Maliko 3:1-35

3  Kachiwirinso Yesu analowa m’sunagoge. Mmenemo munali munthu wa dzanja lopuwala.+  Choncho Afarisi anali kumuyang’anitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa sabata, n’cholinga chakuti amuimbe mlandu.+  Ndipo iye anauza munthu wa dzanja lopuwalayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.”  Kenako anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiti pa sabata? Chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ Koma iwo anangokhala chete.  Pamenepo Yesu anawayang’ana mokwiya ndi kumva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima kwawo.+ Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhala labwinobwino.+  Ataona zimenezi Afarisiwo anatuluka ndipo nthawi yomweyo anapita kukakonza chiwembu limodzi ndi a chipani cha Herode+ kuti amuphe.+  Koma Yesu ndi ophunzira ake anachoka ndi kupita kunyanja. Chikhamu cha anthu ochokera ku Galileya ndi ku Yudeya chinam’tsatira.+  Ngakhalenso anthu ambiri ochokera ku Yerusalemu, ku Idumeya, kutsidya la Yorodano, ndi m’madera a Turo+ ndi Sidoni, anamva zonse zimene iye anali kuchita, ndipo anakhamukira kwa iye.  Ndipo iye anauza ophunzira ake kuti am’bweretsere ngalawa yaing’ono yoti akweremo kuti khamu la anthulo lisam’panikize. 10  Popeza kuti anali atachiritsa anthu ambiri, onse amene anali ndi matenda aakulu anali kudziponya kwa iye kuti angomukhudza.+ 11  Ngakhalenso mizimu yonyansa,+ imati ikamuona, inali kudzigwetsa pansi pamaso pake ndi kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”+ 12  Koma iye anali kuilamula mwamphamvu nthawi ndi nthawi kuti isamuulule.+ 13  Kenako anakwera m’phiri ndi kuitana amene anali kuwafuna,+ ndipo iwo anapita kwa iye.+ 14  Ndiyeno anasankha gulu la anthu 12, amenenso anawatcha “atumwi,” kuti azikhala naye nthawi zonse ndi kuti aziwatuma kukalalikira+ 15  ndi kuwapatsa mphamvu zotulutsa ziwanda.+ 16  Choncho m’gulu la anthu 12 amene anasankha aja munali Simoni, amene anamutchanso Petulo,+ 17  Yakobo mwana wa Zebedayo, Yohane m’bale wa Yakobo+ (awiriwa anawatchanso a Boanege, kutanthauza Ana a Bingu), 18  Andireya, Filipo, Batolomeyo, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19  ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anadzam’pereka.+ Kenako Yesu analowa m’nyumba. 20  Kumeneko khamu la anthu linasonkhananso, mwakuti sanathe n’komwe kudya chakudya.+ 21  Koma achibale+ ake atamva zimenezo, anapita kukamugwira, chifukwa anali kunena kuti: “Wachita misala.”+ 22  Komanso alembi amene anachokera ku Yerusalemu anali kunena kuti: “Ali ndi Belezebule,* ndipo amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 23  Choncho anawaitana, ndipo anayamba kuwapatsa mafanizo akuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24  Ngati ufumu wagawanika, ufumu umenewo sungakhale.+ 25  Ngati nyumba yagawanika, nyumba yoteroyo singakhale.+ 26  Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana wadziukira yekha ndipo wagawanika, sangakhale, koma akupita kokatha.+ 27  Kunena zoona, palibe amene angalowe m’nyumba ya munthu wamphamvu ndi kulanda+ katundu wake ngati sangamange munthu wamphamvuyo choyamba. Atam’manga, m’pamene angathe kutenga katundu m’nyumbamo.+ 28  Ndithu ndikukuuzani, ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya ndi machimo otani amene anachita kapena mawu onyoza otani amene analankhula.+ 29  Komabe, aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya, koma adzakhala ndi mlandu wa tchimo losatha.”+ 30  Ananena zimenezi chifukwa iwo anali kumunena kuti: “Ali ndi mzimu wonyansa.”+ 31  Tsopano panafika mayi ake ndi abale ake,+ ndipo anaimirira kunja, ndi kutumiza mthenga kukamuitana.+ 32  Iye anali ndi khamu la anthu litakhala momuzungulira, ndipo anthuwo anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.”+ 33  Koma iye anawayankha kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndani?”+ 34  Kenako anayang’ana onse amene anakhala pansi momuzungulira aja, ndi kunena kuti: “Onani! Mayi anga ndi abale anga ndi awa.+ 35  Aliyense wochita chifuniro cha Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.”+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Kananiya” likutanthauza munthu wachangu.
Limeneli ndi dzina lina la Satana.