Genesis 38:1-30
38 Tsopano Yuda anachoka pakati pa abale ake, ndipo anakamanga hema wake pafupi ndi munthu wina wachiadulamu,+ dzina lake Hira.
2 Kumeneko Yuda anaona mwana wamkazi wa Mkanani+ winawake, ndipo anam’kwatira mtsikanayo. Mkananiyo dzina lake anali Sua.
3 Mkaziyo anatenga pakati. Kenako, anabereka mwana wamwamuna, ndipo Yuda anamutcha dzina lakuti Ere.+
4 Anatenganso pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha dzina lakuti Onani.
5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna n’kumutcha dzina lakuti Shela. Mwana ameneyu anam’bereka ali ku Akizibu. +
6 Patapita nthawi, Yuda anatengera mkazi Ere, mwana wake woyamba. Mkaziyo dzina lake anali Tamara.+
7 Koma Ere, mwana woyamba wa Yuda, anakhala munthu woipa pamaso pa Yehova.+ Chotero Yehova anamupha.+
8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa m’bale wako ndipo uchite chokolo, kuti um’berekere ana m’bale wako.”+
9 Koma Onani anadziwa kuti anawo sadzakhala ake.+ Choncho, nthawi zonse akagona ndi mkazi wa m’bale wakeyo, anali kutaya pansi umuna wake kuti asam’berekere ana m’bale wakeyo.+
10 Zimene anachitazo zinamuipira Yehova,+ chotero nayenso anamupha.+
11 Zitatero, Yuda anauza Tamara mpongozi wake kuti: “Pita kunyumba kwa bambo ako, ukakhale kumeneko monga mkazi wamasiye kufikira Shela mwana wanga wamwamuna atakula.”+ Anatero chifukwa mumtima mwake anati: “Nayenso Shela angamwalire ngati abale ake aja.”+ Choncho, Tamara anapita kukakhala kunyumba kwa bambo ake.+
12 Patapita nthawi, mkazi wa Yuda, yemwe anali mwana wa Sua,+ anamwalira. Nthawi yolira maliro+ itatha Yuda anapita ku Timuna,+ kumene anyamata ake anali kumeta ubweya nkhosa zake. Anapita kumeneko limodzi ndi bwenzi lake Hira wachiadulamu+ uja.
13 Tsopano munthu wina anauza Tamara kuti: “Apongozi ako akupita ku Timuna kukameta nkhosa zawo.”+
14 Tamara atamva zimenezo, anavula zovala zake zaumasiye n’kufunda nsalu. Kenako anaphimba nkhope yake ndi nsalu ina. Atatero anakakhala pansi pachipata cha Enaimu m’mbali mwa msewu wopita ku Timuna. Tamara anachita zimenezi poona kuti Shela wakula, koma apongozi ake sakudzam’tenga kuti akakhale mkazi wa Shelayo.+
15 Yuda ataona mkaziyo, anaganiza kuti ndi hule+ chifukwa anali ataphimba nkhope yake.+
16 Choncho Yuda anapatukira kwa mkaziyo pambali pa msewu n’kumuuza kuti: “Ndikufuna ndigone nawe.”+ Anatero posadziwa kuti anali mpongozi wake.+ Koma mkaziyo anayankha kuti: “Mundipatsa chiyani kuti mugone nane?”+
17 Iye anayankha kuti: “Ndidzakutumizira mwana wa mbuzi.” Koma mkaziyo anati: “Mundipatse chikole choti ndisunge kufikira pamene mudzaitumize.”+
18 Iye anati: “Ukufuna ndikupatse chikole chotani?” Mkaziyo anapitiriza kuti: “Mundipatse mphete yanu ya udindo+ wanuyo ndi chingwe chake, ndiponso ndodo yanuyo.” Pamenepo iye anapereka zinthuzo kwa mkaziyo, n’kugona naye ndipo mkaziyo anakhala ndi pakati.
19 Atagona naye, mkaziyo ananyamuka n’kubwerera kwawo. Atafika anavula nsalu imene anadziphimba nayo ija n’kuvala chovala chake chaumasiye.+
20 Yuda anatumiza mwana wa mbuzi uja. Anapempha mnzake wachiadulamu+ uja kuti akam’perekere mbuziyo, ndi cholinga chakuti akamutengere chikole chake kwa mkazi uja, koma sanakam’peze.
21 Kenako anayamba kufunsira kwa amuna akumaloko, kuti: “Kodi hule lapakachisi+ lija lili kuti, lija limene limaima pambali pa msewu kuno ku Enaimu?” Koma amunawo ankayankha kuti: “Kunotu sitinakhalepo ndi hule lapakachisi.”
22 Potsirizira pake, mnzakeyo anabwerera kwa Yuda n’kumuuza kuti: “Mkazi ujatu sindinam’peze. Ndiponso amuna akumeneko anena kuti, ‘Kunotu sitinakhalepo ndi hule lapakachisi.’”
23 Pamenepo Yuda anati: “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopera kuti anthu angatiseke.+ Ndipotu kutumiza ndinatumiza ndithu mwana wa mbuziyo, koma sunakam’peze mkaziyo.”
24 Patapita miyezi itatu, Yuda anauzidwa kuti: “Tamara mpongozi wako anachita chiwerewere,+ ndipo ali ndi pakati.”+ Yuda atamva zimenezo, anati: “M’tulutseni kuti aphedwe ndi kuotchedwa.”+
25 Pamene anali kum’tulutsa, Tamarayo anatumiza mawu kwa apongozi ake kuti: “Mwiniwake zinthu izi ndiye anandipatsa pakatipa.”+ Ananenanso kuti: “Chonde ziyang’anitsitseni,+ muone kuti mpheteyo ndi chingwe chake, komanso ndodoyo n’zandani.”+
26 Ndiyeno Yuda ataziyang’anitsitsa, ananena kuti:+ “Mkaziyu ndi wolungama koposa ine,+ chifukwa sindinam’pereke kwa mwana wanga Shela.”+ Zitatero, Yuda sanagone nayenso.+
27 Itakwana nthawi yoti Tamara abereke, anapezeka kuti ali ndi mapasa m’mimba mwake.
28 Ndipo mmene anali kubereka, mwana mmodzi anatulutsa dzanja lake. Nthawi yomweyo mzamba anatenga kachingwe kofiira kwambiri n’kumanga dzanjalo, n’kunena kuti: “Uyu ndiye wayamba kubadwa.”
29 Koma mwanayo anabweza dzanja lake. Nthawi yomweyo m’bale wake anatuluka, moti mzambayo anafuula kuti: “Ndiye chiyani wachitachi? Bwanji ukuchita kung’amba wekha njira?” N’chifukwa chake anamutcha dzina lakuti Perezi.*+
30 Pambuyo pake, m’bale wake yemwe anali ndi kachingwe kofiira kwambiri padzanja lake uja anatuluka, ndipo anamutcha dzina lakuti Zera.+
Mawu a M'munsi
^ Dzina lakuti “Perezi” limatanthauza kung’amba njira yotulukira mwana pobadwa.