Genesis 48:1-22
48 Ndiyeno patapita nthawi Yosefe anauzidwa kuti: “Bambo anutu afooka.” Pamenepo, Yosefe anatenga ana ake awiri, Manase ndi Efuraimu,+ n’kupita kwa bambo akewo.
2 Ndiyeno Yakobo anauzidwa kuti: “Mwana wanu Yosefe wabwera.” Choncho Isiraeli anadzuka modzilimbitsa n’kukhala tsonga pabedi.
3 Tsopano Yakobo anauza Yosefe kuti:
“Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine ku Luzi+ m’dziko la Kanani kuti andidalitse.+
4 Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana,+ ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu yambiri ya anthu.+ Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako kuti lidzakhale dziko lawo mpaka kalekale.’+
5 Tsopano ana awiri amene unabereka ku Iguputo kuno ine ndisanabwere, ndi ana anga.+ Efuraimu ndi Manase akhala ana anga monga alili Rubeni ndi Simiyoni.+
6 Koma ana amene udzabereke pambuyo pa anawa, amenewo adzakhala ako. Iwo adzalandira mbali ya malo amene abale awo adzalandire ngati cholowa.+
7 Kunena za ine, pamene ndinali kuchokera ku Padani,+ mayi ako Rakele anandifera+ panjira m’dziko la Kanani, patatsala mtunda ndithu kuti tifike ku Efurata. Zitatero, ndinawaika m’manda panjira yopita ku Efurata,+ kapena kuti Betelehemu.”+
8 Tsopano Isiraeli anaona ana a Yosefe, ndipo anafunsa kuti: “Kodi awa ndani?”+
9 Yosefe anayankha bambo akewo kuti: “Ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kunoko.”+ Ndiyeno bambo akewo anati: “Chonde, tawabweretsa kuno ndiwadalitse.”+
10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+
11 Ndiyeno Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Ndinalibiretu chiyembekezo choti ndidzaonanso nkhope yako,+ koma tsopano Mulungu wandilola kuona iwe limodzi ndi ana ako omwe.”
12 Atatero, Yosefe anachotsa anawo pambali pa mawondo a bambo ake. Kenako, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+
13 Tsopano Yosefe anatenga ana ake awiriwo. Efuraimu anamuika kudzanja lake lamanja, kumanzere kwa Isiraeli.+ Ndipo Manase anamuika kudzanja lake lamanzere, kudzanja lamanja la Isiraeli.+ Atatero, anawabweretsa pafupi ndi bambo ake.
14 Koma Isiraeli anatambasula dzanja lake lamanja n’kuliika pamutu pa Efuraimu,+ ngakhale kuti ndiye anali wamng’ono.+ Anatambasulanso dzanja lake lamanzere n’kuliika pamutu pa Manase.+ Anasemphanitsa dala choncho manja ake chifukwa Manase ndiye anali mwana woyamba.+
15 Pamenepo anadalitsa Yosefe,+ kuti:
“Mulungu woona amene makolo anga Abulahamu ndi Isaki anayenda pamaso pake,+Mulungu woona amene wakhala m’busa wanga moyo wanga wonse mpaka lero,+
16 Mngelo amene wakhala akundiwombola ku masoka anga onse,+ adalitse anyamatawa.+
Dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abulahamu ndi Isaki, apitirize kutchulidwa kudzela mwa anawa,+Komanso, anawa adzachulukane, adzakhale khamu la anthu padziko lapansi.”+
17 Yosefe ataona kuti bambo ake aika dzanja lawo lamanja pamutu pa Efuraimu, sizinamusangalatse.+ Choncho, anagwira dzanja la bambo ake kuti alichotse pamutu pa Efuraimu, n’kuliika pamutu pa Manase.+
18 Yosefe anauza bambo ake kuti: “Ayi bambo, musatero ayi. Mwana woyamba ndi uyu.+ Ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.”
19 Koma bambo akewo anakanabe, kuti: “Ndikudziwa mwana wanga, ndikudziwa zimenezo. Uyunso adzakhala mtundu wa anthu, ndipo adzakhala wamkulu.+ Koma mng’ono wakeyu adzakhala wamkulu kuposa iyeyu,+ ndipo mbadwa zake zidzachuluka kwambiri n’kupanga mitundu ya anthu.”+
20 Iye anapitiriza kuwadalitsa pa tsikulo.+ Anati:
“Pogwiritsa ntchito dzina lako, Aisiraeli azidzadalitsana kuti,‘Mulungu akudalitse monga anadalitsira Efuraimu ndi Manase.’”+
Choncho Isiraeli anaikabe Efuraimu patsogolo pa Manase.+
21 Isiraeli atatero, anauza Yosefe kuti: “Taona, inetu ndikufa.+ Koma Mulungu adzakhalabe nanu ndithu anthu inu, ndipo adzakubwezerani kudziko la makolo anu.+
22 Koma ine ndikukuwonjezera gawo limodzi la dziko kuposa abale ako,+ limene ndinalanda Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.”