Levitiko 9:1-24
9 Tsopano pa tsiku la 8,+ Mose anaitana Aroni, ana ake ndi akulu a Isiraeli.
2 Pamenepo anauza Aroni kuti: “Tenga ng’ombe yaing’ono kuti ikhale nsembe yamachimo,+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Nyama zonsezi zikhale zopanda chilema, ndipo uzipereke kwa Yehova.+
3 Koma uza ana a Isiraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yamphongo+ kuti ikhale nsembe yamachimo. Mutengenso mwana wa ng’ombe ndi nkhosa yaing’ono yamphongo,+ zonsezi zikhale za chaka chimodzi, zopanda chilema, kuti zikhale nsembe yopsereza.
4 Mutengenso ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo kuti muzipereke kwa Yehova monga nsembe zachiyanjano.+ Komanso mubwere ndi nsembe yambewu+ yothira mafuta, chifukwa lero Yehova aonekera ndithu kwa inu.’”+
5 Choncho anthuwo anatenga zimene Mose analamula n’kupita nazo kuchihema chokumanako. Kenako khamu lonse linayandikira ndi kuima pamaso pa Yehova.+
6 Ndiyeno Mose anati: “Mverani zimene Yehova walamula kuti muchite, kuti ulemerero wa Yehova uonekere kwa inu.”+
7 Pamenepo Mose anauza Aroni kuti: “Pita kuguwa lansembe ndi kupereka nsembe yako yamachimo+ ndi nsembe yako yopsereza, kuti uphimbe machimo+ ako ndi a nyumba yako. Kenako uperekere nsembe anthuwa+ ndi kuwaphimbira machimo awo,+ monga mmene Yehova walamulira.”
8 Nthawi yomweyo Aroni anapita kuguwa lansembe ndi kupha ng’ombe yaing’ono kuti ikhale nsembe yake yamachimo.+
9 Ndiyeno ana ake anam’bweretsera magazi+ a ng’ombeyo, ndipo iye anaviika chala chake m’magaziwo+ ndi kuwapaka panyanga za guwa lansembe.+ Magazi otsala anawathira pansi pa guwa lansembelo.
10 Ndipo mafuta,+ impso ndi mafuta a pachiwindi zimene anazitenga panyama ya nsembe yamachimo anazitentha paguwa lansembe,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.
11 Koma nyama ndi chikopa chake anazitentha kunja kwa msasa.+
12 Ndiyeno Aroni anapha nyama ya nsembe yopsereza, ndipo ana ake anam’patsa magazi a nyamayo. Pamenepo iye anawaza magaziwo mozungulira paguwa lansembe.+
13 Kenako anam’patsa ziwalo za nyama ya nsembe yopsereza pamodzi ndi mutu, ndipo anazitentha paguwa lansembe.+
14 Atatero, anatsuka matumbo ndi ziboda, n’kuzitentha paguwa lansembe+ pamwamba pa nsembe yopsereza.
15 Ndiyeno anaperekera nsembe anthu.+ Anatenga mbuzi yoperekera anthu nsembe yamachimo, ndipo anaipha, n’kuipereka monga nsembe yamachimo, mmene anachitira ndi nyama yoyamba ija.
16 Atatero anapereka nsembe yopsereza motsatira ndondomeko yake.+
17 Kenako anapereka nsembe yambewu.+ Anatapako nsembeyo kudzaza dzanja lake ndi kuitentha paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya m’mawa.+
18 Ndiyeno Aroni anapha ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yachiyanjano yoperekera anthuwo.+ Kenako ana ake anam’patsa magazi a nyamazo ndipo iye anawaza magaziwo mozungulira paguwa lansembe.+
19 Kunena za mafuta+ a ng’ombeyo, mchira wa mafuta+ wa nkhosa, mafuta okuta matumbo, impso ndi mafuta a pachiwindi,
20 ana a Aroni anaika zinthu za mafuta zimenezo pamwamba pa nganga+ za nyamazo. Kenako anatentha mafutawo paguwa lansembe.
21 Koma Aroni anaweyula*+ cha uku ndi uku ngangazo ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja pamaso pa Yehova, monga mmene Mose analamulira.
22 Kenako Aroni anakweza manja ake pa anthuwo ndi kuwadalitsa.+ Atatero, anatsika+ kuguwa lansembe kumene anali atapereka nsembe yamachimo, nsembe yopsereza ndi nsembe zachiyanjano.
23 Pamenepo Mose ndi Aroni analowa m’chihema chokumanako, kenako anatulukamo n’kudalitsa anthuwo.+
Atatero, ulemerero wa Yehova+ unaonekera kwa anthu onse,
24 ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ n’kunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi, anayamba kufuula mokondwera+ ndipo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.