Genesis 40:1-23
40 Pambuyo pake, woperekera chikho+ wa Farao mfumu ya ku Iguputo+ ndi womuphikira mkate, anachimwira mbuye wawo.
2 Farao anawakwiyira kwambiri atumiki ake awiriwo,+ mkulu wa operekera chikho ndi mkulu wa ophika mkate.+
3 Choncho, anawaika m’ndende+ ya m’nyumba mwa mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ mmene Yosefe anali mkaidi.
4 Mmenemo, mkulu wa asilikali olondera mfumu anaika Yosefe kuti azikhala nawo n’kumawalondera,+ ndipo iwo anakhala m’ndendemo kwa masiku ndithu.
5 Usiku wina,+ woperekera chikho ndi wophika mkate, atumiki a mfumu ya Iguputo omwe anali m’ndende+ aja, analota maloto.+ Aliyense analota maloto ake okhala ndi tanthauzo lakelake.+
6 Yosefe atabwera kudzawaona m’mawa, anadabwa poona kuti nkhope zawo zinali zakugwa.+
7 Choncho anafunsa atumiki a Farao aja, omwe anali naye m’ndende ya kunyumba kwa mbuye wakeyo, kuti: “N’chifukwa chiyani nkhope zanu zili zachisoni lero?”+
8 Iwo anamuyankha kuti: “Talota maloto, koma palibe wotimasulira malotowo.” Pamenepo Yosefe anawauza kuti: “Kodi Mulungu sindiye amamasulira?+ Tandifotokozerani malotowo.”
9 Choncho mkulu wa operekera chikho anafotokozera Yosefe maloto ake kuti: “M’maloto anga, ndinaona mtengo wa mpesa uli pamaso panga.
10 Mtengo wa mpesawo unali ndi nthambi zitatu, ndipo unatulutsa mphukira.+ Kenako unamasula maluwa n’kubereka mphesa ndipo zinapsa.
11 M’manja mwanga ndinali ndi chikho cha Farao, ndipo ndinatenga mphesazo n’kuzifinyira m’chikho cha Faraocho.+ Nditatero, ndinapereka chikhocho kwa Farao.”+
12 Pamenepo Yosefe anamuuza kuti: “Kumasulira kwake ndi uku:+ Nthambi zitatuzo zikuimira masiku atatu.
13 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa. Adzakubwezera ndithu pa ntchito yako yakale,+ yoperekera chikho kwa mfumuyo.+
14 Komabe, zonse zikadzakhala bwino kwa iwe usadzandiiwale.+ Chonde, udzandikomere mtima ponditchula kwa Farao,+ ndipo ukayesetse kuti ndidzatuluke m’ndende muno.
15 Kuti ndipezeke kuno anachita chondiba kudziko la Aheberi,+ ndiponso kuno palibe chilichonse chimene ndinalakwa choti andiikire m’ndende muno.”+
16 Mkulu wa ophika mkate ataona kuti Yosefe wamasulira zabwino, nayenso anati: “Inenso ndinalota maloto. Ndinalota nditasenza pamutu pangapa nsengwa zitatu za mikate yoyera.
17 Munsengwa yapamwambayo munali mikate yosiyanasiyana ya Farao,+ ndipo mbalame+ zinali kudya mikateyo munsengwayo pamutu panga.”
18 Ndiyeno Yosefe anati: “Kumasulira kwake ndi uku:+ Nsengwa zitatuzo zikuimira masiku atatu.
19 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa n’kukudula mutu. Adzakupachika pamtengo,+ ndipo mbalame zidzadya nyama yako ndithu.”+
20 Tsiku lachitatulo linafika, ndipo linali tsiku lokumbukira kubadwa kwa Farao.+ Mfumuyo inakonzera phwando antchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa m’ndende mkulu wa operekera chikho ndi mkulu wa ophika mkate, n’kuwaimika pamaso pa antchito ake onse.+
21 Farao anabwezeradi pa ntchito mkulu wa operekera chikho uja,+ moti anapitiriza ntchito yake yoperekera chikho kwa Farao.
22 Koma mkulu wa ophika mkate anam’pachika,+ monga mmene Yosefe anawauzira pomasulira maloto+ aja.
23 Komabe, mkulu wa operekera chikho uja anamuiwala Yosefe osam’kumbukira.+