Genesis 45:1-28

45  Pamenepo Yosefe analephera kudzigwira pamaso pa anthu onse amene anaima pafupi naye.+ Choncho anafuula kuti: “Tulutsani aliyense muno!” Motero, panalibe aliyense amene anali naye pa nthawi imene Yosefe ankadziulula kwa abale ake.+  Atatero, anayamba kulira mokweza mawu+ mpaka Aiguputo anamva, ndiponso a kunyumba ya Farao anamva zakuti Yosefe akulira.  Kenako Yosefe anauza abale akewo kuti: “Ndine Yosefe! Kodi bambo anga ali moyobe?” Koma abale akewo sanathe kumuyankha chifukwa anali atawasokoneza maganizo.+  Pamenepo Yosefe anauza abale akewo kuti: “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anasenderadi pafupi naye. Ndiyeno Yosefe anati: “Ndine m’bale wanu uja Yosefe, amene munamugulitsa ku Iguputo.+  Koma musadzimvere chisoni+ kapena kudzipsera mtima kuti munandigulitsa kuno. Mulungu ndiye ananditumiza patsogolo panu kuti ndidzapulumutse miyoyo yanu.+  Chino ndi chaka chachiwiri cha njala padziko pano.+ Kutsogoloku kukubwera zaka zina zisanu zimene anthu sadzalima kapena kukolola.+  Choncho Mulungu ananditumiza kuno patsogolo panu, kuti pakhale otsalira a anthu inu padziko lapansi,+ ndi kuti mukhalebe ndi moyo mwa chipulumutso chachikulu.  Chotero si inu amene munanditumiza kuno,+ koma Mulungu woona. Anachita zimenezi kuti andiike kukhala tate+ kwa Farao, ndi mbuye wa nyumba yake yonse, ndiponso woyang’anira wa dziko lonse la Iguputo.  “Pitani kwa bambo anga msanga, ndipo mukawauze kuti, ‘Mwana wanu Yosefe wati: “Mulungu wandiika ine kukhala mbuye wa dziko lonse la Iguputo.+ Bwerani kuno kwa ine, musachedwe. 10  Inuyo, ana anu, adzukulu anu, nkhosa ndi ng’ombe zanu, ndi zonse zimene muli nazo mudzakhale m’dziko la Goseni+ pafupi ndi ine. 11  Kumeneko ndizidzakupatsani chakudya. Kwatsala zaka zisanu za njala,+ ndipo sindikufuna kuti inuyo ndi a m’nyumba yanu, ndi zonse zimene muli nazo muvutike ndi njala.”’ 12  Inuyo ndi m’bale wangayu Benjamini, mukuona ndi maso anu kuti ndine amene ndikulankhula kwa inu ndi pakamwa pangapa.+ 13  Choncho, mukauze bambo anga za ulemerero wanga wonse kuno ku Iguputo, ndi zonse zimene mwaona. Ndipo fulumirani mukatenge bambo anga n’kubwera nawo kuno.” 14  Yosefe atatero, anakumbatira Benjamini m’bale wake n’kuyamba kulira. Nayenso Benjamini analira atakumbatira m’bale wakeyo.+ 15  Pamenepo Yosefe anayamba kupsompsona abale ake onsewo n’kumalira akuwakumbatira.+ Pambuyo pake, abale akewo analankhula naye. 16  Nkhani inamveka kunyumba kwa Farao kuti: “Abale ake a Yosefe abwera!” Farao ndi atumiki ake anasangalala atamva zimenezo.+ 17  Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: “Uza abale ako kuti, ‘Chitani izi: Kwezani katundu panyama zanu, mupite kudziko la Kanani.+ 18  Mukatenge bambo anu ndi mabanja anu n’kubwera nawo kuno kwa ine. Ndidzakupatsani zabwino za dziko la Iguputo, ndipo mudzadya zonona za dzikoli.+ 19  Uwauzenso kuti:+ “Chitani izi: Mutenge ngolo+ kuno ku Iguputo zokatengera ana anu aang’ono ndi akazi anu. Ngolo ina mukatengere bambo anu n’kubwera kuno.+ 20  Musakadandaule za katundu wanu,+ chifukwa zabwino za dziko lonse la Iguputo ndi zanu.”’”+ 21  Ana a Isiraeli aja anachitadi zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga momwe Farao analamulira. Anawapatsanso kamba+ wa pa ulendo. 22  Aliyense wa iwo anam’patsa chovala choti asinthire,+ koma Benjamini anam’patsa zovala zosinthira zisanu, ndi ndalama zasiliva 300.+ 23  Kwa bambo ake anatumizako abulu 10 onyamula zinthu zokoma zochokera ku Iguputo, ndi abulu aakazi 10 onyamula tirigu ndi chakudya chawo cha pa ulendo. 24  Atatero, anauza abale akewo kuti anyamuke, ndipo iwo ananyamuka. Koma anawachenjeza kuti: “Musakanganetu m’njira.”+ 25  Iwo ananyamuka ku Iguputo kuja n’kuyenda ulendo wawo mpaka kukafika kudziko la Kanani, kwa Yakobo bambo awo. 26  Atafika, anauza bambo awo kuti: “Yosefe uja ali moyo! Ndiye woyang’anira dziko lonse la Iguputo!”+ Yakobo atamva zimenezo sizinam’khudze chifukwa sanazikhulupirire.+ 27  Koma atamufotokozera mawu onse amene Yosefe ananena, ndiponso ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti zidzam’tenge, mtima wa Yakobo bambo awo unayamba kubwereramo.+ 28  Pamenepo Isiraeli anafuula kuti: “Basi, tsopano ndakhulupirira! Yosefe mwana wanga akadali ndi moyo! Ndipita ndikamuone ndisanafe!”+

Mawu a M'munsi