Levitiko 8:1-36
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
2 “Tenga Aroni pamodzi ndi ana ake,+ zovala zawo,+ mafuta odzozera,+ ng’ombe yamphongo ya nsembe yamachimo,+ nkhosa ziwiri zamphongo, ndi dengu la mikate yopanda chofufumitsa.+
3 Ndiyeno usonkhanitse khamu lonse+ pakhomo la chihema chokumanako.”+
4 Mose anachita monga mmene Yehova anam’lamulira. Ndipo khamu lonse linasonkhana pakhomo+ la chihema chokumanako.
5 Pamenepo Mose anauza khamulo kuti: “Yehova walamula kuti tichite zinthu izi.”+
6 Kenako Mose anaitana Aroni ndi ana ake ndi kuwalamula kuti asambe.+
7 Atatero anaveka Aroni mkanjo+ ndi kum’manga lamba wa pamimba.+ Anamuvekanso malaya odula manja+ komanso efodi,*+ ndi kum’manga kwambiri ndi lamba+ wa efodiyo.
8 Anamuveka chovala cha pachifuwa+ ndi kuika Urimu ndi Tumimu+ m’chovala cha pachifuwacho.
9 Anamuvekanso nduwira+ pamutu pake, n’kuika patsogolo pa nduwirayo kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.
10 Ndiyeno Mose anatenga mafuta odzozera n’kudzoza chihema chopatulika+ ndi zonse zimene zinali mkati mwake, n’kuzipatula.
11 Anawaza ena mwa mafuta odzozerawo maulendo 7 paguwa lansembe+ ndi kudzoza guwa lansembelo, zipangizo zake zonse, beseni ndi choikapo chake, n’kuzipatula.
12 Pomalizira, Mose anathira ena mwa mafuta odzozera pamutu pa Aroni ndi kum’dzoza kuti akhale wopatulika.+
13 Kenako Mose anaitana ana a Aroni+ ndi kuwaveka mikanjo, kuwamanga malamba a pamimba,+ ndi kuwakulunga mipango+ kumutu, monga mmene Yehova analamulira Mose.
14 Atatero anabweretsa ng’ombe yamphongo+ ya nsembe yamachimo, ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu+ pa ng’ombe ya nsembe yamachimoyo.
15 Ndiyeno Mose anapha+ ng’ombeyo, ndipo anatenga magazi+ ake ndi kuwapaka ndi chala chake panyanga zonse za guwa lansembe, n’kuyeretsa guwalo ku uchimo. Koma magazi otsalawo anawathira pansi pa guwa lansembe kuti alipatule, kuphimba machimo+ paguwalo.
16 Ndipo Mose anatenga mafuta onse okuta matumbo, mafuta a pachiwindi ndi impso ziwiri ndi mafuta ake, n’kuzitentha paguwa lansembe.+
17 Koma chikopa cha ng’ombeyo, nyama yake ndi ndowe zake anazitentha kunja kwa msasa,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.
18 Kenako anatenga nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza, ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+
19 Mose anapha nkhosayo ndi kuwaza magazi ake mozungulira paguwa lansembe.+
20 Atatero anaidula ziwaloziwalo,+ ndipo Mose anatenga mutu wake, ziwalozo ndi mafuta ake, ndi kuziika paguwa lansembe.
21 Anatenganso matumbo ndi ziboda n’kuzitsuka ndi madzi. Ndiyeno Mose anatentha nkhosa yonseyo paguwa lansembe.+ Inali nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi.+ Komanso, inali nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose.
22 Atatero anabweretsa nkhosa yamphongo yachiwiri, nkhosa yolongera unsembe,+ ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.
23 Mose anapha nkhosayo ndi kutengako magazi ake n’kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la Aroni, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha kumwendo wa kudzanja lamanja.+
24 Kenako Mose anaitana ana a Aroni ndi kuwapaka magazi m’munsi pakhutu lawo la kudzanja lamanja, pachala chawo chamanthu kudzanja lamanja ndi pachala chawo chachikulu cha kumwendo wa kudzanja lamanja. Koma Mose anawaza magazi otsalawo mozungulira paguwa lansembe.+
25 Pamenepo anatenga mafuta a nkhosayo, mchira wa mafuta, mafuta onse okuta matumbo,+ mafuta a pachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja.+
26 M’dengu la mikate yosafufumitsa limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati,+ mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta,+ ndi kamtanda kamodzi ka mkate kopyapyala.+ Anaziika pamwamba pa mafuta ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja.
27 Atatero anaika zonsezi m’manja mwa Aroni ndi m’manja mwa ana ake n’kuyamba kuziweyula* uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+
28 Ndiyeno Mose anazitenga m’manja mwawo n’kuzitentha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza.+ Zimenezi zinali nsembe yowalongera unsembe,+ yafungo lokhazika mtima pansi.+ Inali nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.+
29 Kenako Mose anatenga nganga+ ndi kuiweyula uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+ Nganga imeneyi anaitenga pa nkhosa yowalongera unsembe ndipo inakhala gawo+ la Mose, monga mmene Yehova analamulira Mose.
30 Atatero Mose anatengako mafuta odzozera+ ndi magazi amene anali paguwa lansembe aja n’kuwawaza pa Aroni ndi pazovala zake. Anawawazanso pa ana ake aja ndi pazovala zawo. Motero anapatula+ Aroni ndi zovala zake komanso ana a Aroni+ ndi zovala zawo.
31 Ndiyeno anauza Aroni ndi ana ake kuti: “Wiritsani+ nyamayo pakhomo la chihema chokumanako, ndipo muidyerenso pomwepo+ pamodzi ndi mkate umene uli m’dengu logwiritsidwa ntchito polonga anthu unsembe, monga mmene anandilamulira, kuti, ‘Aroni ndi ana ake adye zimenezi.’
32 Ndipo nyama ndi mkate zotsala muzitenthe ndi moto.+
33 Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kwa masiku 7,+ kufikira tsiku lomaliza la kulongedwa kwanu unsembe, chifukwa kukupatsani mphamvu* kudzatenga masiku 7.+
34 Yehova walamula kuti mmene zachitikira lero, zichitikenso chimodzimodzi pa masiku otsalawa pokuphimbirani machimo.+
35 Chotero mukhale pakhomo la chihema chokumanako usana ndi usiku kwa masiku 7.+ Ndipo muyenera kuchita ulonda umene Yehova walamula,+ kuti musafe. Chifukwa n’zimene ndalamulidwa.”
36 Choncho Aroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.