Machitidwe 1:1-26

1  A Teofilo,+ m’nkhani yoyamba ija, ndinalemba zonse zimene Yesu anali kuchita ndi kuphunzitsa kuchokera pa chiyambi,+  mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba,+ atapereka malangizo kudzera mwa mzimu woyera kwa atumwi amene iye anawasankha.+  Ndiponso, mwa maumboni ambiri otsimikizika, iye anadzionetsa kwa atumwiwo kuti ali moyo pambuyo pa zovuta zimene anakumana nazo.+ Iwo anamuona masiku onse 40, ndipo anali kuwauza za ufumu wa Mulungu.+  Pamene iye anali pa msonkhano limodzi ndi ophunzirawo, anawapatsa malangizo akuti: “Musatuluke mu Yerusalemu,+ koma muyembekezere chimene Atate analonjeza,+ chimene munamva kwa ine.  Chifukwa Yohane anabatizadi ndi madzi, koma pasanathe masiku ambiri mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.”+  Tsopano atasonkhana pamodzi, anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu+ kwa Isiraeli pa nthawi ino?”  Iye anawayankha kuti: “Si kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo+ zimene Atate waziika pansi pa ulamuliro wake.+  Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.+ Pamenepo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”+  Atatsiriza kunena zimenezi, Mulungu anamunyamula kupita m’mlengalenga iwo akuonerera,+ ndipo mtambo unamuphimba moti sanathenso kumuona.+ 10  Mmene iwo anali kuyang’anitsitsa kuthambo pamene iye anali kukwera kumwamba,+ panaonekera amuna awiri ovala zoyera+ ataimirira pambali pawo. 11  Amunawo anawafunsa kuti: “Amuna inu a ku Galileya, n’chifukwa chiyani muli chilili choncho kuyang’ana kuthambo? Yesu ameneyu, amene watengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati panu, adzabwera m’njira yofanana+ ndi mmene mwamuonera akukwera kuthambo.” 12  Pamenepo anabwerera+ ku Yerusalemu, kuchokera kuphiri lotchedwa phiri la Maolivi. Phiri limeneli lili pafupi ndi Yerusalemu, pa mtunda wa ulendo wa tsiku la sabata.*+ 13  Atafika mumzindawo anakwera m’chipinda cham’mwamba,+ mmene anali kukhala. Mmenemo munali Petulo, Yohane, Yakobo, Andireya, Filipo, Tomasi, Batolomeyo, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Simoni wachangu uja komanso Yudasi mwana wa Yakobo.+ 14  Mogwirizana, onsewa analimbikira kupemphera,+ pamodzi ndi amayi ena+ komanso Mariya mayi a Yesu, limodzinso ndi abale ake a Yesu.+ 15  Tsopano m’masiku amenewa, Petulo anaimirira pakati pa abalewo (gulu lonselo linali la anthu pafupifupi 120) n’kunena kuti: 16  “Amuna inu, abale, kudzera pakamwa pa Davide, mzimu woyera+ unaneneratu lemba lokhudza Yudasi,+ amene anatsogolera anthu okagwira Yesu.+ Kunali kofunikira kuti lembalo likwaniritsidwe+ 17  chifukwa anali mmodzi wa ife,+ ndipo anali kutumikira nafe limodzi.+ 18  (Chotero munthu ameneyu, anagula+ munda ndi malipiro a ntchito zosalungama.+ Anagwa chamutu+ n’kuphulika mimba, moti phokoso la kuphulikako linamveka, ndipo matumbo ake onse anakhuthuka. 19  Izi zinadziwika kwa anthu onse okhala mu Yerusalemu, moti munda umenewo anali kuutchula m’chilankhulo chawo kuti A·kelʹda·ma, kutanthauza kuti Munda wa Magazi.) 20  M’buku la Masalimo analembamo kuti, ‘Malo ake okhala asanduke bwinja, ndipo pasapezeke aliyense wokhalamo,’+ komanso kuti, ‘Udindo wake monga woyang’anira utengedwe ndi munthu wina.’+ 21  Choncho n’kofunikira kuti pamalo pake palowe mmodzi mwa amuna amene akhala akusonkhana nafe nthawi zonse pamene Ambuye Yesu anali kuchita zinthu zosiyanasiyana pakati pathu.+ 22  Wotenga malo amenewa akhale munthu amene wakhala akusonkhana nafe kuyambira pamene Yesu anabatizidwa+ ndi Yohane, kudzafika tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati pathu.+ Mmodzi wa amuna amenewa, akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.”+ 23  Choncho anaimika awiri, Yosefe wotchedwa Barasaba, amene amadziwikanso kuti Yusito, ndi Matiya. 24  Ndipo anapemphera kuti: “Ambuye wathu Yehova, inu amene mumadziwa mitima ya anthu onse,+ tisonyezeni amene inu mwamusankha mwa amuna awiriwa, 25  kuti atenge malo a utumiki uwu ndi utumwi,+ amene Yudasi anawasiya ndi kuyenda njira zake.” 26  Atatero anachita maere+ pa iwo, ndipo maerewo anagwera Matiya. Choncho iye anamuphatikiza pa atumwi 11+ aja.

Mawu a M'munsi

Ulendowu unali wa mtunda wa mamita 890, malinga ndi kufotokoza kwa mabuku achirabi, otengera mfundo za pa Yos 3:4.