Levitiko 13:1-59

13  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti:  “Munthu akatuluka zotupa, kapena nkhanambo,+ kapena chikanga pakhungu lake, ndipo chasintha n’kukhala nthenda ya khate,+ azibwera naye kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake amenenso ndi ansembe.+  Ndiyeno wansembeyo aone nthenda imene yatuluka pakhunguyo.+ Ngati cheya cha pamalopo chasanduka choyera ndipo pakuoneka kuti m’pozama kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe aone nthendayo n’kugamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa.  Koma ngati chikangacho chikuoneka choyera ndipo si chozama kupitirira khungu, komanso cheya sichinasanduke choyera, wansembe azibindikiritsa+ munthuyo masiku 7.  Ndiyeno wansembe azionanso munthuyo pa tsiku la 7, ndipo ngati nthendayo yaoneka kuti yatha, moti sinafalikire pakhungu, wansembe azibindikiritsa+ munthuyo masiku enanso 7.  “Ndiyeno pa tsiku la 7, wansembe azionanso munthuyo kachiwiri. Ngati nthendayo yayamba kuzimiririka ndipo sinafalikire pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera. Inali chabe nkhanambo. Munthuyo azichapa zovala zake ndi kukhala woyera.  Koma ngati nkhanambo yafalikira pakhungu la munthu pambuyo poti anaonekera kwa wansembe ndipo anagamula kuti ndi woyera, munthuyo azikaonekeranso kachiwiri kwa wansembe.+  Pamenepo wansembe azionanso munthuyo, ndipo ngati nkhanambo yake yafalikira pakhungu, wansembeyo azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate.+  “Munthu akagwidwa ndi nthenda ya khate, azim’bweretsa kwa wansembe. 10  Wansembe aziona nthendayo,+ ndipo ngati pali zotupa moti khungu ndi cheya zayera, ndipo chilondacho chikunyeka,+ 11  limenelo ndi khate losachiritsika+ pakhungu lake, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asam’bindikiritse,+ pakuti ndi wodetsedwa. 12  Koma ngati khate labukadi pakhungu lake, moti n’zoonekeratu kwa wansembe kuti lafalikira pathupi lonse la munthuyo, kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13  ndipo wansembe wamuona, n’kutsimikizira kuti khatelo lafalikiradi thupi lonse, pamenepo azigamula kuti munthuyo ndi woyera.* Khungu lake lonse latuwa, choncho ndi woyera. 14  Koma tsiku limene zilonda zonyeka zidzaonekera, adzakhala wodetsedwa. 15  Wansembe+ aziona zilondazo ndi kugamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa chifukwa cha zilondazo. Limenelo ndi khate.+ 16  Kapena ngati zilondazo zapola n’kusanduka zoyera, munthuyo azibwera kwa wansembe. 17  Ndiyeno wansembe azimuona.+ Ngati khungu lake latuwa, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wosadetsedwa. Iye ndi woyera. 18  “Ngati pakhungu la munthu pali chithupsa,+ ndipo kenako chapola, 19  ndipo pamene panali chithupsapo pabuka chotupa choyera kapena chikanga chotuwa mofiirira, munthuyo azikadzionetsa kwa wansembe. 20  Pamenepo wansembe azimuona,+ ndipo ngati chikuoneka kuti n’chozama kupitirira khungu, ndipo cheya chake chasanduka choyera, pamenepo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. Yabuka pachithupsa. 21  Koma wansembe akachiona n’kupeza kuti palibe cheya choyera ndipo si chozama kupitirira khungu komanso chayamba kuzimiririka, pamenepo azim’bindikiritsa+ masiku 7. 22  Ngati chikangacho chafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda. 23  Koma ngati chikangacho sichinasinthe, osafalikira, kumeneko ndi kutukusira+ kwa chithupsa. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ 24  “Kapena ngati pakhungu pali chilonda cha moto, ndipo mnofu wa pachilondacho wayamba kuoneka wotuwa mofiirira kapena woyera, 25  pamenepo wansembe aziona chilondacho. Ngati cheya cha pamenepo chasanduka choyera ndipo chilondacho chikuoneka chozama kupitirira khungu, limenelo ndi khate. Labuka pachilonda, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 26  Koma ngati wansembe waona chilondacho, n’kupeza kuti palibe cheya choyera ndipo chilondacho si chozama kupitirira khungu, komanso chikubwerera mwakale, wansembe azim’bindikiritsa masiku 7. 27  Ndipo wansembe aziona munthuyo pa tsiku la 7. Ngati nthendayo yafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 28  Koma ngati kutuwa kwa pachilondapo sikunasinthe, osafalikira pakhungu, ndipo kwayamba kuzimiririka, kumeneko ndi kutupa kwa chilonda. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera chifukwa kumeneko ndi kutukusira kwa chilonda. 29  “Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi nthenda ina yake pamutu kapena pachigama, 30  wansembe+ aziona nthendayo. Ngati pamalopo pakuoneka pozama kupitirira khungu, komanso tsitsi lachita chikasu ndipo lili patalipatali, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda yothothola tsitsi.+ Ndi khate la kumutu kapena kuchigama. 31  Koma wansembe akaona nthenda yothothola tsitsiyo, n’kuona kuti pamalopo pakuoneka kuti si pozama kupitirira khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda, wansembe azibindikiritsa+ munthuyo masiku 7.+ 32  Wansembe azionanso nthendayo pa tsiku la 7. Ngati nthenda yothothola tsitsiyo+ sinafalikire, komanso pamalopo sipanamere tsitsi lachikasu ndipo pakuoneka kuti si pozama kupitirira khungu, 33  pamenepo munthuyo azimetedwa tsitsi lake, koma asamam’mete pamene pali nthenda yothothola tsitsipo.+ Ndipo wansembe azibindikiritsa munthuyo masiku enanso 7. 34  “Ndiyeno pa tsiku la 7 wansembe azionanso nthenda yothothola tsitsiyo. Ngati nthendayo sinafalikire pakhungu, ndipo pamalopo pakuoneka kuti si pozama kupitirira khungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ Pamenepo munthuyo azichapa zovala zake ndi kukhala woyera. 35  Koma ngati nthenda yothothola tsitsiyo yafalikiradi pakhungu pambuyo pogamula kuti munthuyo ndi woyera, 36  wansembe+ azionanso munthuyo. Ngati nthenda yothothola tsitsiyo yafalikira pakhungu, wansembe asafufuzenso tsitsi lachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa. 37  Koma ngati nthenda yothothola tsitsiyo ikuoneka kuti yasiya, ndipo pamera tsitsi lakuda, ndiye kuti nthendayo yatha. Munthuyo ndi woyera, ndipo wansembe azigamula kuti ndi woyera.+ 38  “Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi zikanga+ zotuwa pakhungu lake, 39  wansembe+ aziziona. Ngati zikangazo zayamba kuzimiririka, imeneyo ndi nthenda yosaopsa imene yabuka pakhungu lake. Munthuyo ndi woyera. 40  “Mwamuna akayamba kutha tsitsi,+ limenelo ndi dazi, ndipo ndi woyera. 41  Ngati tsitsi likutha patsogolo pa mutu wake, limenelo ndi dazi la pamphumi, ndipo ndi woyera. 42  Koma ngati padazi la pankhongo kapena la pamphumi pabuka nthenda yotuwitsa khungu mofiirira, limenelo ndi khate, labuka padazi la pankhongo kapena la pamphumi. 43  Wansembe+ aziona munthuyo, ndipo ngati padazi lake la pankhongo kapena la pamphumi patuluka ziwengo zotuwa mofiirira zooneka ngati khate pakhungu lakelo, 44  ameneyo ali ndi khate ndipo ndi wodetsedwa. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Ali ndi nthenda pamutu pake. 45  Ndiyeno zovala za munthu amene am’peza ndi khateyo zizing’ambidwa.+ Munthuyo asamakonze tsitsi lake+ ndipo aziphimba ndevu zake zapamlomo+ ndi kufuula kuti, ‘Wodetsedwa, wodetsedwa!’+ 46  Masiku onse pamene akudwala nthendayo azikhala wodetsedwa. Iye ndi wodetsedwa ndipo azikhala payekha. Azikhala kunja kwa msasa.+ 47  “Nthenda ya khate ikabuka pachovala, kaya chovalacho ndi chaubweya wa nkhosa kapena chansalu, 48  kaya yabuka cha m’litali+ kapena cha m’lifupi* mwa chovala chansalu ndi chovala chaubweya wa nkhosa, kapena pachikopa kapenanso pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa,+ 49  ndipo nthendayo ikuoneka yobiriwira mopitira ku chikasu kapena yofiirira pachovala kapena pachikopa, m’litali kapena m’lifupi mwa nsalu, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nthenda ya khate ndipo iyenera kusonyezedwa kwa wansembe. 50  Pamenepo wansembe+ aziona nthendayo, ndipo azisunga chinthucho kwachokha+ masiku 7. 51  Akaona nthendayo pa tsiku la 7, n’kupeza kuti nthendayo yafalikira pachovala, m’litali kapena m’lifupi,+ kapena pachikopa, kaya amachigwiritsa ntchito yotani, nthendayo ndi khate loopsa.+ Chinthucho ndi chodetsedwa. 52  Pamenepo azitentha chovalacho, nsalu ya ubweya wa nkhosa kapena nsalu ina iliyonse,+ kapena zilizonse zopangidwa ndi chikopa, zimene zagwidwa ndi nthenda ya khateyo, chifukwa khate limenelo ndi loopsa.+ Zizitenthedwa pamoto. 53  “Koma wansembeyo akaona, n’kupeza kuti nthendayo sinafalikire pachovalacho, m’litali kapena m’lifupi, kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa,+ 54  wansembe azilamula kuti achape chinthu chogwidwa ndi nthendacho ndipo azichisungira kwachokha masiku enanso 7. 55  Wansembe aziona nthendayo, chinthucho chitachapidwa. Ngati nthendayo ikuonekabe chimodzimodzi koma sinafalikire, chinthucho ndi chodetsedwa. Muzichitentha pamoto. Chimenecho chadyedwa ndi nthendayo kuyambira mkati kapena kuyambira kunja kwake. 56  “Koma ngati wansembe waona, n’kupeza kuti nthenda ija yayamba kuzimiririka chinthucho chitachapidwa, azing’amba mbali yogwidwa ndi nthendayo pachovalacho kapena pachikopacho. 57  Koma ngati ikuonekabe pachovala, m’litali kapena m’lifupi,+ kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nthendayo ikufalikira. Chilichonse chimene chagwidwa ndi nthendayi muzichitentha+ pamoto. 58  Koma ngati nthendayo yazimiririka mutachapa chovala kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, muzichichapanso kachiwiri, pamenepo chizikhala choyera. 59  “Limeneli ndilo lamulo lokhudza nthenda ya khate yopezeka pachovala chaubweya wa nkhosa kapena chansalu,+ m’litali kapena m’lifupi, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti wansembe adziwe chinthu choyenera kugamula kuti n’choyera kapena n’chodetsedwa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “nthendayo sangapatsire ena.”
Mawu ake enieni, “ulusi wowombera nsalu woyenda m’litali kapena m’lifupi.”