Genesis 6:1-22
6 Pamene anthu anayamba kuchuluka padziko lapansi, kunabadwa ana aakazi.+
2 Ndiyeno ana a Mulungu+ woona anayamba kuona+ kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.
3 Pambuyo pake, Yehova anati: “Mzimu wanga+ supitiriza mpaka kalekale kulezera mtima anthu,+ popeza alinso athupi.+ Choncho, masiku a moyo wawo adzangokhala zaka 120.”+
4 M’masiku amenewo ndiponso kupita m’tsogolo, padziko lapansi panali Anefili.* Pa nthawiyo, ana a Mulungu woona anali kugona ndi ana aakazi a anthu ndipo anawaberekera ana. Anawo anali ziphona zakalelo, amuna otchuka.
5 Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+
6 Chotero, Yehova anamva chisoni+ kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.+
7 Choncho Yehova anati: “Ndidzaseseratu padziko lapansi anthu amene ndinawalenga.+ Kuyambira munthu, nyama yoweta, nyama yokwawa, mpaka cholengedwa chouluka m’mlengalenga,+ chifukwa ndikumva chisoni kuti ndinazipanga.”+
8 Koma Nowa anayanjidwa ndi Yehova.
9 Tsopano nayi mbiri ya Nowa.
Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+
10 M’kupita kwa nthawi, Nowa anabereka ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.+
11 Koma dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo linadzaza ndi chiwawa.+
12 Chotero, Mulungu poyang’ana dziko lapansi anaona kuti laipa,+ chifukwa njira za anthu onse zinali zitaipa.+
13 Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse,+ popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. Choncho ndiwawonongera limodzi ndi dziko lapansi.+
14 Udzipangire chingalawa cha mtengo wa mnjale.+ Uchigawe zipindazipinda, ndipo uchimate ndi phula+ mkati ndi kunja komwe.
15 Uchipange motere: M’litali chikhale mikono*+ 300, m’lifupi mikono 50, ndipo kutalika kwake kuyambira pansi mpaka pamwamba chikhale mikono 30.
16 Chingalawacho uchiike windo.* Windolo likhale la mpata wa mkono umodzi kuchokera kudenga* lake. Khomo la chingalawacho uliike m’mbali mwake.+ Chikhale cha nyumba zosanjikiza zitatu, yapansi, yapakati, ndi yapamwamba.
17 “Koma ine ndidzabweretsa chigumula+ chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo+ chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo* m’thupi mwake. Chilichonse cha m’dziko lapansi chidzafa.+
18 Ndipo ndikupanga pangano ndi iwe. Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.+
19 Udzalowetsenso m’chingalawacho chamoyo chilichonse cha mtundu uliwonse.+ Udzazilowetse ziwiriziwiri, champhongo ndi chachikazi, kuti zidzasungike zamoyo limodzi nawe.+
20 Udzalowe nazo ziwiriziwiri za mtundu uliwonse. Zolengedwa zouluka monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo,+ nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yawo, kuti zidzasungike zamoyo.+
21 Koma iweyo udzatenge chakudya cha mtundu uliwonse chodyedwa.+ Udzachisonkhanitse kuti chidzakhale chakudya chanu ndi cha zamoyo zinazo.”+
22 Ndipo Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu akuti “Anefili” amatanthauza “ogwetsa anzawo.”
^ “Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
^ Mawu achiheberi ndi “tsoʹhar,” ndipo angatanthauze “windo” kapenanso “denga.”
^ Kapena kuti “tsindwi.”
^ Onani Zakumapeto 4.