Machitidwe 23:1-35
23 Pamene anali kuyang’anitsitsa Khoti Lalikulu la Ayudalo, Paulo anati: “Amuna inu, abale anga, ndachita zinthu popanda chikumbumtima changa kunditsutsa ngakhale pang’ono pamaso pa Mulungu+ mpaka lero.”
2 Atamva zimenezi Hananiya mkulu wa ansembe, analamula anthu amene anaimirira pafupi naye kuti amubwanyule+ pakamwa.
3 Pamenepo Paulo anamuuza kuti: “Uona, Mulungu akukantha, khoma* lopaka laimu+ iwe. Wakhala pamenepo kuti undiweruze motsatira Chilamulo,+ kodi ukuphwanyanso wekha Chilamulocho+ polamula kuti andimenye?”
4 Anthu amene anaima pafupi naye anati: “Kodi ukulalatira mkulu wa ansembe wa Mulungu?”
5 Pamenepo Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Pakuti Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+
6 Tsopano Paulo ataona kuti ena mwa iwo anali Asaduki+ ndipo ena anali Afarisi, anafuula m’khotimo kuti: “Amuna inu, abale anga, ine ndine Mfarisi,+ mwana wa Afarisi. Pano ndikuweruzidwa+ chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka+ kwa akufa.”
7 Atanena zimenezi, panabuka mkangano+ pakati pa Afarisi ndi Asaduki, ndipo khamulo linagawanika.
8 Pakuti Asaduki+ amanena kuti akufa sadzauka,+ kulibe angelo, kapena cholengedwa chauzimu, koma Afarisi amavomereza poyera kuti zonsezi zilipo.
9 Choncho panabuka phokoso lalikulu,+ ndipo alembi ena a gulu la Afarisi anaimirira ndi kuyamba kutsutsa mwaukali kuti: “Sitikupeza cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu.+ Koma ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye,+ . . .”
10 Mkanganowo utakula kwambiri, mkulu wa asilikali anachita mantha kuti anthuwo amukhadzulakhadzula Paulo. Chotero analamula asilikali+ kuti apite komweko kuti akamuchotse pakati pawo ndi kumubweretsa kumpanda wa asilikali.+
11 Koma tsiku lomwelo usiku, Ambuye anaimirira pambali pake+ ndi kunena kuti: “Limba mtima!+ Pakuti wandichitira umboni mokwanira+ mu Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.”+
12 Kutacha, Ayuda anakonza chiwembu+ ndi kulumbira mwa kudzitemberera+ kuti sadya kapena kumwa kanthu kufikira atapha Paulo.+
13 Analipo amuna oposa 40 amene anakonza chiwembu chochita kulumbirirachi.
14 Chotero anapita kwa ansembe aakulu+ ndi kwa akulu kukanena kuti: “Ife tachita lumbiro ndi kudzitemberera kuti sitilawa chakudya kufikira titapha Paulo.
15 Tsopano, inuyo pamodzi ndi Khoti Lalikulu la Ayuda, mufotokoze momveka bwino kwa mkulu wa asilikali. Mumuuze kuti amubweretse kwa inu, ngati kuti mukufuna kumvetsetsa bwino nkhani yokhudza munthu ameneyu.+ Koma asanafike n’komwe ife tidzakhala okonzeka kumupha.”+
16 Koma mwana wamwamuna wa mlongo wake wa Paulo anamva kuti anthuwo akonza zokamudikirira panjira,+ ndipo anapita ndi kukalowa kumpanda wa asilikali kukanena zimenezi kwa Paulo.
17 Choncho Paulo anaitana mmodzi mwa akapitawo a asilikali ndi kunena kuti: “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali, pakuti ali ndi mawu oti amuuze.”
18 Choncho mwamunayo anamutengadi ndi kupita naye kwa mkulu wa asilikali, ndipo anamuuza kuti: “Mkaidi uja Paulo, anandiitana ndi kundipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu, akuti ali ndi mawu oti akuuzeni.”
19 Mkulu wa asilikali uja anamugwira+ dzanja mnyamatayo ndi kupita naye pambali. Kumeneko anayamba kumufunsa kuti: “N’chiyani chimene ukufuna kundiuza?”
20 Iye anati: “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mupititse Paulo kubwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda mawa, ngati kuti iwo akufuna kumvetsa bwino za iye.+
21 Koma chonde musalole kuti akunyengerereni, pakuti amuna oposa 40 akumudikirira panjira.+ Amenewa achita kulumbira modzitemberera kuti sadya kapena kumwa kanthu kufikira atamupha.+ Moti panopa akonzeka, akungoyembekezera chilolezo chanu.”
22 Pamenepo mkulu wa asilikaliyo anauza mnyamatayo kuti azipita atamulangiza kuti: “Usauze aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”
23 Ndiyeno anaitanitsa akapitawo awiri a asilikali ndi kuwauza kuti: “Uzani asilikali 200 kuti akonzekere kuyenda mpaka kukalowa mu Kaisareya cha m’ma 9 koloko* usiku uno. Pakhalenso amuna 70 okwera mahatchi* ndi asilikali 200 a mikondo.
24 Muwapatsenso nyama zonyamula katundu kuti akwezepo Paulo ndi kukamufikitsa kwa bwanamkubwa Felike ali wotetezeka.”
25 Ndiyeno iye analemba kalata yotere:
26 “Ine Kalaudiyo Lusiya, ndikulembera inu wolemekezeka, Bwanamkubwa Felike:+ Landirani moni!
27 Munthu uyu anagwidwa ndi Ayuda ndipo anali pafupi kumupha. Koma ine ndinafika mwadzidzidzi ndi gulu la asilikali n’kumulanditsa,+ chifukwa ndinamva kuti iyeyu ndi Mroma.+
28 Choncho ine pofuna kudziwa chimene anapalamula, ndinapita naye kubwalo la Khoti lawo Lalikulu.+
29 Kumeneko ndinapeza kuti akumuimba mlandu pa nkhani zokhudza Chilamulo chawo.+ Koma sanapezeke ndi mlandu uliwonse woyenera chilango cha imfa kapena kuponyedwa m’ndende.+
30 Komabe popeza andiululira za chiwembu+ chimene amukonzera munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga, ndipo ndalamula omuimba mlanduwo kuti adzamuneneze mlanduwo pamaso panu.”+
31 Pamenepo asilikali+ amenewa anatenga Paulo usiku, monga anawalamulira ndi kupita naye ku Antipatiri.
32 M’mawa wake analola amuna okwera mahatchi aja kuti apitirire naye, ndipo iwo anabwerera kumpanda wa asilikali.
33 Amuna okwera mahatchiwo analowa mu Kaisareya+ ndi kupereka kalata ija kwa bwanamkubwa ndipo anaperekanso Paulo.
34 Choncho iye anaiwerenga ndi kufunsa chigawo chimene anali kuchokera, ndipo anapeza kuti+ ndi wochokera ku Kilikiya.+
35 Pamenepo anati: “Ndimvetsera mlandu wako wonse, okuimba mlanduwo akafika.”+ Ndipo analamula kuti amusunge m’nyumba ya mfumu Herode ndi kumuyang’anira.
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
^ Mawu ake enieni, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko madzulo.
^ Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”