Levitiko 22:1-33
22 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
2 “Uza Aroni ndi ana ake kuti asayandikire zinthu zopatulika za ana a Isiraeli ndi kuipitsa dzina langa loyera.+ Asayandikire zinthu zimene azipatula kuti azipereke nsembe kwa ine.+ Ine ndine Yehova.
3 Uwauze kuti, ‘M’mibadwo yanu yonse munthu aliyense wodetsedwa mwa ana anu, amene adzayandikira zinthu zopatulika, zimene ana a Isiraeli azipatula kuti azipereke nsembe kwa Yehova,+ munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pamaso panga. Ine ndine Yehova.
4 Mwamuna aliyense mwa ana a Aroni amene ali ndi khate+ kapena nthenda yakukha,+ asadye zinthu zopatulika kufikira atakhala woyera.+ Zikhalenso chimodzimodzi ndi aliyense wokhudza munthu amene wadetsedwa chifukwa cha munthu wakufa,+ kapena mwamuna amene watulutsa umuna,+
5 kapenanso mwamuna amene wakhudza chilichonse mwa zamoyo zodetsedwa+ zopezeka zambiri, kapena amene wakhudza munthu wodetsedwa ndi chilichonse chimene chimadetsa munthu.+
6 Munthu wokhudza chilichonse mwa zinthu zoterezi akhale wodetsedwa kufikira madzulo ndipo asadye chilichonse mwa zinthu zopatulika, koma asambe thupi lonse.+
7 Dzuwa likalowa akhalenso woyera, ndipo pambuyo pake akhoza kudya zina mwa zinthu zopatulika, chifukwa ndi chakudya chake.+
8 Iye asadye nyama iliyonse imene waipeza yakufa, kapena iliyonse yophedwa ndi zilombo, chifukwa angakhale wodetsedwa.+ Ine ndine Yehova.
9 “‘Chotero azisunga malamulo anga kuti asasenze tchimo ndi kufa,+ chifukwa chosasunga malamulowo ndi kuipitsa zinthu zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndawapatula monga anthu oyera.
10 “‘Munthu wamba* asadye chopatulika chilichonse.+ Mlendo wokhala m’nyumba ya wansembe kapena munthu waganyu, asadye chopatulika chilichonse.
11 Koma munthu amene wansembe wamugula ndi ndalama zake, nayenso angathe kudya zopatulikazo. Akapolo obadwira m’nyumba ya wansembe, nawonso angadye nawo chakudya chake.+
12 Mwana wamkazi wa wansembe akakwatiwa ndi munthu amene si wa m’banja la ansembe, asadye nawo zopereka zopatulika.
13 Koma mwana wa wansembe akakhala mkazi wamasiye, kapena wosiyidwa ukwati alibe mwana aliyense, ndipo wabwerera kunyumba kwa bambo ake kumene anali ali mwana,+ angadye nawo chakudya cha bambo ake.+ Koma munthu wamba asadye nawo chakudya chimenecho.
14 “‘Munthu akadya mosadziwa chinthu chopatulika,+ azibwezera chinthucho ndi kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo ake asanu.+ Azipereka chinthu chopatulikacho kwa wansembe.
15 Zili choncho kuti ansembe asaipitse zinthu zopatulika za ana a Isiraeli, zimene angapereke kwa Yehova,+
16 ndi kuchititsa anthuwo kulandira chilango pa kulakwa kwawoko chifukwa chakuti adya zinthu zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndikuwapatula kuti akhale oyera.’”
17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
18 “Uza Aroni ndi ana ake ndi ana onse a Isiraeli kuti, ‘Mwamuna aliyense wa nyumba ya Isiraeli, kapena mlendo wokhala mu Isiraeli amene akupereka nsembe+ pofuna kukwaniritsa lonjezo lake lililonse,+ kapena amene akupereka nsembe yake yaufulu,+ imene akuipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza,
19 azipereka nyama yopanda chilema,+ ng’ombe yamphongo, nkhosa yamphongo kapena mbuzi, kuti Mulungu akuyanjeni.+
20 Nyama iliyonse yachilema musaipereke nsembe,+ chifukwa Mulungu sadzakuyanjani.
21 “‘Munthu akafuna kupereka nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova kuti akwaniritse lonjezo lake+ kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, azipereka ng’ombe kapena nkhosa yopanda chilema, kuti Mulungu ailandire. Izikhala yopanda chilema chilichonse.
22 Isakhale yakhungu, yothyoka chiwalo, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo kapena zipere.+ Iliyonse yokhala ndi zimenezi musaipereke kwa Yehova ndipo musaike nsembe yotentha ndi moto+ ya nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova.
23 Ng’ombe kapena nkhosa yokhala ndi chiwalo chimodzi chachitali kwambiri kapena chachifupi kwambiri kuposa chinzake,+ mungaipereke monga nsembe yaufulu, koma Mulungu sadzailandira mukaipereka pokwaniritsa lonjezo lanu.
24 Nyama imene mavalo+ ake anawafinya, kuwatswanya, kuwathothola kapena kuwadula, musaipereke kwa Yehova, ngakhalenso m’dziko lanu musadzapereke nsembe nyama zoterezi.
25 Ndipo iliyonse mwa nyama zonse zoterezi yochokera kwa mlendo musaipereke nsembe monga chakudya cha Mulungu wanu, chifukwa ndi yowonongeka. Ili ndi chilema,+ ndipo Mulungu sadzailandira.’”+
26 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
27 “Ng’ombe, nkhosa kapena mbuzi ikabadwa, izikhala ndi mayi ake masiku 7,+ koma kuyambira tsiku la 8 kupita m’tsogolo mungaipereke kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto, ndipo Mulungu adzailandira.
28 Ng’ombe kapena nkhosa, musaiphe tsiku limodzi ndi mwana wake.+
29 “Mukafuna kupereka nsembe yoyamikira kwa Yehova+ muziipereka m’njira yakuti Mulungu akuyanjeni.
30 Muziidya pa tsiku lomwelo.+ Musasiyeko iliyonse kufikira m’mawa.+ Ine ndine Yehova.
31 “Muzisunga malamulo anga.+ Ine ndine Yehova.
32 Musaipitse dzina langa loyera,+ m’malomwake muzindiona kukhala wopatulika pakati pa ana a Isiraeli.+ Ine ndine Yehova amene ndikukupatulani kuti mukhale oyera.+
33 Ndine amene ndakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu wanu.+ Ine ndine Yehova.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti munthu amene si wa m’banja la Aroni.