Machitidwe 11:1-30

11  Tsopano atumwi ndi abale amene anali mu Yudeya anamva kuti anthu a mitundu ina+ nawonso alandira mawu a Mulungu.  Choncho Petulo atapita ku Yerusalemu, olimbikitsa mdulidwe+ anayamba kutsutsana naye.  Iwo anali kumunena kuti anakalowa m’nyumba ya anthu osadulidwa ndi kudya nawo.  Pamenepo Petulo anayamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene zinachitika, kuti:  “Ndinali kupemphera mumzinda wa Yopa. Ndipo ndinayamba kuona masomphenya. M’masomphenyawo ndinaona chinthu chikutsika. Chinthucho chinali chooneka ngati chinsalu chachikulu chimene achigwira m’makona onse anayi, ndipo anali kuchitsitsa kuchokera kumwamba moti chinafika kwa ine.  Nditayang’anitsitsa m’chinthucho, ndinaonamo nyama za miyendo inayi zapadziko lapansi, zilombo zakutchire, zokwawa komanso mbalame zam’mlengalenga.+  Ndinamvanso mawu akundiuza kuti, ‘Nyamuka Petulo, ipha udye!’+  Koma ine ndinati, ‘Iyayi Ambuye, m’kamwa mwangamu simunalowepo choipitsidwa ndi chonyansa chilichonse chiyambire.’+  Poyankha, mawu ochokera kumwambawo anamveka kachiwiri kuti, ‘Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.’+ 10  Mawu amenewo anamvekanso kachitatu, ndipo zonse zinakwezedwanso kumwamba.+ 11  Nthawi yomweyo, amuna atatu amene anatumidwa kwa ine kuchokera ku Kaisareya anaima panyumba imene tinali kukhala.+ 12  Chotero mzimu+ unandiuza kuti ndipite nawo, ndisakayikire ngakhale pang’ono. Pamenepo abale 6 awa anatsagana nane, ndipo tinakalowa m’nyumba ya munthuyo.+ 13  “Iye anatiuza mmene anaonera mngelo ataimirira m’nyumba yake ndi kunena kuti, ‘Tuma anthu kuti apite ku Yopa akaitane Simoni wotchedwanso Petulo.+ 14  Iye adzalankhula nawe zinthu zimene zidzathandize iwe ndi banja lako lonse kupulumuka.’+ 15  Koma nditangoyamba kulankhula, mzimu woyera unawagwera monga mmene unachitiranso pa ife poyamba paja.+ 16  Zitatero ndinakumbukira mawu a Ambuye aja akuti, ‘Yohane anabatiza ndi madzi,+ koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.’+ 17  Chotero ngati Mulungu anapereka mphatso yaulere imodzimodziyo kwa iwo, monga mmenenso anachitira kwa ife amene tinakhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu,+ ine ndine ndani kuti ndiletse Mulungu?”+ 18  Tsopano pamene iwo anamva zimenezi, anangovomereza,+ ndipo anatamanda Mulungu+ kuti: “Chabwino, pamenepa ndiye kuti Mulungu wapereka mwayi kwa anthu a mitundu ina kuti iwonso alape ndi kudzapeza moyo.”+ 19  Ndiyeno anthu amene anabalalika+ chifukwa cha chisautso chimene chinagwera Sitefano anayenda mpaka ku Foinike,+ ku Kupuro+ ndi ku Antiokeya. Ndipo sanali kulalikira mawu kwa wina aliyense koma kwa Ayuda okha.+ 20  Koma pakati pawo panali amuna ena a ku Kupuro ndi ku Kurene. Amenewa atafika ku Antiokeya anayamba kulankhula ndi anthu olankhula Chigiriki,+ ndipo anali kulengeza kwa iwo uthenga wabwino wa Ambuye Yesu.+ 21  Apanso, dzanja la Yehova+ linali nawo, ndipo ambiri amene anakhulupirira anatembenukira kwa Ambuye.+ 22  Mpingo wa ku Yerusalemu unamva za iwo, ndipo unatumiza Baranaba+ kuti apite ku Antiokeya. 23  Atafika kumeneko ndi kuona kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu, anakondwera+ ndipo anayamba kulimbikitsa onse kuti apitirize kukhala okhulupirika kwa Ambuye motsimikiza mtima.+ 24  Baranaba anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi mzimu woyera komanso wachikhulupiriro. Ndipo khamu lalikulu ndithu linakhulupirira Ambuye.+ 25  Kenako Baranaba anapita ku Tariso+ kukafufuza Saulo+ 26  ndipo atamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Choncho iwo anasonkhana ndi mpingo kumeneko chaka chonse, ndipo anaphunzitsa anthu ambirimbiri. Ku Antiokeya, n’kumene ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.+ 27  M’masiku amenewa aneneri+ anapita ku Antiokeya kuchokera ku Yerusalemu. 28  Mmodzi wa iwo dzina lake Agabo,+ analosera mwa mzimu kuti padziko lonse lapansi kumene kuli anthu,+ padzagwa njala yaikulu. Izi zinachitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo. 29  Chotero aliyense wa ophunzirawo, anatsimikiza mtima kutumiza thandizo+ lililonse limene akanatha+ kwa abale okhala ku Yudeya. 30  Ndipo anachitadi zimenezo mwa kutumiza thandizolo kwa akulu, kudzera mwa Baranaba ndi Saulo.+

Mawu a M'munsi