Maliko 16:1-20
16 Choncho tsiku la sabata+ litapita, Mariya Mmagadala,+ Mariya mayi wa Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhira kuti akapake thupi la Yesu.+
2 M’mawa kwambiri tsiku loyamba+ la mlunguwo, iwo anafika kumanda achikumbutsowo, dzuwa litatuluka.+
3 Iwo anali kufunsana kuti: “Nanga ndani amene akatigubuduzire chimwala chija pakhomo la manda achikumbutso?”
4 Koma atayang’anitsitsa, anaona kuti mwalawo wagubuduzidwa kale ngakhale kuti unali waukulu kwambiri.+
5 Atalowa m’manda achikumbutsowo, anaona mnyamata atakhala pansi kudzanja lamanja, atavala mkanjo woyera, ndipo iwo anadabwa kwambiri.+
6 Iye anawauza kuti: “Musadabwe choncho. Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu Mnazareti, amene anapachikidwa.+ Iyetu wauka kwa akufa,+ salinso muno ayi. Taonani! Si apa pamene anamugoneka!+
7 Inuyo pitani, mukauze ophunzira ake komanso Petulo kuti, ‘Watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona, monga anakuuzirani.’”+
8 Tsopano iwo atatuluka, m’manda achikumbutsowo anayamba kuthawa, pakuti anali kunjenjemera ndi kunthunthumira kwambiri. Ndipo sanaulule kanthu kwa aliyense, chifukwa anagwidwa ndi mantha.+
MAWU OMALIZA AAFUPI
Mipukutu ndi Mabaibulo ena amene analembedwa pambuyo pake ali ndi mawu omaliza aafupi awa pambuyo pa Maliko 16:8:
Koma zinthu zonse zimene analamula, iwo anazifotokoza mwachidule kwa amene anali pafupi ndi Petulo. Komanso izi zitatha, Yesu mwiniyo anatumiza uthenga woyera ndi wosawonongeka wa chipulumutso chosatha kudzera mwa ophunzira, kuchokera kum’mawa mpaka kumadzulo.
MAWU OMALIZA AATALI
Mipukutu ina yakale (Codex Alexandrinus, Codex Ephraemi, Codex Bezae) ndi Mabaibulo ena (Latin Vulgate, Curetonian Syriac, Syriac Peshitta) anawonjezera mawu omaliza aatali otsatirawa, koma mawuwa anawachotsamo m’mipukutu yotchedwa Codex Sinaiticus, Codex Vaticanus, the Sinaitic Syriac codex, komanso mu Armenian Version:
9 Atauka m’mawa tsiku loyamba la mlungu, anaonekera choyamba kwa Mariya Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7.
10 Mayiyu anapita ndi kukauza amene anali kukhala ndi Yesu, pakuti anali achisoni ndipo anali kulira.
11 Koma iwo, pamene anamva kuti ali moyo ndi kuti iye wamuona, sanakhulupirire.
12 Komanso, izi zitachitika anaonekera mwamtundu wina kwa awiri a iwo pamene anali kuyenda nawo limodzi popita kumidzi.
13 Pamenepo iwo anabwerera ndi kukauza enawo. Ndipo nawonso sanakhulupirire zimenezo.
14 Koma pambuyo pake anaonekera kwa ophunzira 11 aja pamene anali kudya chakudya patebulo. Pamenepo iye anawadzudzula chifukwa chosowa chikhulupiriro ndi kuuma mitima kwawo, pakuti iwo sanakhulupirire anthu amene anamuona atauka kwa akufa.
15 Iye anawauza kuti: “Pitani m’dziko lonse ndi kukalalikira uthenga wabwino ku cholengedwa chilichonse.
16 Amene adzakhulupirira ndi kubatizidwa adzapulumuka, koma amene sadzakhulupirira adzaweruzidwa.
17 Komanso, okhulupirira adzachita zizindikiro izi: M’dzina langa adzatulutsa ziwanda, ndi kulankhula m’malilime.
18 Adzanyamula njoka ndi manja awo, ndipo akadzamwa chilichonse chakupha sichidzawavulaza ngakhale pang’ono. Adzaika manja awo pa anthu odwala, ndipo adzachira.”
19 Choncho Ambuye Yesu atatsiriza kulankhula nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndi kukakhala kudzanja lamanja la Mulungu.
20 Pamenepo iwo anachoka ndi kupita kukalalikira kwina kulikonse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito limodzi ndi kutsimikizira uthengawo mwa zizindikiro zimene anali kuchita.