Salimo 104:1-35
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+Inu Yehova Mulungu wanga, mwasonyeza kuti ndinu wamkulu koposa.+Mwadziveka ulemu ndi ulemerero.+
2 Mwadzifunditsa kuwala ngati chofunda,+Mwatambasula kumwamba ngati nsalu ya chihema.+
3 Inu munamanga zipinda za m’mwamba pamadzi pogwiritsa ntchito mitanda,+Munapanga mitambo kukhala galeta lanu,+Mumayenda pamapiko a mphepo.+
4 Inu mumapanga angelo anu kukhala mizimu,+Ndipo atumiki anu kukhala moto wonyeketsa.+
5 Mwakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba.+Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.+
6 Munalikuta ndi madzi ngati mwalikuta ndi nsalu.+Madziwo anakwera kupitirira mapiri.+
7 Chifukwa cha kudzudzula kwanu, madziwo anayamba kuthawa.+Atamva mabingu anu anayamba kuthamanga mopanikizika kwambiri,
8 Kupita kumalo amene munawakonzera.Mapiri anakwera,+Zigwa zinatsika.
9 Munawaikira malire kuti asapitirire malirewo,+Kuti asamizenso dziko lapansi.+
10 Mwatsegula akasupe m’zigwa,+Ndipo madziwo akudutsa pakati pa mapiri.
11 Akasupewo amapereka madzi kwa zilombo zonse zakutchire.+Nthawi zonse mbidzi+ zimapha ludzu lawo mmenemo.
12 Zolengedwa zouluka m’mlengalenga zimamanga zisa zawo pafupi ndi akasupewo,+Ndipo zimalira m’mitengo ya masamba ambiri obiriwira.+
13 Mulungu amathirira mapiri kuchokera m’zipinda zake za m’mwamba.+Dziko lapansi ladzaza ndi zipatso za ntchito yake.+
14 Amameretsa msipu kuti nyama zidye,+Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke m’nthaka,+
15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+
16 Mitengo ya Yehova imathiriridwa bwino,Mikungudza ya ku Lebanoni imene iye anabzala.+
17 Mbalame zimamanga zisa zawo mmenemo.+Dokowe nyumba yake ndiyo mitengo ya mlombwa.+
18 M’mapiri aatali+ ndi mmene mumakhala mbuzi zakumapiri.+Ndipo m’mapanga ndiye mothawiramo mbira.+
19 Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.+Dzuwa nalo limadziwa bwino kumene limalowera.+
20 Munapanga mdima kuti kukhale usiku.+Nyama zonse zakutchire zimayendayenda usikuwo.
21 Mkango wamphamvu umabangula pofunafuna nyama,+Ndiponso popempha chakudya kwa Mulungu.+
22 Dzuwa likayamba kuwala+ zimachoka,Ndipo zimakagona m’malo awo obisalamo.
23 Munthu amapita ku ntchito zake,+Ndipo amagwira ntchito mpaka madzulo.+
24 Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu.+Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.+
25 M’nyanja yakuya iyi ndiponso yotambalala,+Muli zinthu zoyenda zosawerengeka,+Muli zamoyo zazikulu ndi zazing’ono zomwe.+
26 Zombo zimayenda mmenemo.+Ndipo Leviyatani*+ munam’panga kuti azisewera mmenemo.+
27 Zonsezi zimayembekezera inu+Kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.+
28 Zimalandira zimene mwazipatsa.+Mumatambasula dzanja lanu ndipo zimakhutira ndi zinthu zabwino.+
29 Mukaphimba nkhope yanu, zimasokonezeka.+Mukachotsa mzimu wawo, zimafa,+Ndipo zimabwerera kufumbi.+
30 Mukatumiza mzimu wanu zimalengedwa.+Ndipo mumachititsa dziko kukhala latsopano.
31 Ulemerero wa Yehova udzakhalapobe mpaka kalekale.+Yehova adzakondwera ndi ntchito zake.+
32 Amayang’ana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.+Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+
33 Ndidzaimbira Yehova moyo wanga wonse.+Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.+
34 Kulingalira za iye kukhale kosangalatsa.+Ine ndidzakondwera mwa Yehova.+
35 Ochimwa adzafafanizidwa padziko lapansi.+Ndipo anthu oipa sadzakhalaponso.+Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Tamandani Ya, anthu inu!*+