Salimo 115:1-18
115 Ife sitikuyenerera kalikonse, inu Yehova, ife sitikuyenerera kalikonse,+Koma dzina lanu ndi loyenera kulemekezedwa+Malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha, malinganso ndi choonadi chanu.+
2 Musalole kuti mitundu izinena kuti:+“Mulungu wawo ali kuti tsopano?”+
3 Koma Mulungu wathu ali kumwamba.+Chilichonse chimene anafuna kuchita anachita.+
4 Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+
5 Pakamwa ali napo koma salankhula,+Maso ali nawo koma saona.+
6 Makutu ali nawo koma satha kumva.+Mphuno ali nayo koma sanunkhiza.+
7 Manja ali nawo, koma sakhudza kanthu.+Mapazi ali nawo koma sayenda.+Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+
8 Amene amawapanga adzafanana nawo.+Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+
9 Iwe Isiraeli, khulupirira Yehova.+Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.+
10 Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova.+Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+
11 Inu oopa Yehova, khulupirirani Yehova.+Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+
12 Yehova watikumbukira, ndipo adzapereka madalitso,+Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli,+Adzadalitsa nyumba ya Aroni.+
13 Yehova adzadalitsa anthu omuopa,+Adzadalitsa onsewo osasiyapo aliyense.+
14 Yehova adzakuchulukitsani,+Inu ndi ana anu.+
15 Inu ndinu amene mwadalitsidwa ndi Yehova,+Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+
16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+
17 Akufa satamanda Ya,+Ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.+
18 Koma ife tidzatamanda Ya+Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+Tamandani Ya, anthu inu!+