Machitidwe 13:1-52

13  Tsopano mumpingo wa ku Antiokeya munali aneneri+ ndi aphunzitsi. Iwo anali Baranaba, Sumeoni wotchedwa Nigeri, Lukiyo+ wa ku Kurene, Manayeni amene anaphunzira pamodzi ndi Herode wolamulira chigawo, ndi Saulo.  Pamene anali kutumikira+ Yehova ndi kusala kudya, mzimu woyera unati: “Mwa anthu onse, mundipatulire Baranaba ndi Saulo+ kuti agwire ntchito imene ndinawaitanira.”  Pamenepo anasala kudya ndipo anapemphera, kenako anawaika manja+ ndi kuwalola kuti apite.  Chotero amuna awa, amene mzimu woyera unawatumiza, anapita ku Selukeya, ndipo kuchokera kumeneko ananyamuka ulendo wa pamadzi wopita ku Kupuro.  Atafika kumeneko, mumzinda wa Salami anayamba kufalitsa mawu a Mulungu m’masunagoge a Ayuda. Iwo analinso ndi Yohane+ monga wowatumikira.  Iwo anayenda pachilumba chonsecho mpaka kukafika ku Pafo. Kumeneko anakumana ndi munthu wina wamatsenga. Munthu ameneyu anali Myuda dzina lake Bara-Yesu, ndipo analinso mneneri wonyenga.+  Iyeyu anali limodzi ndi bwanamkubwa Serigio Paulo, munthu wanzeru. Bwanamkubwayu anaitana Baranaba ndi Saulo, chifukwa anali kufunitsitsa kumva mawu a Mulungu.  Koma Elima, wamatsenga, (uku ndiye kumasulira kwa dzina lakeli) anayamba kutsutsana nawo.+ Iye anali kuyesetsa kuti bwanamkubwayo asakhulupirire Ambuye.  Saulo, wotchedwanso Paulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera, anamuyang’anitsitsa 10  n’kunena kuti: “Iwe munthu wodzazidwa ndi mtundu uliwonse wa chinyengo ndi zoipa, mwana wa Mdyerekezi,+ mdani wa chilichonse cholungama, kodi sudzaleka kupotoza njira zowongoka za Yehova? 11  Tsopano tamvera! Dzanja la Yehova lili pa iwe, ndipo ukhala wakhungu. Kwa kanthawi, suthanso kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo nkhungu yamphamvu ndi mdima wandiweyani zinamugwera, ndipo anafufuza uku ndi uku kufuna anthu oti amugwire dzanja ndi kumutsogolera.+ 12  Bwanamkubwa+ uja ataona zimenezo, anakhala wokhulupirira, pakuti anadabwa kwambiri ndi zimene anaphunzira zokhudza Yehova. 13  Tsopano amunawo, pamodzi ndi Paulo, anayamba ulendo wa panyanja kuchoka ku Pafo, ndipo anafika ku Pega, ku Pamfuliya.+ Koma Yohane+ anawasiya ndi kubwerera+ ku Yerusalemu. 14  Iwo anapitiriza ulendo wawo kuchokera ku Pega ndi kukafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa m’sunagoge+ tsiku la sabata ndi kukhala pansi. 15  Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zitawerengedwa pamaso pa anthu,+ atsogoleri+ a sunagoge anawatumizira mawu akuti: “Amuna inu, abale athu, ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.” 16  Choncho Paulo anaimirira, ndipo anakweza dzanja+ lake ndi kunena kuti: “Anthu inu, Aisiraeli, ndi ena nonse oopa Mulungu, tamverani.+ 17  Mulungu wa anthu awa Aisiraeli, anasankha makolo athu akale. Anakweza anthu amenewa pamene anali kukhala m’dziko lachilendo la Iguputo, ndipo anawatulutsa mmenemo ndi dzanja lokwezeka.+ 18  Kwa nthawi ya zaka pafupifupi 40,+ anapirira khalidwe lawo m’chipululu. 19  Ndipo atawononga mitundu 7 m’dziko la Kanani, anagawa dzikolo kwa Aisiraeli mwa kuchita maere.+ 20  Zonsezi zinachitika m’zaka pafupifupi 450. “Zimenezi zitatha anawapatsa oweruza mpaka kudzafika pa mneneri Samueli.+ 21  Koma kuchokera pamenepo anthuwo ananena kuti akufuna mfumu.+ Chotero Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini,+ ndipo anakhala mfumu yawo kwa zaka 40. 22  Atamuchotsa ameneyu,+ anawapatsa Davide monga mfumu yawo.+ Iyeyu Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Jese,+ munthu wapamtima panga.+ Ameneyu adzachita zonse zimene ine ndikufuna.’+ 23  Kuchokera mwa ana+ a munthu ameneyu, malinga ndi lonjezo lake, Mulungu wabweretsa mpulumutsi mu Isiraeli,+ amene ndi Yesu. 24  Mpulumutsi+ ameneyu asanafike, Yohane+ anali atalalikiriratu poyera kwa anthu onse mu Isiraeli za ubatizo, monga chizindikiro cha kulapa. 25  Koma pamene Yohane anali kukwaniritsa utumiki wake, anali kunena kuti, ‘Kodi mukuganiza kuti ine ndine ndani? Amene inu mukumuganizira si ine ayi. Koma wina akubwera pambuyo panga, amene ine sindili woyenera kumumasula nsapato kumapazi kwake.’+ 26  “Amuna inu, abale anga, inu ana a mbadwa za Abulahamu, ndi ena onse oopa Mulungu amene ali pakati panu, mawu a chipulumutso chimenechi atumizidwa kwa ife.+ 27  Pakuti okhala mu Yerusalemu ndi olamulira awo sanamudziwe Iyeyu.+ Koma pochita ngati oweruza, anakwaniritsa zinthu zonenedwa ndi Aneneri,+ zimene zimawerengedwa mokweza Sabata lililonse. 28  Ngakhale kuti sanapeze chifukwa chomuphera,+ anaumiriza Pilato kuti ameneyu anyongedwe basi.+ 29  Ndiyeno iwo atakwaniritsa zinthu zonse zolembedwa zonena za iye,+ anamutsitsa pamtengo+ ndi kumuika m’manda achikumbutso.+ 30  Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa.+ 31  Ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anatsagana naye popita ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amene tsopano ndiwo mboni zake kwa anthu.+ 32  “Chotero ife tikulengeza kwa inu uthenga wabwino wa lonjezo limene linaperekedwa kwa makolo athu.+ 33  Uthengawo ndi wakuti Mulungu wakwaniritsa lonjezo lonselo kwa ife ana awo mwa kuukitsa Yesu.+ Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene zinalembedwa mu salimo lachiwiri kuti, ‘Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala Atate wako.’+ 34  Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa kwa akufa, osayembekezera kubwereranso kuthupi limene lingathe kuvunda, anaitchula motere, ‘Ine ndidzakusonyezani anthu inu kukoma mtima kwanga kosatha ndi kokhulupirika, kumene ndinasonyeza Davide.’+ 35  Ndipo mu salimo lina akunenanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.’+ 36  Koma Davide+ anakwaniritsa chifuniro cha Mulungu mu nthawi ya m’badwo wake, ndipo anagona mu imfa ndi kuikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake, moti thupi lake linavunda.+ 37  Komatu amene Mulungu anamuukitsa uja thupi lake silinavunde.+ 38  “Chotero dziwani abale anga kuti, ife tikulalikira kwa inu za kukhululukidwa kwa machimo kudzera mwa Iyeyu.+ 39  Dziwaninso kuti pa zinthu zonse zimene kunali kosatheka kuti muyesedwe opanda mlandu kudzera m’chilamulo cha Mose,+ aliyense wokhulupirira akuyesedwa wopanda mlandu kudzera mwa Iyeyu.+ 40  Chotero samalani kuti zimene Zolemba za aneneri zikunena zisakugwereni. Zolemba za anenerizo zikuti, 41  ‘Inu onyoza zimene ine ndikuchita, mudzaona zimene ndikuchitazo ndi kudabwa nazo. Kenako mudzazimiririka, chifukwa simudzakhulupirira ngakhale pang’ono zimene ndidzachite m’masiku anu, ngakhale wina atakufotokozerani mwatsatanetsatane.’”+ 42  Tsopano pamene anali kutuluka, anthu anayamba kuwachonderera kuti adzawauzenso nkhani zimenezi sabata lotsatira.+ 43  Choncho msonkhano wa m’sunagoge utatha, Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda ambiri amene anali kupembedza Mulungu anatsatira Paulo ndi Baranaba.+ Ndipo iwo polankhula ndi anthuwo anawalimbikitsa+ kuti apitirize kuyenda m’kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+ 44  Sabata lotsatira, pafupifupi mzinda wonse unasonkhana pamodzi kudzamvera mawu a Yehova.+ 45  Ayuda ataona khamu la anthulo, anachita nsanje+ ndipo anayamba kutsutsa mwamwano zimene Paulo anali kulankhula.+ 46  Chotero Paulo ndi Baranaba analankhula molimba mtima kuti: “Kunali koyenera kuti inu mukhale oyamba kuuzidwa mawu a Mulungu.+ Koma popeza kuti mukuwatayira kumbali+ ndipo mukudziweruza nokha kukhala osayenera moyo wosatha, ifeyo tikutembenukira kwa anthu a mitundu ina.+ 47  Ndipotu Yehova anatiikira lamulo lakuti, ‘Ndakuikani monga kuwala kwa anthu a mitundu ina,+ kuti mukhale chipulumutso mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’”+ 48  Pamene anthu a mitundu inawo anamva zimenezi, anakondwera ndi kutamanda mawu a Yehova.+ Ndipo onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.+ 49  Komanso, mawu a Yehova anapitirira kufalitsidwa m’dziko lonselo.+ 50  Koma Ayuda+ anauza zoipa amayi otchuka amene anali opembedza Mulungu, komanso amuna olemekezeka a mumzindawo. Chotero iwowa anachititsa kuti Paulo ndi Baranaba ayambe kuzunzidwa,+ ndipo anawaponya kunja kwa mzinda wawo. 51  Koma Paulo ndi Baranaba anasansira anthuwo fumbi kumapazi awo+ n’kupita ku Ikoniyo. 52  Ndipo ophunzirawo anapitiriza kudzazidwa ndi chimwemwe+ ndi mzimu woyera.

Mawu a M'munsi