Salimo 12:1-8
Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe chapansipansi.*+ Nyimbo ya Davide.
12 Ndipulumutseni,+ inu Yehova, pakuti anthu okhulupirika atha.+Anthu okhulupirika atheratu pakati pa ana a anthu.
2 Iwo amalankhulana zabodza.+Amalankhulana ndi milomo yoshashalika+ komanso ndi mitima iwiri.+
3 Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengoNdi lilime lolankhula modzikuza.+
4 Iye adzadula anthu onena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana.+Timalankhula chilichonse chimene tikufuna ndi milomo yathu. Ndani angatilamulire?”
5 Tsopano Yehova wanena kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+Ndidzanyamuka pa nthawiyo,+Ndidzawateteza kwa aliyense wowanyodola.”+
6 Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino,+Ngati siliva woyengedwa nthawi zokwanira 7 mung’anjo ya m’nthaka.
7 Inu Yehova mudzawayang’anira.+Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku m’badwo uwu mpaka kalekale.
8 Anthu oipa akuyendayenda ponseponse,Chifukwa ana a anthu amayamikira zoipa.+