Machitidwe 24:1-27

24  Patapita masiku asanu, kunafika mkulu wa ansembe Hananiya+ pamodzi ndi akulu ena, komanso munthu wina wodziwa kulankhula, dzina lake Teritulo. Iwo ananeneza+ Paulo kwa bwanamkubwa.+  Teritulo atapatsidwa mwayi kuti alankhulepo, anayamba kuneneza Paulo. Iye anati: “Tili pa mtendere wochuluka+ chifukwa cha inu, komanso zinthu zikusintha mu mtundu wathuwu chifukwa cha nzeru zanu zoona patali.  Choncho nthawi zonse komanso kulikonse, Inu Wolemekezeka+ a Felike, ife timayamikira kwambiri kulandira nzeru zanuzo.  Koma kuti ndisakutayitseni nthawi, ndikupempha chonde kuti mumve mawu athu pang’ono, mwa kukoma mtima kwanu.  Ife tapeza kuti munthu uyu ndi wovutitsa kwabasi,+ ndipo akuyambitsa zoukira boma+ pakati pa Ayuda onse padziko lapansi kumene kuli anthu. Ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lampatuko wa Anazareti.+  Iyeyu anayesanso kudetsa kachisi,+ ndipo tinamugwira. 7 * ——  Mutamufunsa, mungathe kutsimikizira nokha zonse zimene tikumunenezazi.”  Atanena zimenezi Ayuda nawonso analowerera kumuukira. Iwo anali kunena motsindika kuti zimenezo n’zoonadi. 10  Pamene bwanamkubwayo anagwedezera Paulo mutu kuti alankhule, Paulo anayankha kuti: “Ine podziwa bwino kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu kwa zaka zambiri, ndine wokondwa kuti ndilankhule podziteteza+ pa zimene akundinenezazi. 11  Inu mukhoza kupeza umboni wakuti sipanapite masiku 12 kuchokera pamene ine ndinapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu.+ 12  Ndipo iwowa sanandipezepo m’kachisi+ ndikutsutsana ndi wina aliyense, ngakhale kuyambitsa chipolowe+ m’masunagoge kapena pena paliponse mumzindawu. 13  Ngakhalenso panopa sangathe kukupatsani umboni+ wa zimene akundinenezazi. 14  Komatu ndikuvomereza izi kwa inu: Njira yolambirira imene iwo akuitcha ‘gulu lampatuko,’ ndi njira imene ine ndikuchitira utumiki wopatulika kwa Mulungu wa makolo anga.+ Pakuti ndimakhulupirira zonse zimene zili m’Chilamulo+ ndi Zolemba za aneneri. 15  Ndipo ine ndili ndi chiyembekezo+ mwa Mulungu, chimenenso anthu awa ali nacho, kuti kudzakhala kuuka+ kwa olungama+ ndi osalungama omwe.+ 16  Pambali imeneyi, ndikuyesetsa mwakhama, kuchita mozindikira+ kuti ndisapalamule kwa Mulungu kapena kwa anthu. 17  Choncho pambuyo pa zaka zambiri, ndinabwera kudzapatsa mtundu wanga mphatso zachifundo, ndiponso kudzapereka nsembe.+ 18  Pamene ndinali kuchita zimenezi, anandipeza m’kachisi nditadziyeretsa monga mwa mwambo,+ koma panalibe khamu la anthu kapena wochita phokoso. Kumeneko kunali Ayuda ena ochokera m’chigawo cha Asia. 19  Amenewo ndiwo anali oyenera kupezeka pano pamaso panu kudzandineneza ine akanakhala ndi chifukwa chondiimbira mlandu.+ 20  Kapena, muwalole anthu ali panowa, afotokoze okha ngati anandipeza ndi cholakwa chilichonse pamene ndinaimirira pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. 21  Mawu amodzi okha amene ine ndinafuula, pamene ndinaimirira pakati pawo ndi akuti, ‘Ine lero ndikuweruzidwa pamaso panu chifukwa cha nkhani ya kuuka kwa akufa!’”+ 22  Komabe Felike,+ ankadziwa bwino kwambiri nkhani yokhudza Njira imeneyi,+ choncho anaimitsa mlanduwo ndi kunena kuti: “Ndidzagamula mlandu wanuwu akadzafika Lusiya+ mkulu wa asilikali.” 23  Choncho analamula kapitawo wa asilikali kuti amuyang’anire munthuyu ndi kumupatsako ufulu, ndi kuti asaletse munthu aliyense mwa anthu a mtundu wake kumutumikira.+ 24  Patapita masiku angapo, Felike+ anafika pamodzi ndi mkazi wake Durusila, amene anali mayi wachiyuda.+ Choncho Felike anaitanitsa Paulo ndi kumumvetsera pamene anali kufotokoza za kukhulupirira Khristu Yesu.+ 25  Koma pamene anali kulankhula za chilungamo,+ za kudziletsa,+ ndi za chiweruzo+ chimene chikudzacho, Felike anachita mantha ndipo anayankha kuti: “Basi, padakali pano ungapite, ndikadzapeza nthawi ndidzakuitananso.” 26  Pa nthawi imodzimodziyo, anali kuyembekezera kuti Paulo amupatse ndalama.+ Pa chifukwa chimenechi anali kumuitanitsa kawirikawiri n’kumakambirana naye.+ 27  Koma zaka ziwiri zitatha, Felike anachoka ndipo Porikiyo Fesito ndi amene analowa m’malo mwake. Koma popeza kuti Felike ankafuna kuti Ayuda azimukonda,+ anangomusiya m’ndende Paulo.

Mawu a M'munsi

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.