Genesis 22:1-24

22  Tsopano zimenezi zitapita, Mulungu woona anamuyesa Abulahamu+ pomuuza kuti: “Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!”+  Mulungu anapitiriza kuti: “Tenga Isaki+ mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo,+ ndipo muyende ulendo wopita ku Moriya.+ Kumeneko ukamupereke nsembe yopsereza paphiri limene ndidzakuuza.”+  Choncho Abulahamu anadzuka m’mawa kwambiri, n’kumanga chishalo pabulu wake, ndi kutenga anyamata ake awiri limodzi ndi mwana wake Isaki.+ Anawazanso nkhuni zokawotchera nsembe. Atatero, ananyamuka ulendo wopita kumalo amene Mulungu woona anamuuza.  Pa tsiku lachitatu, Abulahamu anakweza maso ake n’kuyamba kuona malowo chapatali.  Tsopano Abulahamu anauza anyamata akewo+ kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambira,+ tikupezani.”  Pamenepo Abulahamu anatenga nkhuni zokawotchera nsembe zija n’kumusenzetsa Isaki mwana wake.+ Iye ananyamula moto ndi mpeni wophera nyama, ndipo iwo anapitira limodzi.+  Ndiyeno Isaki analankhula ndi Abulahamu bambo ake kuti: “Bambo!”+ Abulahamu anayankha kuti: “Lankhula mwana wanga.”+ Chotero iye anafunsa kuti: “Moto ndi nkhuni n’zimenezi, nanga nkhosa yokapereka nsembe yopsereza ili kuti?”+  Abulahamu anayankha kuti: “Mwana wanga, Mulungu apeza yekha nkhosa yopereka nsembe yopsereza.”+ Choncho awiriwo anapitiriza ulendo wawo.  Kenako iwo anafika pamalo amene Mulungu woona anamuuza Abulahamu. Atafika pamalowo, iye anamanga guwa lansembe+ n’kuyala nkhuni zija paguwapo. Atatero, anamanga Isaki mwana wakeyo manja ndi miyendo, n’kumugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni.+ 10  Tsopano Abulahamu anatenga mpeni uja kuti aphe mwana wakeyo.+ 11  Koma mngelo wa Yehova anamuitana kuchokera kumwamba kuti:+ “Abulahamu! Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!” 12  Ndiyeno mngeloyo anapitiriza kulankhula kuti: “Usatambasulire dzanja lako mwanayo ndipo usam’chite kanthu kena kalikonse.+ Tsopano ndadziwa kuti ndiwe woopa Mulungu, pakuti sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”+ 13  Pamenepo Abulahamu anakweza maso ake n’kuona nkhosa yamphongo chapotero, itakodwa ndi nyanga zake m’ziyangoyango. Ndiyeno Abulahamu anakaitenga n’kuipereka nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake.+ 14  Chotero Abulahamu anatcha malowo Yehova-yire.* Ndiye chifukwa chake lero pali mawu akuti: “M’phiri lake Yehova adzapereka zinthu zofunikira.”+ 15  Mngelo wa Yehova anaitananso Abulahamu kachiwiri kuchokera kumwamba, 16  n’kumuuza kuti: “Yehova wati, ‘Ndikulumbira+ pali dzina langa, kuti chifukwa cha zimene wachitazi, posakana kupereka mwana wako yekhayo,+ 17  ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbewu yako ngati nyenyezi zakumwamba, monganso mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Komanso mbewu yako idzalanda chipata* cha adani ake.+ 18  Kudzera mwa mbewu yako,+ mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso* ndithu chifukwa chakuti wamvera mawu anga.’”+ 19  Kenako Abulahamu anabwerera kwa anyamata ake aja, n’kunyamukira nawo limodzi kubwerera ku Beere-seba.+ Abulahamu anapitirizabe kukhala ku Beere-seba. 20  Pambuyo pa zimenezi, uthenga unafika kwa Abulahamu wonena kuti: “Panopo Milika+ naye waberekera m’bale wako Nahori+ ana aamuna. 21  Mwana wake woyamba ndi Uza, ndi Buza+ m’bale wake, komanso Kemueli bambo ake a Aramu. 22  Palinso Kesede, Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betuele.”+ 23  Betuele anabereka Rabeka.+ Ana 8 amenewa ndi amene Milika anaberekera Nahori m’bale wake wa Abulahamu. 24  Panalinso mdzakazi* wake, dzina lake Reuma. M’kupita kwa nthawi iyenso anaberekera Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Yehova-yire” limatanthauza kuti, “Yehova Adziwa Chochita,” ndiponso kuti, “Yehova Adzapereka Zinthu Zofunikira.”
“Chipata” ichi ndi chipata cha mzinda.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 12:3.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.