Malaki 2:1-17
2 “Tsopano lamulo ili ndi la inu ansembe.+
2 Mukapanda kumvera,+ ndiponso ngati simuganizira nkhani imeneyi mumtima mwanu+ kuti mulemekeze dzina langa,+ ndidzakutumizirani temberero+ ndi kutemberera madalitso anu.+ Ndatemberera dalitso la aliyense wa inu chifukwa simunaganizire nkhani imeneyi mumtima mwanu,” watero Yehova wa makamu.
3 “Tamverani! Ndiwononga mbewu chifukwa cha inu+ ndipo ndikuwazani ndowe kumaso. Ndikuwazani ndowe za nyama zimene mumapereka nsembe pa zikondwerero zanu. Munthu wina adzakunyamulani ndi kukakutayani pandowezo.
4 Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndakutumizirani lamulo limeneli+ kuti pangano+ limene ndinapangana ndi Levi lipitirire,”+ watero Yehova wa makamu.
5 “Pangano limene ndinapangana naye linasunga moyo wake. Linamuthandizanso kukhala ndi moyo wamtendere.+ Chifukwa cha madalitso amenewa, anali kundiopa.+ Popeza kuti anali kulemekeza dzina langa, sankachita chilichonse chondikwiyitsa.+
6 Lamulo la choonadi linali m’kamwa mwake+ ndipo pamilomo pake panalibe zosalungama. Anali kuyenda ndi ine mwamtendere komanso mowongoka mtima,+ ndipo anabweza anthu ambiri panjira zawo zolakwika.+
7 Wansembe ayenera kuphunzitsa anthu kuti adziwe Mulungu. Anthuwo ayenera kufunafuna kumva chilamulo kuchokera pakamwa pake,+ pakuti iye ndi mthenga wa Yehova wa makamu.+
8 “Koma inu mwapatuka panjira yoyenera.+ Mwalepheretsa anthu ambiri kutsatira chilamulo.+ Mwaphwanya pangano limene ndinapangana ndi Levi,”+ watero Yehova wa makamu.
9 “Inenso ndidzachititsa kuti inu mukhale anthu onyozeka ndi otsika kwa anthu onse,+ chifukwa simunayende m’njira zanga, koma munali kukondera pa nkhani zokhudza chilamulo.”+
10 “Kodi tonsefe atate wathu si mmodzi?+ Kodi si Mulungu mmodzi amene anatilenga?+ N’chifukwa chiyani tikuchitirana zachinyengo,+ mwa kuipitsa pangano la makolo athu akale?+
11 Yuda wachita zachinyengo, ndipo mu Isiraeli ndi mu Yerusalemu mwachitika zinthu zonyansa.+ Pakuti Yuda wadetsa chiyero cha Yehova+ chimene Mulungu amachikonda, ndipo Yuda wakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.+
12 Yehova adzapha ndi kuchotsa munthu aliyense wochita zonyansazi+ m’mahema a Yakobo. Iye adzapha ndi kuchotsamo aliyense, kaya akhale ndani.* Komanso adzapha aliyense amene akupereka nsembe ngati mphatso+ kwa Yehova wa makamu.”
13 “Pali chinthu china chimene anthu inu mukuchita ndipo chikuchititsa kuti guwa lansembe la Yehova lidzaze ndi misozi, kulira ndi kubuula. Chifukwa cha zimenezi, nsembe zanu zimene mumapereka ngati mphatso n’zosavomerezeka kwa iye ndipo sakusangalala ndi chilichonse chochokera m’manja mwanu.+
14 Inu mwanena kuti, ‘Chifukwa chiyani?’+ Chifukwa chakuti Yehova wakudzudzulani popeza kuti aliyense wa inu wachitira zachinyengo mkazi amene anamukwatira ali mnyamata,+ ngakhale kuti iye anali mnzake komanso mkazi wa pangano lake.+
15 Komabe pakati panu pali ena amene atsimikiza mtima kuti asachite zoterezi. Iwo akufuna kukhala ndi ana amene angakhaledi anthu a Mulungu.*+ Mphamvu ya Mulungu ikutsogolera anthu amenewa pa zonse zimene akuchita. Tsopano inunso ganizirani mofatsa ndipo mukhale ndi maganizo oyenera.+ Tsimikizani mtima kuti musachitire zachinyengo akazi anu amene munawakwatira muli anyamata.+
16 Pakuti ine ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja,”+ watero Yehova Mulungu wa Isiraeli. “Ndimadana ndi munthu amene zochita zake zankhanza zili ngati chovala chauve chimene wavala.+ Musamale ndi maganizo a mumtima mwanu ndipo musamachite zachinyengo,”+ watero Yehova wa makamu.
17 “Anthu inu mwatopetsa Yehova ndi mawu anu,+ ndipo mwanena kuti, ‘Tamutopetsa motani?’ Mwa kunena kuti, ‘Aliyense wochita zoipa ndi wabwino kwa Yehova, ndipo iye amakondwera ndi anthu otero.’+ Kapena mwa kunena kuti, ‘Kodi Mulungu wachilungamo ali kuti?’”+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “amene ali maso ndiponso amene akuyankha.”
^ Mawu ake enieni, “mbewu ya Mulungu.”