Salimo 102:1-28
Pemphero la munthu wosautsika pamene walefuka ndipo akutula nkhawa zake kwa Yehova.+
102 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo.+
2 Musandibisire nkhope yanu pa tsiku limene ndili m’masautso aakulu.+Tcherani khutu lanu kwa ine.+Fulumirani kundiyankha pa tsiku limene ndikuitana.+
3 Pakuti masiku a moyo wanga atha ndi kuzimiririka ngati utsi,+Ndipo mafupa anga atentha kwambiri ngati ng’anjo.+
4 Mtima wanga wawauka ngati udzu ndipo wauma,+Pakuti ndilibe chilakolako chofuna kudya chakudya.+
5 Chifukwa cha kuusa moyo kwanga,+Thupi langa langotsala mafupa okhaokha.+
6 Ndafanana ndi vuwo wam’chipululu.+Ndakhala ngati nkhwezule yakubwinja.
7 Ndafika pofooka,Ndipo ndakhala ngati mbalame imene ili yokhayokha padenga.*+
8 Tsiku lonse adani anga amanditonza.+Anthu ondinyoza amagwiritsa ntchito dzina langa potemberera ena.+
9 Pakuti ndadya phulusa ngati chakudya.+Ndipo zakumwa zanga ndazisakaniza ndi misozi,+
10 Chifukwa cha kudzudzula kwanu kwamphamvu ndi mkwiyo wanu.+Inu mwandikweza m’mwamba kuti munditaye.+
11 Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka dzuwa likalowa,+Ndipo ndauma ngati udzu.+
12 Koma inu Yehova, mudzakhalapobe kwamuyaya,+Dzina lanu* lidzakhalapobe ku mibadwomibadwo.+
13 Inu mudzanyamuka ndi kusonyeza Ziyoni chifundo,+Pakuti imeneyi ndi nyengo yomukomera mtima,Chifukwa nthawi yoikidwiratu yakwana.+
14 Atumiki anu akondwera ndi miyala ya mpanda wake,+Ndipo amakomera mtima fumbi lake.+
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina lanu, inu Yehova,+Ndipo mafumu onse a padziko lapansi adzaopa ulemerero wanu.+
16 Yehova adzamangadi Ziyoni.+Iye ayenera kuonekera mu ulemerero wake.+
17 Iye adzamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse,+Ndipo sadzapeputsa pemphero lawo.+
18 Zimenezi zalembedwera m’badwo wam’tsogolo.+Ndipo anthu amene adzakhalapo m’tsogolo* adzatamanda Ya.+
19 Iye wayang’ana pansi ali kumalo oyera, okwezeka,+Yehova wayang’ana dziko lapansi ali kumwambako,+
20 Kuti amve kuusa moyo kwa akaidi,+Ndi kumasula anthu opita kukaphedwa.+
21 Wachita izi kuti dzina la Yehova lilengezedwe m’Ziyoni,+Ndi kuti atamandidwe mu Yerusalemu,+
22 Pamene mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa pamodzi,+Komanso maufumu, kuti atumikire Yehova.+
23 Moyo wanga utafika pachimake, anachepetsa mphamvu zanga,+Anafupikitsa masiku a moyo wanga.+
24 Ine ndinati: “Inu Mulungu wanga,Musadule pakati masiku a moyo wanga.+Mudzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
25 Munaika kalekale maziko a dziko lapansi,+Ndipo kumwamba ndiko ntchito ya manja anu.+
26 Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe.+Ndipo zonsezi zidzatha ngati chovala.+Mofanana ndi zovala zimene zatha, mudzapezerapo zina ndipo nazonso zidzatha.+
27 Koma inu simudzasintha, ndipo mudzakhalapo kwamuyaya.+
28 Ana a atumiki anu adzapitiriza kukhala motetezeka pamaso panu.+Ndipo ana awo adzakhazikika pamaso panu.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “patsindwi.”
^ Mawu ake enieni, “chikumbutso chanu.”
^ Mawu ake enieni, “anthu amene adzalengedwe.”