Genesis 24:1-67

24  Tsopano Abulahamu anali atakalamba ndipo anali ndi zaka zambiri. Yehova anali atamudalitsa m’chilichonse.+  Chotero Abulahamu anauza mtumiki wake yemwe anali wamkulu koposa m’nyumba yake, ndi woyang’anira zinthu zake zonse,+ kuti: “Chonde, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.+  Ndikufuna ulumbire pali Yehova,+ Mulungu wakumwamba ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti sutengera mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi a Akanani, amene ndikukhala pakati pawo.+  M’malomwake, upite kudziko lakwathu kwa abale anga,+ ndipo kumeneko, ndithu ukam’tengere mkazi Isaki mwana wanga.”  Koma mtumikiyo anamufunsa kuti: “Bwanji ngati mkaziyo atakana kubwera nane kuno? Kodi ndidzatenge mwana wanuyu ndi kum’bwezera kudziko lanu kumene munachokera?”+  Pamenepo Abulahamu anayankha kuti: “Ayi, usadzabweze mwana wanga kudziko lakwathu.+  Yehova Mulungu wakumwamba, amene ananditenga ine kunyumba kwa bambo anga ndi kudziko la abale anga,+ amenenso anandilankhula ndi kundilumbirira+ kuti, ‘Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbewu yako,’+ ameneyo atumiza mngelo wake kuti akutsogolere,+ ndipo kumeneko, ndithu ukam’tengere mwana wanga mkazi.+  Koma ngati mkaziyo angakakane kubwera nawe, iweyo udzamasuka pa lumbiro limeneli.+ Koma zoti ukabwezere mwana wanga kumeneko, zimenezo ayi.”  Atatero, mtumikiyo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu ya Abulahamu mbuye wake, n’kulumbira kwa iye pa nkhani imeneyi.+ 10  Pamenepo mtumikiyo anatenga ngamila 10 pa ngamila za mbuye wake, n’kutenganso zabwino za mtundu uliwonse kwa mbuye wake zoti akazigwiritse ntchito.+ Kenako ananyamuka ulendo wopita ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori. 11  Atafika, anagwaditsa pansi ngamilazo kunja kwa mzindawo pachitsime cha madzi.+ Anafika chakumadzulo, pamene akazi mwachizolowezi anali kutuluka mumzindamo kukatunga madzi.+ 12  Ndiyeno mtumikiyo anati: “Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abulahamu,+ chonde chititsani kuti lero zinthu zindiyendere bwino, ndipo sonyezani mbuyanga Abulahamu kukoma mtima kwanu kosatha.+ 13  Ndaima pano pakasupe wa madzi, ndipo ana aakazi a mumzindawu akubwera kudzatunga madzi.+ 14  Zichitike kuti, mtsikana amene ndimuuze kuti, ‘Chonde tula pansi mtsuko wako wa madzi kuti ndimweko,’ ndipo amenedi ati andiyankhe kuti, ‘Imwani, ndiponso nditungira madzi ngamila zanu kuti zimwe,’ ameneyo ndi amene mwasankhira mtumiki wanu+ Isaki. Mukachita zimenezo, ndidziwa kuti mwasonyeza mbuyanga chikondi chosatha.”+ 15  Koma asanamalize kulankhula,+ anangoona Rabeka mwana wa Betuele+ akutuluka mumzindawo. Betuele anali mwana wa Milika,+ ndipo Milika anali mkazi wa Nahori,+ m’bale wake wa Abulahamu. Rabekayo anali atasenza mtsuko paphewa pake.+ 16  Mwana wa mkaziyo anali wokongola mochititsa kaso,+ ndipo anali namwali amene anali asanagonepo ndi mwamuna.+ Iye analowa m’chitsimemo n’kutunga madzi mumtsuko wake, kenako anatulukamo. 17  Nthawi yomweyo mtumiki wa Abulahamuyo anamuthamangira n’kumuuza kuti: “Chonde ndipatse madzi a mumtsuko wako ndimweko pang’ono.”+ 18  Rabekayo anayankha kuti: “Eni, imwani mbuyanga.” Atatero anatsitsa mtsuko wake mwamsanga n’kuupendeketsa kuti mtumikiyo amwe.+ 19  Atamaliza kupereka madzi akumwawo, anati: “Nditungiranso madzi ngamila zanu mpaka zitamwa mokwanira.”+ 20  Choncho, iye mwamsanga anakhuthulira madzi amene anali mumtsuko aja muchomweramo ziweto. Kenako anayamba kuthamanga mobwerezabwereza kukatunga madzi ena pachitsimepo+ mpaka ngamila zonse za mlendoyo zitamwa mokwanira. 21  Nthawi yonseyi n’kuti munthu uja akungomuyang’ana modabwa osanena kalikonse, kuti aone ngati Yehova wapangitsadi ulendo wake kukhala wopambana kapena ayi.+ 22  Kenako, ngamila zija zitatha kumwa, mlendoyo anatenga ndolo yagolide yovala pamphuno+ yolemera hafu ya sekeli, ndi zibangili ziwiri+ zagolide zoti Rabeka azivala m’mikono, zolemera masekeli 10, 23  n’kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe mwana wa ndani? Chonde ndiuze. Kodi kunyumba kwa bambo ako kuli malo oti tikhoza kugonako?”+ 24  Pamenepo iye anayankha kuti: “Ine ndine mwana wa Betuele.+ Bambo angawo mayi awo ndi Milika, bambo wawo ndi Nahori.”+ 25  Ananenanso kuti: “Chakudya cha ziweto tili nacho chambiri, komanso malo ogona alipo.”+ 26  Pamenepo mwamunayo anagwada pansi n’kuwerama pamaso pa Yehova+ 27  n’kunena kuti: “Atamandike Yehova,+ Mulungu wa mbuyanga Abulahamu, amene sanasiye kusonyeza mbuyanga kukoma mtima kosatha ndi kukhala wokhulupirika kwa iye. Pa ulendo wangawu, Yehova wanditsogolera kunyumba kwa abale a mbuyanga.”+ 28  Ndiyeno mtsikanayo anathamangira kunyumba kwa mayi ake n’kufotokozera onse zimenezi. 29  Rabeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani.+ Ndipo Labani anathamanga kupita kwa munthu uja, yemwe anali kuchitsime, kunja kwa mzinda. 30  Tsopano Labani ataona ndolo ya pamphuno ndi zibangili+ pamikono ya mlongo wake, ndiponso atamva mawu a mlongo wake Rabeka akuti: “Munthuyo anandiuza zakutizakuti,” Labaniyo anapita kwa munthuyo ndipo anamupeza ataimirira ndi ngamila zake pachitsimepo. 31  Atangomuona anamuuza kuti: “Tabwerani, inu wodalitsika wa Yehova.+ Bwanji mwangoima kunja kuno? Inetu ndakonza kale malo kunyumbaku, a inu ndi a ngamilazi.” 32  Munthuyo atamva zimenezo, anapita n’kukalowa m’nyumbamo. Pamenepo Labani anamasula ngamila ndi kuzipatsa chakudya. Anatenganso madzi n’kusambitsa mapazi a mlendoyo ndi mapazi a anyamata omwe iye anali nawo.+ 33  Kenako anamuikira chakudya, koma iye anati: “Sindidya kufikira nditanena chimene ndabwerera.” Choncho Labani anati: “Ndiye lankhulanitu!”+ 34  Iye anati: “Ine ndine mtumiki wa Abulahamu.+ 35  Yehova wamudalitsa kwambiri mbuyanga moti akum’lemeretsabe pomupatsa nkhosa, ng’ombe, siliva, golide, antchito aamuna ndi aakazi, ngamila ndi abulu.+ 36  Ndiponso Sara mkazi wake anamuberekera mbuyangayo mwana wamwamuna, mbuyangayo atakalamba.+ Mbuyangayo adzapatsa mwanayo zonse zimene ali nazo.+ 37  Choncho mbuyangayo anandilumbiritsa kuti, ‘Usatengere mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi achikananiwa amene ndikukhala m’dziko lawo.+ 38  Usachite zimenezo, koma upite kubanja la bambo anga, kwa abale anga,+ ukam’tengere mwana wanga mkazi.’+ 39  Koma ineyo ndinafunsa mbuyanga kuti, ‘Bwanji ngati mkaziyo sakabwera nane?’+ 40  Iye anandiyankha kuti, ‘Yehova, amene ndakhala ndikuyenda pamaso pake movomerezeka,+ atumiza mngelo+ wake kuti apite nawe limodzi, ndipo ameneyo akakuthandiza ndithu kuti ukapeze chimene uyendere.+ Kumeneko, ukam’tengere mkazi mwana wanga, kwa abale anga, kubanja la bambo anga.+ 41  Ukakafika kwa abale anga, udzamasuka ku lumbiro limene wachita, ndiponso ngati sakakupatsa mkaziyo, udzamasuka ku lumbiroli.’+ 42  “Nditafika kuchitsime lero, ndinati, ‘Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abulahamu, ngati mundithandizadi kuti ndipeze chimene ndayendera,+ 43  ndaima pano pakasupe wa madzi. Zichitike kuti, namwali+ wotuluka mumzindawu kudzatunga madzi amene ndimuuze kuti, “Chonde, ndimweko pang’ono madzi a mumtsuko wakowo,” 44  amenedi andiyankhe kuti, “Imwani, ndiponso nditungira ngamila zanu kuti zimwe,” ameneyo ndiye mkazi amene Yehova wasankhira mwana wa mbuyanga.’+ 45  “Ndisanamalize kulankhula+ mumtima mwanga,+ ndinangoona Rabeka akutuluka mumzindawu, atanyamula mtsuko wake paphewa. Iye anatsikira kukasupe n’kuyamba kutunga madzi.+ Pamenepo ndinamupempha kuti, ‘Chonde ndigawireko madzi ndimwe.’+ 46  Mwamsanga iye anatula pansi mtsuko wake n’kundiuza kuti, ‘Imwani,+ ndipo nditungiranso ngamila zanu kuti zimwe.’ Choncho ndinamwa madziwo, ndipo iye anatungiranso ngamila kuti zimwe. 47  Atatero ndinamufunsa kuti, ‘Kodi ndiwe mwana wa ndani?’+ Iye anandiyankha kuti, ‘Ine bambo anga ndi a Betuele. Bambo awo ndi a Nahori, ndipo mayi awo ndi a Milika.’ Ndiyeno ndinamuveka ndolo ya pamphuno ndi zibangili m’mikono yake.+ 48  Kenako ndinagwada pansi n’kuwerama pamaso pa Yehova. Ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abulahamu,+ amene wanditsogolera panjira yolondola,+ kuti ndidzatengere mkazi mwana wa mbuyanga kwa m’bale wake. 49  Tsopano ngati mukusonyezadi mbuyanga kukoma mtima kosatha ndi kukhala okhulupirika kwa iye,+ ndiuzeni. Koma ngati ayi, mundiuzenso kuti ndikayang’ane kwina.”+ 50  Ndiyeno Labani ndi Betuele anamuyankha kuti: “Zimenezi zachokera kwa Yehova.+ Ife sitingathe kuvomera kapena kukana kwa inu.+ 51  Nayu Rabeka. M’tengeni muzipita naye, ndipo akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu monga Yehova wanenera.”+ 52  Mtumiki wa Abulahamu atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada n’kuweramira pansi pamaso pa Yehova.+ 53  Kenako, mtumikiyo anayamba kutulutsa zinthu zasiliva, zagolide, ndi zovala n’kupatsa Rabeka. Anaperekanso zinthu zamtengo wapatali kwa mlongo wake wa Rabeka ndi kwa mayi ake.+ 54  Pambuyo pake, iye limodzi ndi anyamata ake anadya ndi kumwa, ndipo anagona komweko ndi kudzuka m’mawa. Kenako mtumiki wa Abulahamu uja anati: “Ndiloleni ndizipita kwa mbuyanga.”+ 55  Koma mlongo wa mtsikanayo ndi mayi ake anati: “Bwanji mtsikanayu akhalebe nafe masiku 10 okha, pambuyo pake akhoza kupita.” 56  Iye anawauza kuti: “Musandichedwetse, chifukwa Yehova wandithandiza kukwaniritsa zimene ndayendera.+ Ndiloleni ndizipita kwa mbuyanga.”+ 57  Pamenepo iwo anati: “Tiyeni timuitane mtsikanayo kuti timve zimene iyeyo anene.”+ 58  Ndiyeno anamuitana Rabekayo ndi kumufunsa kuti: “Kodi upita naye limodzi munthuyu?” Iye anayankha kuti: “Inde ndipita.”+ 59  Pamenepo, iwo analola kuti mlongo wawo Rabeka+ ndi mlezi wake,+ azipita limodzi ndi mtumiki wa Abulahamuyo ndi anyamata ake. 60  Ndiyeno iwo anayamba kudalitsa Rabeka kuti: “Iwe mlongo wathu, ukakhale mayi wa anthu masauzande kuchulukitsa ndi masauzande 10, ndipo mbewu yako ikalande mizinda ya adani awo.”+ 61  Atatha kum’dalitsa, Rabeka ndi adzakazi ake+ ananyamuka n’kukwera ngamila+ kumapita limodzi ndi mtumiki wa Abulahamu uja. Motero mtumikiyo anatenga Rabeka n’kupita naye. 62  Isaki anali kukhala m’dziko la Negebu.+ Tsiku lina, atapatuka panjira yopita ku Beere-lahai-roi,+ 63  anapita m’tchire madzulo kuti akasinkhesinkhe.+ Ataponya maso, anaona ngamila zikubwera poteropo! 64  Nayenso Rabeka atakweza maso anaona Isaki, ndipo mwamsanga anatsika pangamila. 65  Atatero, anafunsa mtumiki uja kuti: “Kodi munthu akubwera apoyo kuchokera m’tchire kudzakumana nafe ndani?” Mtumikiyo anayankha kuti: “Ameneyo ndi mbuyanga.” Pamenepo iye anatenga nsalu yophimba kumutu n’kudziphimba nayo.+ 66  Kenako, mtumikiyo anafotokozera Isaki zonse zimene anachita. 67  Zitatero, Isaki analowa ndi mkaziyo m’hema wa Sara, mayi ake.+ Umu ndi mmene Isaki anatengera Rabeka kukhala mkazi wake.+ Iye anam’konda kwambiri,+ ndipo anatonthozedwa pambuyo pa imfa ya mayi ake.+

Mawu a M'munsi