Genesis 3:1-24

3  Tsopano njoka+ inali yochenjera kwambiri+ kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga.+ Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo+ kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?”+  Pamenepo mkaziyo anayankha njokayo kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya.+  Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda,+ Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’”+  Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: “Kufa simudzafa ayi.+  Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”+  Mkaziyo atamva zimenezo, anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo n’zokoma kudya, zokhumbirika ndi zosiririka.+ Choncho anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya. Pambuyo pake, anapatsako mwamuna wake pamene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.+  Atatero maso awo anatseguka, ndipo anazindikira kuti ali maliseche.+ Choncho anadzisokera masamba a mkuyu n’kupanga zovala zomangira m’chiuno.+  Pambuyo pake, iwo anamva mawu a Yehova Mulungu pamene iye anali kuyendayenda m’mundamo pa nthawi ya kamphepo kayeziyezi.+ Mwamuna ndi mkaziyo atamva, anathawa n’kukabisala pakati pa mitengo ya m’mundamo kuti Yehova Mulungu asawaone.+  Koma Yehova Mulungu anapitiriza kuitana mwamunayo, ndipo anati: “Kodi uli kuti?”+ 10  Potsirizira pake, mwamunayo anayankha kuti: “Ndinamva kuitana kwanu m’munda muno, koma ndinachita mantha poona kuti ndili maliseche. Choncho ndinabisala.”+ 11  Pamenepo Mulungu anati: “Wakuuza ndani kuti uli maliseche?+ Kodi wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti usadzadye?”+ 12  Mwamunayo anayankha kuti: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.”+ 13  Yehova Mulungu atamva zimenezi, anafunsa mkaziyo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi?” Mkaziyo anayankha kuti: “Njoka ndi imene inandinyenga, ndipo ine ndadya.”+ 14  Tsopano Yehova Mulungu anauza njokayo+ kuti: “Chifukwa cha zimene wachitazi, ukhala wotembereredwa pa nyama zonse zoweta ndi zakutchire. Udzakwawa ndi mimba yako ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako.+ 15  Ndidzaika+ chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ ndi pakati pa mbewu yako+ ndi mbewu yake.+ Mbewu ya mkaziyo+ idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe+ udzaivulaza chidendene.”+ 16  Kwa mkaziyo, Mulungu ananena kuti: “Ndidzawonjezera kuvutika kwako pamene uli ndi pakati.+ Pobereka ana udzamva zowawa.+ Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira.”+ 17  Kwa Adamu, Mulungu ananena kuti: “Chifukwa wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula+ kuti, ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa kwa iwe.+ Udzadya zotuluka m’nthakayo movutikira masiku onse a moyo wako.+ 18  Minga ndi zitsamba zobaya* zidzamera panthaka,+ ndipo udzadya zomera za m’nthaka. 19  Udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+ 20  Pambuyo pa izi, Adamu anatcha mkazi wake dzina lakuti Hava,*+ chifukwa anali kudzakhala mayi wa munthu aliyense wamoyo.+ 21  Kenako Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zazitali zachikopa, n’kuwaveka.+ 22  Ndiyeno Yehova Mulungu anati: “Tsopano munthu wakhala wodziwa zabwino ndi zoipa ngati ife.+ Choncho, kuti asathyolenso ndi kudya chipatso cha mtengo wa moyo,+ n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale,* . . .” 23  Yehova Mulungu atatero, anatulutsa munthuyo kunja kwa munda wa Edeni,+ kuti akalime nthaka imene anatengedwako.+ 24  Chotero anam’pitikitsa munthuyo. Ndiyeno anaika akerubi+ kum’mawa kwa munda wa Edeniwo.+ Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linali kuzungulira mosalekeza, kutchinga njira yopita ku mtengo wa moyo.

Mawu a M'munsi

Ena amati “zolasa.”
Dzina limeneli limatanthauza “Wamoyo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.