:1-18

8  M’chaka cha 6, m’mwezi wa 6, pa tsiku lachisanu la mweziwo, ndinali nditakhala m’nyumba mwanga ndipo akuluakulu a Yuda anali atakhala pamaso panga.+ Pamenepo, dzanja la Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, linafika pa ine.+  Ndinayamba kuona masomphenya ndipo ndinaona winawake wooneka ngati moto.+ Kuchokera pa chimene chinali kuoneka ngati chiuno chake kupita m’munsi, panali moto.+ Kuchokera m’chiuno mwake kupita m’mwamba, panali chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide.+  Kenako iye anatambasula chinachake chooneka ngati dzanja+ ndipo anagwira tsitsi la kumutu kwanga n’kundinyamula. Ndiyeno mzimu+ unandinyamulira m’malere, pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, n’kundipititsa ku Yerusalemu m’masomphenya a Mulungu.+ Unandifikitsa pakhomo la kanyumba ka pachipata cha bwalo lamkati+ choyang’ana kumpoto. Pamenepo m’pamene panali kukhala chizindikiro choimira nsanje, chimene chinali kuchititsa Mulungu nsanje.+  Kumeneko ndinaonako ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli,+ wofanana ndi zimene ndinaona kuchigwa zija.  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, takweza maso ako uyang’ane kumpoto.” Chotero ndinakweza maso anga n’kuyang’ana kumpoto, ndipo ndinaona kuti kumpoto kwa chipata cha guwa lansembe kunali chizindikiro choimira nsanje+ pakhomo la chipatalo.  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zinthu zonyansa kwambiri zimene anthuwa akuchita?+ Ukuona kodi zinthu zimene anthu a nyumba ya Isiraeli akundichitira kunoko kuti nditalikirane ndi malo anga opatulika?+ Koma uonanso zinthu zina zonyansa kwambiri.”  Kenako anandipititsa pakhomo lolowera m’bwalo lamkati, ndipo ndinaona kuti pakhoma* panali chibowo.  Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, taboola khomalo.”+ Ine ndinabooladi khomalo ndipo ndinangoona kuti panalinso khomo lina.  Kenako iye anandiuza kuti: “Lowa uone zinthu zoipa ndi zonyansa zimene anthu akuchita kuno.”+ 10  Chotero ine ndinalowa, ndipo ndinaona kuti pamakoma anajambulapo zithunzi+ za nyama iliyonse yokwawa, za chilombo chilichonse chonyansa+ ndi za mafano onse onyansa a nyumba ya Isiraeli.+ Pamakoma onse anajambulapo zithunzizo mochita kugoba. 11  Ndinaonanso akuluakulu 70+ a nyumba ya Isiraeli ataimirira. Yaazaniya mwana wa Safani+ anali ataima pakati pawo. Iwo anaima pamaso pa zojambulazo, aliyense atanyamula chiwaya chofukizira nsembe m’manja mwake. Utsi wonunkhira wa zofukizazo unali kukwera m’mwamba.+ 12  Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mu mdima?+ Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita m’chipinda chamkati mmene muli fano lake losema? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona.+ Yehova wachokamo m’dziko muno.’” 13  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Uonanso zinthu zina zonyansa kwambiri zimene iwo akuchita.”+ 14  Chotero anandipititsa pakhomo la pachipata cha nyumba ya Yehova chimene chili mbali ya kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona amayi atakhala pansi akulirira mulungu wotchedwa Tamuzi. 15  Iye anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimenezi? Uonanso zinthu zina zonyansa kwambiri+ kuposa zimenezi.” 16  Chotero anandipititsa kubwalo lamkati la nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno ndinaona kuti pakhomo lolowera m’kachisi wa Yehova, pakati pa khonde ndi guwa lansembe,+ panali amuna pafupifupi 25+ atafulatira kachisi wa Yehova.+ Nkhope zawo anali atazilozetsa kum’mawa ndipo anali kugwadira dzuwa atayang’ana kum’mawa.+ 17  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi? Kodi a nyumba ya Yuda akuona ngati ndi chinthu chaching’ono kuchita zinthu zonyansa zimene akuchita panozi? Kodi akufunanso kuti adzaze dzikoli ndi chiwawa+ n’kundikwiyitsa kachiwiri? Kodi waonanso kuti iwowo akulozetsa nthambi* kumphuno kwanga? 18  Choncho ineyo ndidzachitapo kanthu mwaukali.+ Diso langa silidzawamvera chisoni ndipo sindidzawachitira chifundo.+ Iwo adzandiitana mofuula, koma ine sindidzamva.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
Zikuoneka kuti nthambi imeneyi anali kuigwiritsa ntchito polambira mafano.